Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
104 Tamanda Yehova, iwe moyo wanga.
Inu Yehova Mulungu wanga, ndinu wamkulu kwambiri;
mwavala ulemerero ndi ufumu.
2 Iye wadzifunditsa kuwala ngati chovala;
watambasula miyamba ngati tenti
3 ndipo wayika pa madzi mitanda ya chipinda chake.
Iye amasandutsa mitambo kukhala galeta lake,
ndi kuwuluka pa mapiko a mphepo.
4 Amapanga mphepo kukhala amithenga ake,
malawi amoto kukhala atumiki ake.
5 Anakhazikitsa dziko lapansi pa maziko ake;
silingasunthike.
6 Munaliphimba ndi nyanja yozama ngati chovala;
madzi anayimirira pamwamba pa mapiri.
7 Koma pakudzudzula kwanu madzi anathawa,
pa mkokomo wa bingu lanu iwo anamwazika;
8 Inu munamiza mapiri,
iwo anatsikira ku zigwa
kumalo kumene munawakonzera.
9 Inu munayika malire ndipo sangathe kudutsa,
iwo sadzamizanso dziko lapansi.
24 Ntchito zanu ndi zochulukadi Inu Yehova!
Munazipanga zonse mwanzeru,
dziko lapansi ladzaza ndi zolengedwa zanu.
35 Koma anthu ochimwa awonongeke pa dziko lapansi
ndipo anthu oyipa asapezekenso.
Tamanda Yehova, Iwe moyo wanga.
Tamandani Yehova.
37 “Mtima wanga ukulumphalumpha pa chimenechinso
ndipo ukuchoka mʼmalo mwake.
2 Tamverani! Tamverani kubangula kwa liwu lake,
kugunda kumene kukuchokera mʼkamwa mwake.
3 Iye amaponya chingʼaningʼani chake pansi pa thambo lonse
ndipo amachitumiza ku dziko lapansi.
4 Pambuyo pake kubangula kwake kumamveka.
Iye amabangula ndi liwu lake laulemerero.
Pamene wabangula,
palibe chimene amalephera kuchita.
5 Liwu la Mulungu limabangula mʼnjira zambiri zodabwitsa
Iye amachita zinthu zazikulu zimene sitingathe kuzimvetsa.
6 Amalamula chisanu chowundana kuti, ‘Igwa pa dziko lapansi,’
ndipo amalamulanso mvula yamawawa kuti, ‘Khala mvula yamphamvu.’
7 Kuti anthu onse amene anawalenga athe kuzindikira ntchito yake.
Iye amalepheretsa anthu kugwira ntchito zawo.
8 Zirombo zimakabisala
ndipo zimakhala mʼmaenje mwawo.
9 Mphepo yamkuntho imatuluka ku malo ake,
kuzizira kumatuluka mʼmphepo yamkunthoyo.
10 Mpweya wa Mulungu umawunditsa madzi
ndipo madzi a mʼnyanja amawuma kuti gwaa.
11 Iye amadzaza mitambo ndi madzi a mvula,
amabalalitsa zingʼaningʼani zake kuchokera mʼmitambomo.
12 Mulungu amayendetsa mitamboyo
mozungulirazungulira dziko lonse lapansi
kuti ichite zonse zimene Iye akufuna pa dziko lapansi.
13 Iye amagwetsa mvula kuti alange anthu,
kapena kubweretsa chinyontho pa dziko lapansi kuti aonetse chikondi chake.
14 “Abambo Yobu, tamvani izi;
imani ndipo muganizire ntchito zodabwitsa za Mulungu.
15 Kodi mukudziwa momwe Mulungu amayendetsera mitambo
ndi kuchititsa kuti kukhale zingʼaningʼani?
16 Kodi mukudziwa momwe Mulungu amayalira mitambo,
ntchito zodabwitsa za Iye amene ndi wanzeru zangwiro?
17 Inu amene mʼzovala zanu mumatuluka thukuta
pamene kunja kwatentha chifukwa cha mphepo yakummwera,
18 kodi mungathe kuthandizana naye kutambasula thambo
limene ndi lolimba ngati chitsulo?
19 “Tiwuzeni ife zoti tikanene kwa Iye;
sitingathe kufotokoza mlandu wathu chifukwa cha mdima umene uli mwa ife.
20 Kodi nʼkofunika kumudziwitsa Mulungu kuti ndili naye mawu?
Kodi kutero sikuchita ngati kupempha kuti ndiwonongeke?
21 Tsopano munthu sangathe kuyangʼana dzuwa,
ndi kunyezimira mlengalenga,
kuwomba kwa mphepo kutachotsa mitambo yonse.
22 Kuwala kwake kumaonekera cha kumpoto;
Mulungu amabwera ndi ulemerero woopsa.
