Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Salimo la Davide.
28 Kwa Inu ine ndiyitana, Yehova ndinu Thanthwe langa;
musakhale osamva kwa ine.
Pakuti mukapitirira kukhala chete,
ndidzakhala ngati iwo amene atsikira ku dzenje.
2 Imvani kupempha chifundo kwanga
pomwe ndikuyitana kwa Inu kuti mundithandize,
pomwe ndikukweza manja anga
kuloza ku malo anu oyeretsetsa.
3 Musandikokere kutali pamodzi ndi anthu oyipa,
pamodzi ndi iwo amene amachita zoyipa,
amene amayankhula mwachikondi ndi anzawo
koma akusunga chiwembu mʼmitima mwawo.
4 Muwabwezere chifukwa cha zochita zawo
ndi ntchito zawo zoyipa;
abwezereni chifuwa cha zimene manja awo achita
ndipo mubweretse pa iwo zimene zowayenera.
5 Popeza iwowo sakhudzidwa ndi ntchito za Yehova,
ndi zimene manja ake anazichita,
Iye adzawakhadzula
ndipo sadzawathandizanso.
6 Matamando apite kwa Yehova,
popeza Iye wamva kupempha chifundo kwanga.
7 Yehova ndiye mphamvu yanga ndi chishango changa;
mtima wanga umadalira Iye, ndipo Ine ndathandizidwa.
Mtima wanga umalumphalumpha chifukwa cha chimwemwe
ndipo ndidzayamika Iye mʼnyimbo.
8 Yehova ndi mphamvu ya anthu ake,
linga la chipulumutso kwa wodzozedwa wake.
9 Pulumutsani anthu anu ndipo mudalitse cholowa chanu;
mukhale mʼbusa wawo ndipo muwakweze kwamuyaya.
Munthu Wochimwa Adzafa
18 Yehova anandiyankhula nati: 2 “Kodi anthu inu mumatanthauza chiyani mukamabwerezabwereza kunena mwambi uwu wokhudza dziko la Israeli kuti:
“ ‘Nkhuyu zodya akulu zimapota
ndi ana omwe?’ ”
3 “Ndithu pali Ine wamoyo, akutero Ambuye Yehova, simudzanenanso mwambi umenewu mu Israeli. 4 Pakuti moyo uliwonse ndi wanga. Moyo wa abambo ndi wanga, wamwananso ndi wanga. Munthu wochimwa ndi amene adzafe.
5 “Tiyerekeze kuti pali munthu wolungama
amene amachita zolungama ndi zolondola.
6 Iye sadyera nawo pa mapiri a chipembedzo
kapena kupembedza mafano a Aisraeli.
Iye sayipitsa mkazi wa mnzake
kapena kugonana ndi mkazi pamene akusamba.
7 Iye sapondereza munthu wina aliyense,
koma amabwezera wangongole nʼchigwiriro chake.
Iye salanda zinthu za osauka,
koma amapereka chakudya kwa anthu anjala,
ndipo amapereka zovala kwa anthu ausiwa.
8 Iye sakongoletsa ndalama mwa katapira,
kapena kulandira chiwongoladzanja chachikulu.
Amadziletsa kuchita zoyipa
ndipo sakondera poweruza milandu.
9 Iye amatsatira malangizo anga,
ndipo amasunga malamulo anga mokhulupirika.
Munthu ameneyo ndi wolungama;
iye adzakhala ndithu ndi moyo,
akutero Ambuye Yehova.
10 “Tiyerekeze kuti munthu wolungama chotere wabala mwana chimbalangondo amene amakhalira kupha anthu ndi kuchita zinthu zina zotere. 11 Iye nʼkumachita zinthu zimene ngakhale abambo ake sanachitepo.
“Amadyera nawo ku mapiri achipembedzo.
Amayipitsa mkazi wa mnzake.
12 Iye amapondereza munthu wosauka ndi wosowa.
Amalanda zinthu za osauka.
Sabweza chikole cha munthu wa ngongole.
Iye amatembenukira ku mafano
nachita zonyansa.
13 Iye amakongoletsa mwa katapira ndipo amalandira chiwongoladzanja chachikulu.
Kodi munthu wotereyu nʼkukhala ndi moyo? Ayi ndithu! Chifukwa wachita zinthu zonyansa zonsezi, adzaphedwa ndipo adzalandira chilango chomuyenera.
14 “Tsono tiyerekeze kuti munthu woyipa uyu wabala mwana amene amaona machimo onse amene abambo ake ankachita. Ngakhale amaona koma osatsanzira ntchito zake zoyipazo.
15 “Sadyera nawo pa mapiri achipembedzo.
Sapembedza mafano a ku Israeli.
Sayipitsa mkazi wa mnzake.
