Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
104 Tamanda Yehova, iwe moyo wanga.
Inu Yehova Mulungu wanga, ndinu wamkulu kwambiri;
mwavala ulemerero ndi ufumu.
2 Iye wadzifunditsa kuwala ngati chovala;
watambasula miyamba ngati tenti
3 ndipo wayika pa madzi mitanda ya chipinda chake.
Iye amasandutsa mitambo kukhala galeta lake,
ndi kuwuluka pa mapiko a mphepo.
4 Amapanga mphepo kukhala amithenga ake,
malawi amoto kukhala atumiki ake.
5 Anakhazikitsa dziko lapansi pa maziko ake;
silingasunthike.
6 Munaliphimba ndi nyanja yozama ngati chovala;
madzi anayimirira pamwamba pa mapiri.
7 Koma pakudzudzula kwanu madzi anathawa,
pa mkokomo wa bingu lanu iwo anamwazika;
8 Inu munamiza mapiri,
iwo anatsikira ku zigwa
kumalo kumene munawakonzera.
9 Inu munayika malire ndipo sangathe kudutsa,
iwo sadzamizanso dziko lapansi.
24 Ntchito zanu ndi zochulukadi Inu Yehova!
Munazipanga zonse mwanzeru,
dziko lapansi ladzaza ndi zolengedwa zanu.
35 Koma anthu ochimwa awonongeke pa dziko lapansi
ndipo anthu oyipa asapezekenso.
Tamanda Yehova, Iwe moyo wanga.
Tamandani Yehova.
36 Ndipo Elihu anapitirira kuyankhula nati:
2 “Mundilole pangʼono pokha ndipo ndikuonetsani
kuti zilipo zambiri zoti ziyankhulidwe mʼmalo mwa Mulungu.
3 Nzeru zanga ndimazitenga kutali;
ndidzaonetsa kulungama kwa Mlengi wanga.
4 Ndithudi mawu anga si abodza;
wanzeru zangwiro ali ndi inu.
5 “Mulungu ndi wamphamvu, koma sanyoza anthu;
Iye ndi wamphamvu, ndipo ndi wokhazikika pa cholinga chake.
6 Salola oyipa kuti akhalebe ndi moyo
koma amapereka ufulu kwa anthu osautsidwa.
7 Iye saleka kuyangʼanira anthu olungama;
amawayika kuti alamulire pamodzi ndi mafumu
ndipo amawalemekeza mpaka muyaya.
8 Koma ngati anthu amangidwa ndi unyolo,
ndipo akondwa ndi zingwe zamasautso,
9 Iye amawafotokozera zomwe anachita,
kuti iwo anachimwa modzikuza.
10 Mulungu amawatsekula makutu kuti amve malangizo ake
ndipo amawalamula kuti alape zoyipa zawo.
11 Ngati iwo amumvera ndi kumutumikira,
adzatsiriza masiku a moyo wawo mwamtendere,
adzatsiriza zaka zawo mosangalala.
12 Koma ngati samvera,
adzaphedwa ndi lupanga
ndipo adzafa osadziwa kanthu.
13 “Anthu osapembedza amasunga mkwiyo mu mtima mwawo;
akawalanga, safuwulira kwa Iye kupempha thandizo.
14 Amafa akanali achinyamata,
pakati pa amuna achiwerewere a kumalo azipembedzo.
15 Koma ovutika, Iye amawapulumutsa pa mavuto awo;
Mulungu amawayankhula mʼmasautso awowo.
16 “Iye akukukopani inu kuti muchoke mʼmasautso,
kuti mupite ku malo aakulu kumene kulibe chokutchingani,
kumalo a mpumulo kumene kuli chakudya chabwino kwambiri.
7 Tsopano landiranani wina ndi mnzake, monganso Khristu anakulandirani inu, ndi cholinga choti Mulungu alemekezeke. 8 Chifukwa kunena zoona, Khristu wasanduka mtumiki wa Ayuda, kuonetsa kuti Mulungu ndi wokhulupirika pa malonjezo amene anachita kwa makolo awo 9 kuti a mitundu ina atamande Mulungu chifukwa cha chifundo chake. Monga kwalembedwa kuti,
“Choncho ine ndidzakutamandani pakati pa a mitundu;
ndidzayimba nyimbo zotamanda dzina lanu.”
10 Akutinso,
“Kondwerani inu anthu a mitundu ina pamodzi ndi anthu ake.”
11 Ndipo akutinso,
“Tamandani Ambuye, inu nonse a mitundu ina,
ndi kuyimba zotamanda Iye, inu anthu onse.”
12 Ndiponso Yesaya akuti,
“Muzu wa Yese udzaphuka,
wina amene adzauka kulamulira anthu a mitundu ina;
mwa Iye mudzakhala chiyembekezo cha a mitundu ina.”
13 Mulungu amene amatipatsa chiyembekezo adzaze mitima yanu ndi chimwemwe ndi mtendere pamene mukumudalira Iye, kuti chiyembekezo chanu chisefukire mwamphamvu ya Mzimu Woyera.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.