Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 26

Salimo la Davide.

26 Weruzeni Inu Yehova
    pakuti ndakhala moyo wosalakwa.
Ndadalira Yehova
    popanda kugwedezeka.
Patseni mayeso, Inu Yehova ndipo ndiyeseni,
    santhulani mtima wanga ndi maganizo anga;
pakuti chikondi chanu chili pamaso panga nthawi zonse,
    ndipo ndimayenda mʼchoonadi chanu nthawi zonse.
Ine sindikhala pansi pamodzi ndi anthu achinyengo,
    kapena kufunsa nzeru kwa achiphamaso.
Ndimanyansidwa ndi msonkhano wa anthu ochita zoyipa
    ndipo ndimakana kukhala pansi pamodzi ndi oyipa.
Ndimasamba mʼmanja mwanga kuonetsa kusalakwa kwanga
    ndi kupita kukatumikira pa guwa lanu la nsembe, Inu Yehova,
kulengeza mofuwula za matamando anu
    ndi kuwuza onse za ntchito zanu zodabwitsa.
Ndimakonda Nyumba imene Inu Yehova mumakhalamo,
    malo amene ulemerero wanu umapezekako.

Musachotse moyo wanga pamodzi ndi ochimwa,
    moyo wanga pamodzi ndi anthu akupha anzawo,
10 amene mʼmanja mwawo muli ndondomeko zoyipa,
    dzanja lawo lamanja ladzaza ndi ziphuphu.
11 Koma ine ndimakhala moyo wosalakwa;
    mu msonkhano wa anthu anu ndidzatamanda Yehova.

12 Ndayima pa malo wopanda zovuta
    ndipo ndidzatamanda Yehova mu msonkhano waukulu.

Yobu 7

“Kodi munthu sakhala ndi ntchito yowawa pa dziko lapansi?
    Kodi masiku ake sali ngati munthu waganyu?
Monga ngati kapolo wolakalaka mthunzi wa nthawi yamadzulo,
    kapena ngati munthu waganyu woyembekezera malipiro ake,
choncho ine ndapatsidwa nthawi yongovutika pachabe,
    ndiponso usiku wamasautso wapatsidwa kwa ine.
Ndikamagona ndimaganiza kuti, ‘Kodi kucha liti?’
    Usikuwo umatalika ndipo sindigona tulo mpaka mmawa.
Thupi langa ladzala mphutsi ndi zipsera,
    khungu langa langʼambika ndipo likutuluka mafinya.

“Masiku anga ndi othamanga kupambana makina wolukira nsalu,
    ndipo amatha wopanda chiyembekezo.
Inu Mulungu kumbukirani kuti moyo wanga uli ngati mpweya;
    sindidzaonanso masiku achisangalalo.
Amene akundiona tsopano akundiona;
    mudzandifunafuna koma sindidzapezekanso.
Monga mtambo umazimirira ndi kukanganuka,
    momwemonso munthu amene walowa mʼmanda sabwerera.
10 Iye sadzabweranso ku nyumba kwake
    ndipo onse omudziwa adzamuyiwala.

11 “Nʼchifukwa chake ine sindidzakhala chete;
    ndidzayankhula mopsinjika mtima,
    ndidzadandaula mowawidwa mtima.
12 Kodi ine ndine nyanja kapena chirombo chamʼnyanja
    kuti inu mundiyikire alonda?
13 Pamene ndikuganiza kuti ndidzapeza chitonthozo pa bedi panga
    ndipo pogona panga padzachepetsa madandawulo anga,
14 ngakhale nthawi imeneyo mumandiopseza ndi maloto
    ndi kundichititsa mantha ndi masomphenya,
15 kotero kuti ndimalakalaka kudzikhweza kapena kufa,
    kupambana kupirira zowawa zimene ndikuzimva mʼthupi mwanga.
16 Ine ndatopa nawo moyo wanga; sindingakonde kukhala moyo nthawi zonse.
    Ndisiyeni ndekha pakuti moyo wanga ulibe tanthauzo.

17 “Kodi munthu nʼchiyani kuti muzimuganizira chotere,
    kuti muzisamala zochita zake,
18 kuti muzimusanthula mmawa uliwonse
    ndi kumamuyesa nthawi yonse?
19 Kodi simudzaleka kumandizonda
    kuti ndipezeko mpata wopumula?
20 Ngati ine ndachimwa, ndachita chiyani kwa Inu,
    Inu wopenyetsetsa anthu?
Chifukwa chiyani mwachititsa kuti ndikhale ngati choponyera chandamale chanu?
    Kodi ndasanduka katundu wolemera kwa Inu?
21 Chifukwa chiyani simukundikhululukira zolakwa zanga
    ndi kundichotsera machimo anga?
Pakuti posachedwa ndilowa mʼmanda;
    mudzandifunafuna ine koma simudzandionanso.”

Luka 16:14-18

14 Afarisi amene ankakonda ndalama atamva zimenezi anamuseka Yesu. 15 Yesu anawawuza kuti, “Inu ndi amene mumadzilungamitsa nokha pamaso pa anthu, koma Mulungu amadziwa mitima yanu. Zinthu zimene anthu amaziyesa zopambana, ndi zonyansa pamaso pa Mulungu.

Ziphunzitso Zina

16 “Malamulo ndi Aneneri zinagwira ntchito mpaka nthawi ya Yohane. Kuyambira nthawi imeneyo, Uthenga Wabwino wa ufumu wa Mulungu ukulalikidwa, ndipo aliyense akuyesetsa mwamphamvu kuti alowemo. 17 Nʼkwapafupi kuti kumwamba ndi dziko lapansi zichoke kulekana ndi kuti kalemba kakangʼono kachoke mʼMalamulo.

18 “Aliyense amene asiya mkazi wake ndi kukakwatira mkazi wina akuchita chigololo, ndipo mwamuna amene akwatira mkazi wosiyidwayo akuchitanso chigololo.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.