Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
104 Tamanda Yehova, iwe moyo wanga.
Inu Yehova Mulungu wanga, ndinu wamkulu kwambiri;
mwavala ulemerero ndi ufumu.
2 Iye wadzifunditsa kuwala ngati chovala;
watambasula miyamba ngati tenti
3 ndipo wayika pa madzi mitanda ya chipinda chake.
Iye amasandutsa mitambo kukhala galeta lake,
ndi kuwuluka pa mapiko a mphepo.
4 Amapanga mphepo kukhala amithenga ake,
malawi amoto kukhala atumiki ake.
5 Anakhazikitsa dziko lapansi pa maziko ake;
silingasunthike.
6 Munaliphimba ndi nyanja yozama ngati chovala;
madzi anayimirira pamwamba pa mapiri.
7 Koma pakudzudzula kwanu madzi anathawa,
pa mkokomo wa bingu lanu iwo anamwazika;
8 Inu munamiza mapiri,
iwo anatsikira ku zigwa
kumalo kumene munawakonzera.
9 Inu munayika malire ndipo sangathe kudutsa,
iwo sadzamizanso dziko lapansi.
24 Ntchito zanu ndi zochulukadi Inu Yehova!
Munazipanga zonse mwanzeru,
dziko lapansi ladzaza ndi zolengedwa zanu.
35 Koma anthu ochimwa awonongeke pa dziko lapansi
ndipo anthu oyipa asapezekenso.
Tamanda Yehova, Iwe moyo wanga.
Tamandani Yehova.
39 “Kodi iwe umadziwa nthawi imene mbalale yayikazi imaswera?
Kodi umaonerera pamene nswala ikubala?
2 Kodi umawerenga miyezi imene zimakhala ndi bere?
Kodi nthawi imene zimaswana iwe umayidziwa?
3 Zimakhala tsonga ndi kuswa ana awo;
pamenepo ululu wobereka nʼkutha.
4 Ana a nyamazi amakhala ndi mphamvu ndipo amakulira mʼthengo;
kenaka amachoka ndipo sabwereranso.
5 “Kodi bulu wakuthengo amamupatsa ndani ufulu wongodziyendera?
Ndani amamasula zingwe zake?
6 Ine ndinamupatsa chipululu kuti chikhale mudzi wake,
nthaka ya mchere kuti ikhale malo ake okhalamo
7 Iye amakhala kutali ndi phokoso la mu mzinda;
ndipo samva kufuwula kwa oyendetsa nyama zakatundu.
8 Amayendayenda mʼmapiri kudya msipu
ndipo amafunafuna msipu uliwonse wobiriwira.
9 “Kodi njati ingavomere kukutumikira?
Kodi ingagone mu gome lako usiku?
10 Kodi ungathe kuyimanga ndi zingwe kuti izilima?
Kodi ingasalaze nthumbira mʼmunda mwako?
11 Kodi ungadalire njatiyo chifukwa champhamvu zake?
Kodi ungayilekere kuti igwire ntchito zako zolemetsa?
12 Kodi ungadalire kuti idzakubweretsera tirigu wako
ndi kumuyika ku malo opunthira?
13 “Nthiwatiwa imakupiza mapiko ake monyadira,
koma mapikowo sangafanane ndi mapiko ndi nthenga za kakowa.
14 Nthiwatiwa imakwirira mazira ake pansi
ndipo amafundidwa ndi nthaka,
15 nthiwatiwayo sidera nkhawa kuti mazira ake angathe kuswanyidwa,
ndi kuti nyama zakuthengo zitha kuwaponda.
16 Nthiwatiwa imachitira nkhanza ana ake ngati anawo si ake;
Imayiwala zoti inavutika powabala.
17 Chifukwa Mulungu anayimana nzeru,
simvetsa kanthu kalikonse.
18 Komatu nthiwatiwa ikadzambatuka ndi kuyamba kuthamanga,
imamusiya kutali kavalo ndi wokwerapo wake.
19 “Kodi ndiwe amene umamupatsa mphamvu kavalo
kapena kumuveka chenjerere mʼkhosi mwake?
20 Kodi ndiwe amene umalipatsa dzombe ulemerero wolumphira,
ukali wake nʼkumachititsa mantha?
21 Iye amalumphalumpha moopseza, kukondwerera mphamvu zake,
ndipo amapita ku nkhondo ndi mphamvu zake zonse.
22 Iye sachita mantha, saopa chilichonse;
sabwerera mʼmbuyo akaona lupanga.
23 Zida zankhondo zimachita kwichikwichi mʼchimake pambali pake
pamodzi ndi mkondo wonyezimira ndi nthungo.
24 Kavaloyo amanjenjemera ndi ukali ndi kulumphalumpha;
satha kungoyima pamene wamva kulira kwa lipenga.
25 Lipenga likalira amati, ‘Twee!’
Amamva fungo la nkhondo ali patali,
kufuwula kwa anthu olamulira nkhondo ndi mfuwu wankhondo.
26 “Kodi kabawi amawuluka ndi nzeru zako,
ndi kutambasula mapiko ake kupita kummwera?
27 Kodi umalamulira chiwombankhanga ndiwe kuti chiziwuluka
ndi kumanga chisa chake pamwamba penipeni?
28 Chimakhala pa phiri ndipo chimakhala pamenepo usiku;
chimakhala pa msonga penipeni pa mwala.
29 Chili pamenepo chimayangʼanayangʼana choti chigwire kuti chidye;
maso ake amachionera patali chinthucho.
30 Ana ake amayamwa magazi,
ndipo kumene kuli mitembo ndiko chimapezeka.”
Mkangano Pakati pa Ophunzira
24 Komanso mkangano unabuka pakati pawo kuti ndani mwa iwo amene amaganiziridwa kukhala wamkulu. 25 Yesu anawawuza kuti, “Mafumu a anthu a mitundu ina amaonetsa mphamvu za ufumu wawo pa anthuwo; ndipo amene ali ndi ulamuliro, amapatsidwa dzina la kuti ‘Opindula.’ 26 Koma inu simuyenera kukhala choncho. Mʼmalo mwake, wamkulu pakati panu akhale ngati wamngʼono pa onse, ndipo iye amene alamulira akhale ngati wotumikira. 27 Pakuti wamkulu ndani, iye amene ali pa tebulo kapena iye amene akutumikira? Kodi si iye amene ali pa tebulo? Koma ndili pakati panu ngati mmodzi wokutumikirani. 28 Inu ndinu amene mwayima nane mʼmayesero. 29 Ndipo Ine ndikupatsani inu ufumu, monga momwe Atate anga anandipatsiranso Ine, 30 kuti inu muthe kudya ndi kumwa pa tebulo langa mu ufumu wanga ndi kukhala pa mipando yaufumu kuweruza mafuko khumi ndi awiri a Israeli.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.