16 Sapondereza munthu wina aliyense.
Satenga chikole akabwereketsa chinthu. Salanda zinthu za osauka.
Salanda zinthu za munthu.
Amapereka chakudya kwa anthu anjala.
Amapereka zovala kwa anthu aumphawi.
17 Amadziletsa kuchita zoyipa.
Sakongoletsa kuti apezepo phindu. Salandira chiwongoladzanja.
Amasunga malangizo anga ndi kumvera malamulo anga.
Munthu wotereyo sadzafa chifukwa cha machimo a abambo ake. Adzakhala ndi moyo ndithu. 18 Koma abambo ake, popeza kuti anazunza anthu ena ndi kubera mʼbale wawo ndiponso popeza kuti sanachitire zabwino anansi ake, adzafera machimo ake omwe.
19 “Mwina inu mukhoza kufunsa kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani mwana salangidwa chifukwa cha kulakwa kwa abambo ake? Ayi, mwanayo adzakhala ndi moyo chifukwa ankachita zolungama ndi zolondola ndipo ankasamala kumvera malamulo anga onse. 20 Munthu wochimwa ndiye amene adzafe. Mwana sadzapezeka wolakwa chifukwa cha abambo ake, kapena abambo kupezeka wolakwa chifukwa cha mwana wawo. Chilungamo cha munthu wolungama ndicho chidzamupulutse, ndipo kuyipa kwa munthu wochimwa ndiko kudzamuwonongetse.
21 “ ‘Munthu woyipa akatembenuka mtima ndi kusiya machimo amene ankachita ndi kuyamba kumvera malamulo anga ndi kumachita zolungama ndi zokhulupirika, ndiye kuti adzakhala ndi moyo. Sadzafa ayi. 22 Zoyipa zake zonse zidzakhululukidwa. Chifukwa cha zinthu zolungama zimene anazichita adzakhala ndi moyo. 23 Kodi Ine ndimakondwera ndi imfa ya munthu woyipa? Ayi, ndimakondwera pamene woyipa watembenuka mtima kuti akhale ndi moyo. Akutero Ambuye Yehova.
24 “ ‘Koma ngati munthu wolungama apatuka kusiya zachilungamo ndi kuyamba kuchita tchimo ndi zonyansa za mtundu uliwonse zimene amachita anthu oyipa, kodi munthu wotereyu nʼkukhala ndi moyo? Ayi ndithu, zolungama zake zonse sizidzakumbukiridwa. Iye adzayenera kufa chifukwa cha machimo amene anachita.
25 “Komabe inu mukunena kuti, ‘Zimene Ambuye amachita ndi zopanda chilungamo.’ Tamvani tsono inu Aisraeli: Kodi zochita zanga ndizo zosalungama? Kodi si zochita zanu zimene ndi zosalungama? 26 Ngati munthu wolungama atembenuka kusiya chilungamo chake ndi kuchita tchimo, iye adzafa chifukwa cha tchimolo. 27 Koma ngati munthu woyipa aleka zoyipa zake zimene anazichita ndi kuyamba kuchita zimene ndi zolungama ndi zolondola, iye adzapulumutsa moyo wake. 28 Popeza waganizira za zolakwa zonse ankachita ndipo wazileka, iye adzakhala ndi moyo ndithu; sadzafa. 29 Komabe Aisraeli akunena kuti, ‘Zimene Ambuye amachita ndi zopanda chilungamo.’ Kodi zochita zanga ndizo zopanda chilungamo, inu Aisraeli? Kodi si zochita zanu zimene ndi zopanda chilungamo?
30 “Chifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti: inu Aisraeli, Ine ndidzakuweruzani aliyense wa inu molingana ndi ntchito zake. Lapani! Lekani zoyipa zanu kuti musawonongeke nazo. 31 Tayani zolakwa zanu zonse zimene munandichimwira nazo ndipo khalani ndi mtima watsopano ndi mzimu watsopano. Kodi muferanji inu Aisraeli? 32 Ine sindikondwera ndi imfa ya munthu aliyense, akutero Ambuye Yehova. Chifukwa chake, lapani kuti mukhale ndi moyo.”
Eneya ndi Tabita
32 Pamene Petro amayendera mpingo, anapita kukachezera oyera mtima a ku Luda. 33 Kumeneko anakapeza munthu dzina lake Eneya, wofa ziwalo amene anagona pa mphasa kwa zaka zisanu ndi zitatu. 34 Petro anati kwa iye, “Eneya, Yesu Khristu akukuchiritsa iwe, dzuka ndipo yalula mphasa yako.” Nthawi yomweyo Eneya anayimirira. 35 Anthu onse amene anakhala ku Luda ndi ku Sharoni anamuona ndipo anatembenukira kwa Ambuye.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.