Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Mawu Oyamba
1 Mʼdziko la Uzi munali munthu wina, dzina lake Yobu. Munthu ameneyu anali wosalakwa ndi wolungama mtima, ankaopa Mulungu ndi kupewa zoyipa.
Yobu Ayesedwa Kachiwiri
2 Tsiku linanso pamene ana a Mulungu anabwera kudzadzionetsa pamaso pa Yehova, nayenso Satana anabwera nawo limodzi kudzadzionetsa pamaso pa Yehova. 2 Ndipo Yehova anati kwa Satana, “Kodi iwe ukuchokera kuti?”
Satana anayankha Yehova kuti, “Ndakhala ndikungoyendayenda ndi kumangozungulira mʼdzikoli.”
3 Pamenepo Yehova anati kwa Satana, “Kodi unalingalirapo za mtumiki wanga Yobu? Palibe wina pa dziko lapansi wofanana naye; ndi munthu wosalakwa ndi wolungama mtima, munthu amene amaopa Mulungu ndi kupewa zoyipa. Ndipo iye akanalibe wangwiro, ngakhale iwe unandiwumiriza kuti ndikulole kuti umuvutitse popanda chifukwa.”
4 Satana anayankha kuti, “Iye ayesedwe mʼthupi mwake. Munthu angathe kupereka zonse ali nazo malingana iyeyo ali ndi moyo. 5 Koma tatambasulani dzanja lanu ndi kuwononga thupi lake, ndipo iyeyo adzakutukwanani ndithu pamaso panu.”
6 Yehova anati kwa Satana, “Chabwino, iye ali mʼmanja mwako; koma moyo wake usawuchotse.”
7 Choncho Satana anachoka pamaso pa Yehova napita kukazunza Yobu ndi zilonda zaululu pa thupi lake lonse. 8 Pamenepo Yobu anatenga phale ndi kumadzikanda nalo atakhala pa dzala la phulusa.
9 Mkazi wake anati kwa iye, “Kodi ukuwumirirabe kukhala wangwiro? Tukwana Mulungu kuti ufe!”
10 Yobu anayankha kuti, “Ukuyankhula ngati mkazi wopusa. Kodi tidzalandira zokoma zokhazokha kwa Mulungu, osalandiranso zowawa?”
Mu zonsezi, Yobu sanachimwe pa zimene anayankhula.
Salimo la Davide.
26 Weruzeni Inu Yehova
pakuti ndakhala moyo wosalakwa.
Ndadalira Yehova
popanda kugwedezeka.
2 Patseni mayeso, Inu Yehova ndipo ndiyeseni,
santhulani mtima wanga ndi maganizo anga;
3 pakuti chikondi chanu chili pamaso panga nthawi zonse,
ndipo ndimayenda mʼchoonadi chanu nthawi zonse.
4 Ine sindikhala pansi pamodzi ndi anthu achinyengo,
kapena kufunsa nzeru kwa achiphamaso.
5 Ndimanyansidwa ndi msonkhano wa anthu ochita zoyipa
ndipo ndimakana kukhala pansi pamodzi ndi oyipa.
6 Ndimasamba mʼmanja mwanga kuonetsa kusalakwa kwanga
ndi kupita kukatumikira pa guwa lanu la nsembe, Inu Yehova,
7 kulengeza mofuwula za matamando anu
ndi kuwuza onse za ntchito zanu zodabwitsa.
8 Ndimakonda Nyumba imene Inu Yehova mumakhalamo,
malo amene ulemerero wanu umapezekako.
9 Musachotse moyo wanga pamodzi ndi ochimwa,
moyo wanga pamodzi ndi anthu akupha anzawo,
10 amene mʼmanja mwawo muli ndondomeko zoyipa,
dzanja lawo lamanja ladzaza ndi ziphuphu.
11 Koma ine ndimakhala moyo wosalakwa;
mu msonkhano wa anthu anu ndidzatamanda Yehova.
12 Ndayima pa malo wopanda zovuta
ndipo ndidzatamanda Yehova mu msonkhano waukulu.
