Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Monga mwa “Mbawala yayikazi ya Mmawa.” Salimo la Davide.
22 Mulungu wanga, Mulungu wanga, nʼchifukwa chiyani mwandisiya?
Chifuwa chiyani simukundithandiza ndi pangʼono pomwe?
Nʼchifukwa chiyani simukumva mawu a kudandaula kwanga?
2 Inu Mulungu wanga, ine ndimalira masana, koma simuyankha,
usikunso, ndipo sindikhala chete.
3 Inu ndinu Woyera, wokhala pa mpando waufumu;
ndinu matamando a Israeli.
4 Pa inu makolo athu anadalira;
iwo anadalira ndipo Inu munawapulumutsa.
5 Analirira kwa inu ndipo munawapulumutsa.
Iwo anakhulupirira Inu ndipo simunawakhumudwitse.
6 Koma ine ndine nyongolotsi osati munthu,
wosekedwa ndi wonyozedwa ndi anthu onse.
7 Onse amene amandiona amandiseka;
amandiyankhulira mawu achipongwe akupukusa mitu yawo kunena kuti
8 “Iyeyu amadalira Yehova,
musiyeni Yehovayo amulanditse.
Musiyeni Yehova amupulumutse
popeza amakondwera mwa Yehovayo.”
9 Komabe Inu ndinu amene munandibadwitsa, munanditulutsa mʼmimba mwa amayi anga.
Munachititsa kuti ndizikudalirani
ngakhale pa nthawi imene ndinkayamwa.
10 Chibadwire ine ndinaperekedwa kwa Inu;
kuchokera mʼmimba mwa amayi anga Inu mwakhala muli Mulungu wanga.
11 Musakhale kutali ndi ine,
pakuti mavuto ali pafupi
ndipo palibe wina wondipulumutsa.
12 Ngʼombe zazimuna zandizungulira;
ngʼombe zazimuna zamphamvu za ku Basani zandizinga.
13 Mikango yobangula pokadzula nyama,
yatsekula kwambiri pakamwa pawo kulimbana nane.
14 Ine ndatayika pansi ngati madzi
ndipo mafupa anga onse achoka mʼmalo mwake.
Mtima wanga wasanduka phula;
wasungunuka mʼkati mwanga.
15 Mphamvu zanga zauma ngati phale,
ndipo lilime langa lamamatira ku nsagwada;
mwandigoneka mʼfumbi la imfa.
17 “Mtima wanga wasweka,
masiku anga atha,
manda akundidikira.
2 Ndithudi, anthu ondiseka andizungulira;
maso anga akupenyetsetsa mdani wanga.
3 “Inu Mulungu, patseni chikole chimene mukufuna.
Ndani wina amene adzandiperekera ine chikole?
4 Inu mwatseka maganizo awo kuti asamvetse zinthu;
choncho simudzawalola kuti apambane.
5 Ngati munthu apereka mnzake chifukwa cha chuma,
ana ake sadzaona mwayi.
6 “Mulungu wandisandutsa chisudzo chochiseka aliyense,
munthu amene anthu amalavulira malovu nkhope yake.
7 Mʼmaso mwanga mwada ndi chisoni;
ndawonda ndi mutu womwe.
8 Anthu olungama akudabwa nazo zimenezi;
anthu osachimwa akupsera mtima anthu osapembedza Mulungu.
9 Komabe anthu olungama adzasunga njira zawo,
ndipo anthu a makhalidwe abwino mphamvu zawo zidzanka zikuchuluka.
10 “Tsono bwerani nonsenu, bwerezaninso mawu anuwo,
sindidzapezapo munthu wanzeru pakati panupo.
11 Masiku anga atha, zimene ndinakonza zalephereka,
pamodzinso ndi zokhumba za mtima wanga.
12 Anthu awa amasandutsa usiku kukhala usana,
nthawi ya usiku iwo amati ‘kwatsala pangʼono kucha.’
13 Ngati nyumba imene ndikuyiyembekezera ndi manda,
ngati ndiyala bedi langa mu mdima,
14 ngati ndinena kwa dzenje la manda ‘ndinu abambo anga,’
ndiponso kwa mphutsi kuti, ‘ndinu amayi anga’ kapena ‘mlongo wanga,’
15 tsono chiyembekezo changa chili kuti?
Ndani angaone populumukira panga?
16 Ndithu sindidzakhalanso ndi chiyembekezo chilichonse,
polowa mʼmanda, pamene ndidzatsikira ku fumbi.”
Chenjezo pa Kusakhulupirira
7 Tsono monga Mzimu Woyera akuti,
“Lero mukamva mawu ake,
8 musawumitse mitima yanu
ngati munachitira pamene munawukira,
pa nthawi yoyesedwa mʼchipululu.
9 Pamene makolo anu anandiputa ndi kundiyesa,
ndipo kwa zaka makumi anayi anaona zimene Ine ndinachita.
10 Nʼchifukwa chake ndinawukwiyira mʼbadowo,
ndipo Ine ndinati, ‘Nthawi zonse mitima yawo imasochera,
ndipo iwo sadziwa njira zanga.’
11 Kotero Ine ndinalumbira nditakwiya kuti,
‘Iwo sadzalowa mu mpumulo wanga.’ ”
12 Abale samalani, kuti pasapezeke wina aliyense mwa inu wokhala ndi mtima woyipa ndi wosakhulupirira, womulekanitsa ndi Mulungu wamoyo. 13 Koma muzilimbikitsana tsiku ndi tsiku, ikanalipo nthawi imene imatchedwa kuti “Lero” kuti aliyense wa inu mtima wake usawumitsidwe ndi chinyengo cha tchimo. 14 Pakuti timakhala anzake a Khristu, ngati tigwiritsitsa mpaka potsiriza chitsimikizo chimene tinali nacho pachiyambi. 15 Monga kunanenedwa kuti,
“Lero ngati mumva mawu ake,
musawumitse mitima yanu
ngati momwe munachitira pamene munawukira.”
16 Nanga amene anamva ndi kuwukira anali ndani? Kodi si onse amene Mose anawatulutsa mu Igupto? 17 Nanga amene Mulungu anawakwiyira zaka makumi anayi anali ndani? Kodi si anthu amene anachimwa, amene mitembo yawo inatsala mʼchipululu muja? 18 Nanga Mulungu ankanena za ndani kuti sadzalowa mu mpumulo wake? Pajatu ankanena za anthu amene sanamvere aja. 19 Tsono ife tikuona kuti sanalowe chifukwa cha kusakhulupirika kwawo.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.