Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.
140 Landitseni Yehova kwa anthu oyipa;
tetezeni kwa anthu ankhanza,
2 amene mu mtima mwawo amakonza zinthu zoyipa
ndi kuyambitsa nkhondo tsiku lililonse.
3 Iwo amanola malilime awo kukhala akuthwa ngati a njoka;
pa milomo yawo pali ululu wa mamba.
Sela
4 Tetezeni Inu Yehova, kwa anthu oyipa;
tchinjirizeni kwa anthu ankhanza
amene amakonza zokola mapazi anga.
5 Anthu odzikuza anditchera msampha mobisika;
iwo atchera zingwe za maukonde awo
ndipo anditchera misampha pa njira yanga.
Sela
6 Inu Yehova, ine ndikuti, “Ndinu Mulungu wanga.”
Imvani kupempha kwanga Yehova.
7 Inu Ambuye Wamphamvuzonse, Mpulumutsi wanga wamphamvu,
mumateteza mutu wanga tsiku lankhondo.
8 Musawapatse anthu oyipa zokhumba zawo, Inu Yehova;
musalole kuti zokonza zawo zitheke,
mwina iwo adzayamba kunyada.
Sela
9 Mitu ya amene andizungulira
iphimbidwe ndi masautso amene milomo yawo yayambitsa.
10 Makala amoto agwere pa iwo;
aponyedwe pa moto,
mʼmaenje amatope, asatulukemonso.
11 Musalole kuti anthu achipongwe akhazikike mʼdziko;
choyipa chilondole anthu ankhanza.
12 Ndikudziwa kuti Yehova amapereka chiweruzo cholungama kwa anthu osauka,
ndipo amateteza zolinga za anthu osowa.
13 Zoonadi anthu olungama adzatamanda dzina lanu,
ndipo anthu owongoka mtima adzakhala pamaso panu.
Lamulo la Mfumu Lothandiza Ayuda
8 Tsiku lomwelo mfumu Ahasiwero anamupatsa mfumukazi Estere nyumba ya Hamani, mdani wa Ayuda. Ndipo Mordekai anafika pamaso pa mfumu, popeza Estere anamuwuza ubale wawo. 2 Mfumu inavula mphete yake yodindira imene analanda kwa Hamani ndipo Estere anamusankha Mordekai kukhala woyangʼanira nyumba ya Hamani.
3 Estere anayankhulanso ndi mfumu ndipo anadzigwetsa pa mapazi ake. Uku akulira iye anapempha mfumu kuti iletse choyipa, makamaka chiwembu chimene Hamani Mwagagi anakonza kuti awononge a Yuda. 4 Ndipo mfumu inamuloza Estere ndi ndodo yake yagolide ndipo Estere anadzuka ndi kuyima pamaso pake.
5 Iye anati, “Ngati chikomera mfumu ndi kukukondweretsani, ngati pempho langa muliona kuti ndi loyenera ndi kuti mukondwera nane tsono mfumu ilole kuti lamulo lilembedwe kusintha mawu a mʼmakalata amene Hamani mwana wa Hamedata, Mwagagi, anatumiza ku zigawo zonse za mfumu. Paja Hamani analemba kuti Ayuda onse awonongedwe. 6 Kodi ndingapirire bwanji pamene ndi kuona tsoka likugwera anthu a mtundu wanga? Ndingapirire bwanji pamene abale anga akuwonongedwa?”
7 Mfumu Ahasiwero anamuyankha mfumukazi Estere ndi Mordekai Myuda kuti, “Ndapereka nyumba ya Hamani kwa Estere ndipo Hamaniyo amupachika kale pa mtanda chifukwa anafuna kuwononga Ayuda. 8 Tsono inu awiri, lembani za Ayudawo monga mufunira. Mulembe mʼdzina la mfumu ndipo musindikize chizindikiro cha mphete ya mfumu popeza kuti cholembedwa mʼdzina la mfumu ndi kusindikizidwa ndi chizindikiro cha mphete ya mfumu sichingasinthidwe.”