Khristu Mwana wa Mulungu Aposa Angelo
1 Kale lija Mulungu ankayankhula ndi makolo athu pa nthawi zosiyanasiyana ndiponso mwa njira zosiyanasiyana kudzera mwa aneneri. 2 Koma masiku otsiriza ano, Mulungu wayankhula nafe kudzera mwa Mwana wake. Mwanayu anamusankha kuti akhale mwini wa zinthu zonse, ndiponso Mulungu analenga dziko lonse kudzera mwa Iye. 3 Mwanayo ndiye kuwala kwa ulemerero wa Mulungu, chithunzithunzi chenicheni cha khalidwe lake. Iyeyu amachirikiza zinthu zonse ndi mphamvu ya mawu ake. Iye atayeretsa anthu kuchoka ku machimo awo, anakhala pansi kumwamba kudzanja lamanja la Mulungu waulemerero. 4 Mwanayu ndi wamkulu koposa angelo, monga momwe dzina limene analandira limaposa dzina la angelo.
Yesu Wofanana ndi Abale ake
5 Mulungu sanapereke kwa angelo ulamuliro wa dziko limene likubwerali, limene ife tikulinena. 6 Koma palipo pena pamene wina anachitira umboni kuti,
“Kodi munthu ndani kuti muzimukumbukira,
kapena mwana wa munthu kuti muzimusamalira?
7 Munamuchepetsa pangʼono kusiyana ndi angelo;
munamupatsa ulemerero ndi ulemu.
8 Munamupatsa ulamuliro pa zinthu zonse.”
Poyika zinthu zonse pansi pa ulamuliro wake, Mulungu sanasiye kanthu kamene sikali mu ulamuliro wake. Koma nthawi ino sitikuona zinthu pansi pa ulamuliro wake. 9 Koma tikuona Yesu, amene kwa kanthawi kochepa anamuchepetsa pangʼono kwa angelo, koma tsopano wavala ulemerero ndi ulemu chifukwa anamva zowawa za imfa, kuti mwachisomo cha Mulungu, Iye afere anthu onse.
10 Mulungu amene analenga zinthu zonse ndipo zinthu zonse zilipo chifukwa cha Iye ndi mwa Iye, anachiona choyenera kubweretsa ana ake ambiri mu ulemerero. Kunali koyenera kudzera mʼnjira ya zowawa, kumusandutsa Yesu mtsogoleri wangwiro, woyenera kubweretsa chipulumutso chawo. 11 Popeza iye amene ayeretsa ndi oyeresedwa onse ndi abanja limodzi. Nʼchifukwa chake Yesu sachita manyazi kuwatcha iwo abale ake. 12 Iye akuti,
“Ine ndidzawuza abale anga za dzina lanu.
Ndidzakuyimbirani nyimbo zamatamando pamaso pa mpingo.”
2 Afarisi ena anabwera kudzamuyesa pomufunsa kuti, “Kodi malamulo amalola kuti mwamuna asiye mkazi wake?”
3 Iye anayankha kuti, “Kodi Mose anakulamulani chiyani?”
4 Iwo anati, “Mose amaloleza mwamuna kulemba kalata ya chisudzulo ndi kumuchotsa mkazi.”
5 Yesu anayankha kuti, “Mose anakulemberani lamulo ili chifukwa chakuwuma kwa mitima yanu. 6 Koma pachiyambi cha chilengedwe, Mulungu ‘analenga iwo, mwamuna ndi mkazi.’ 7 ‘Pa chifukwa ichi mwamuna adzasiya abambo ake ndi amayi ake nakaphatikana ndi mkazi wake, 8 ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi.’ Potero sali awirinso, koma mmodzi. 9 Chifukwa chake chimene Mulungu wachilumikiza pamodzi, munthu wina asachilekanitse.”
10 Pamene analinso mʼnyumba, ophunzira anamufunsa Yesu za izi. 11 Iye anayankha kuti, “Aliyense amene aleka mkazi wake ndi kukakwatira wina achita chigololo kulakwira mkaziyo. 12 Ndipo akasiya mwamuna wake ndi kukakwatiwa ndi wina, achita chigololo.”
Yesu Adalitsa Ana
13 Anthu anabweretsa ana kwa Yesu kuti awadalitse, koma ophunzira anawadzudzula. 14 Pamene Yesu anaona zimenezi anayipidwa. Anati kwa iwo, “Lolani ana abwere kwa Ine, ndipo musawaletse, pakuti Ufumu wa Mulungu uli wa onga awa. 15 Ndikukuwuzani choonadi, aliyense amene sadzalandira Ufumu wa Mulungu ngati kamwana sadzalowamo.” 16 Ndipo ananyamula ana mʼmanja ake, ndi kuyika manja ake pa iwo nawadalitsa.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.