23 Wamphamvuzonse sitingathe kumufikira pafupi ndi wa mphamvu zoposa;
pa chiweruzo chake cholungama ndi mʼchilungamo chake chachikulu Iye sapondereza anthu ozunzika.
24 Nʼchifukwa chake anthu amamuopa kwambiri,
kodi saganizira za onse amene amaganiza kuti ndi anzeru?”
Mkazi Wachiwerewere
17 Mmodzi wa angelo asanu ndi awiri aja amene anali ndi mbale zisanu ndi ziwiri anadza nati kwa ine, “Bwera ndikuonetse chilango cha mkazi wadama wotchuka uja amene akukhala pambali pa madzi ambiri. 2 Mafumu a dziko lapansi amachita naye chigololo ndipo okhala pa dziko lapansi analedzera ndi vinyo wa zigololo zake.”
3 Kenaka mngeloyo anandinyamula mwa Mzimu Woyera kupita nane ku chipululu. Kumeneko ndinaona mkazi atakhala pa chirombo chofiira chokutidwa ndi mayina a chipongwe ndipo chinali ndi mitu isanu ndi iwiri ndi nyanga khumi. 4 Mkaziyo anavala zovala za pepo ndi zofiira nadzikongoletsa ndi golide, miyala yapamwamba ndi ngale. Ananyamula chikho chagolide mʼdzanja lake, chodzaza ndi zinthu zonyansa ndi fungo loyipa la zigololo zake. 5 Pa mphumi pake panalembedwa dzina lodabwitsa:
BABULONI WAMKULU
MAYI WA AKAZI ADAMA
NDI WAZOYIPITSA ZA DZIKO LAPANSI.
6 Ndinaona kuti mkaziyo anali ataledzera ndi magazi a oyera mtima, magazi a amene anachitira umboni Yesu.
Nditamuona mkaziyo ndinadabwa kwambiri. 7 Kenaka mngelo uja anati kwa ine, “Bwanji ukudabwa? Ndikufotokozera chinsinsi cha mkaziyu ndi chinsinsi cha chirombo chimene wakwerapochi chokhala ndi mitu isanu ndi iwiri ndi nyanga khumi. 8 Chirombo chimene wachionachi chinalipo kale koma tsopano kulibe ndipo chidzatuluka ku chidzenje chakuya ndi kupita kukawonongedwa. Anthu okhala pa dziko lapansi amene mayina awo sanalembedwe mʼbuku lamoyo kuyambira pa kulengedwa kwa dziko lapansi adzadabwa pamene adzaona chirombocho, chifukwa chinalipo kale, tsopano kulibe, komabe chidzabwera.
9 “Zimenezi zikufunika kuganizira mwanzeru. Mitu isanu ndi iwiriyo ndi mapiri asanu ndi awiri pomwe mkazi uja amakhalirapo. Yomweyonso ndi mafumu asanu ndi awiri. 10 Mafumu asanu anagwa, imodzi ilipo ndipo ina sinabwere; koma pamene idzafika, idzayenera kukhala kwa kanthawi kochepa. 11 Chirombo chomwe chinalipo kale ndipo tsopano kulibe ndiyo mfumu yachisanu ndi chitatu. Iyo ndi ya mʼgulu la asanu ndi awiriwo ndipo ikupita kukawonongedwa.
12 “Nyanga khumi unaziona zija ndi mafumu khumi amene sanapatsidwe ulamuliro, koma adzapatsidwa ulamuliro pamodzi ndi chirombo kwa ora limodzi. 13 Mafumuwo ali ndi cholinga chimodzi ndipo adzapereka mphamvu ndi ulamuliro wawo kwa chirombocho. 14 Iwo adzachita nkhondo ndi Mwana Wankhosa, koma Mwana Wankhosayo adzawagonjetsa chifukwa Iye ndi Mbuye wa ambuye ndi Mfumu ya mafumu, ndipo amene adzakhala ndi Iye ndi oyitanidwa ake, osankhidwa ndi otsatira ake okhulupirika.”
15 Kenaka mngeloyo anati kwa ine, “Madzi amene unawaona pamene mkazi wadamayo anakhalapo ndiwo anthu ochuluka, mitundu ndi ziyankhulo. 16 Nyanga khumi ndi chirombo unazionazo zidzadya mkazi wadamayo. Zidzamufwifwitsa ndi kumusiya wamaliseche; zidzadya nyama yake ndi kumutentha ndi moto. 17 Pakuti Mulungu wayika ichi mʼmitima mwawo kuti akwaniritse cholinga chake povomerezana kupereka mphamvu zawo zolamulira kwa chirombo, kufikira Mawu a Mulungu atakwaniritsidwa. 18 Mkazi unamuonayo ndi mzinda waukulu umene ulamulira mafumu a dziko lapansi.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.