9 Nthawi yomweyo, pa tsiku la 23 la mwezi wachitatu wa Sivani, mfumu inayitana alembi ake. Analemba zonse zokhudza Ayuda monga ananenera Mordekai. Analembera akazembe, abwanamkubwa ndi nduna za zigawo 127 kuyambira ku India mpaka ku Kusi. Zimene analamula Mordekai zinalembedwa mʼzilembo za chigawo chilichonse ndi chiyankhulo cha mtundu uliwonse wa anthu. Ayudanso anawalembera mʼmalemba awo ndi chiyankhulo chawo. 10 Mordekai analemba makalatawo mʼdzina la mfumu Ahasiwero, nawadinda ndi chizindikiro cha mphete ya mfumu. Ndipo anawatumiza ndi anthu amithenga amene anakwera pa akavalo a ufumu othamanga kwambiri obadwa mu khola la ufumu.
11 Mʼmakalata amenewa mfumu inalola kuti Ayuda okhala mu mzinda uliwonse akhale ndi ufulu wokumana ndi kudzitchinjiriza komanso kuwononga, kupha ndi kufafaniziratu gulu lililonse la nkhondo la anthu a mtundu uliwonse kapena chigawo chimene chingawathire nkhondo. Ayudawo analoledwa kuwononga gulu lankhondo lija, ana awo ndi akazi awo komanso kuti afunkhe katundu wawo. 12 Ayuda analoledwa kuchita zimenezi mʼzigawo zonse za Mfumu Ahasiwero pa tsiku limodzi lokha la 13 la mwezi wa 12, mwezi wa Adara. 13 Mawu a mʼmakalatawo anayenera kudziwitsidwa kwa anthu a mtundu uliwonse mu chigawo chilichonse kuti ndi lamulo ndithu kwa anthu a mtundu uliwonse ndi kuti Ayuda adzakhale okonzeka pa tsikulo kulipsira kwa adani awo.
14 Atawalamulira a mfumu, amithenga aja anapita nawo makalata mwachangu, atakwera pa akavalo a mfumu. Ndipo lamulolo analiperekanso ku likulu la mzinda wa Susa.
15 Mordekai anachoka pamaso pa mfumu atavala zovala zaufumu zooneka ngati mtambo ndi zofewa zoyera, chipewa chachikulu cha golide ndi mkanjo wapepo. Ndipo mzinda wa Susa unafuwula mokondwa. 16 Kwa Ayuda inali nthawi ya nkhope zowala ndi za chimwemwe, chikondwerero ndi ulemu. 17 Mʼchigawo chilichonse ndi mu mzinda uliwonse, kumene mawu a mfumu onena za lamulo lake anafika, kunali chimwemwe ndi chikondwerero pakati pa Ayuda. Linali tsiku la phwando ndi chikondwerero. Ndipo anthu ambiri a mitundu ina anazitcha Ayuda chifukwa anachita mantha ndi Ayudawo.
Za Kuchimwitsa Ena
6 “Koma ngati wina aliyense achimwitsa mmodzi wa ana awa, amene akhulupirira Ine, kuti achimwe, kukanakhala bwino kuti iye amangiriridwe chimwala chachikulu mʼkhosi mwake ndi kumizidwa pansi pa nyanja. 7 Tsoka dziko lapansi chifukwa cha zinthu zimene ziyenera kubwera, koma tsoka kwa munthu amene abweretsa zotere! 8 Ngati dzanja lako kapena phazi lako likuchimwitsa, lidule ndi kulitaya. Ndi bwino kwa iwe kulowa mʼmoyo wosatha wolumala kusiyana ndi kukhala ndi manja awiri kapena mapazi awiri ndi kukaponyedwa ku moto wosatha. 9 Ndipo ngati diso lako likuchimwitsa, ulichotse ndi kulitaya. Ndi bwino kwa iwe kuti ukalowe ku moyo wosatha ndi diso limodzi kuposa ndi kukhala ndi maso awiri ndi kukaponyedwa ku moto wa gehena.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.