Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Mathero: Mkazi Wangwiro
10 Kodi mkazi wangwiro angathe kumupeza ndani?
Ndi wokwera mtengo kuposa miyala yamtengowapatali.
11 Mtima wa mwamuna wake umamukhulupirira
ndipo mwamunayo sasowa phindu.
12 Masiku onse a moyo wake
mkaziyo amachitira mwamuna wake zabwino zokhazokha osati zoyipa.
13 Iye amafunafuna ubweya ndi thonje;
amagwira ntchito ndi manja ake mwaufulu.
14 Iye ali ngati sitima zapamadzi za anthu amalonda,
amakatenga chakudya chake kutali.
15 Iye amadzuka kusanache kwenikweni;
ndi kuyamba kukonzera a pa banja pake chakudya
ndi kuwagawira ntchito atsikana ake antchito.
16 Iye amalingalira za munda ndi kuwugula;
ndi ndalama zimene wazipeza amalima munda wamphesa.
17 Iye amavala zilimbe
nagwira ntchito mwamphamvu ndi manja ake.
18 Iye amaona kuti malonda ake ndi aphindu,
choncho nyale yake sizima usiku wonse.
19 Iye amadzilukira thonje
ndipo yekha amagwira chowombera nsalu.
20 Iye amachitira chifundo anthu osauka
ndipo amapereka chithandizo kwa anthu osowa.
21 Iye saopa kuti banja lake lifa ndi kuzizira pa nyengo yachisanu;
pakuti onse amakhala atavala zovala zofunda.
22 Iye amadzipangira yekha zoyala pa bedi pake;
amavala zovala zabafuta ndi zapepo.
23 Mwamuna wake ndi wodziwika pa chipata cha mzinda,
ndipo amakhala pakati pa akuluakulu a mʼdzikomo.
24 Iye amasoka nsalu zabafuta nazigulitsa;
amaperekanso mipango kwa anthu amalonda.
25 Mphamvu ndi ulemu zimakhala ngati chovala chake;
ndipo amaseka osaopa zamʼtsogolo.
26 Iye amayankhula mwanzeru,
amaphunzitsa anthu mwachikondi.
27 Iye amayangʼanira makhalidwe a anthu a pa banja lake
ndipo sachita ulesi ndi pangʼono pomwe.
28 Ana ake amamunyadira ndipo amamutcha kuti wodala;
ndipo mwamuna wake, amamuyamikira nʼkumati,
29 “Pali akazi ambiri amene achita zinthu zopambana
koma iwe umawaposa onsewa.”
30 Nkhope yachikoka ndi yonyenga, ndipo kukongola nʼkosakhalitsa;
koma mkazi amene amaopa Yehova ayenera kutamandidwa.
31 Mupatseni mphotho chifukwa cha zimene iye wachita
ndipo ntchito zake zimutamande ku mabwalo.
BUKU LOYAMBA
Masalimo 1–41
1 Wodala munthu
amene satsatira uphungu wa anthu ochimwa,
kapena kuyima mʼnjira ya anthu oyipa,
kapena kukhala mʼmagulu a anthu onyoza.
2 Koma chikondwerero chake chili mʼmalamulo a Yehova
ndipo mʼmalamulo akewo amalingaliramo usana ndi usiku.
3 Iye ali ngati mtengo wodzalidwa mʼmbali mwa mitsinje ya madzi,
umene umabereka zipatso zake pa nyengo yake
ndipo masamba ake safota.
Chilichonse chimene amachita amapindula nacho.
4 Sizitero ndi anthu oyipa!
Iwo ali ngati mungu
umene umawuluzidwa ndi mphepo.
5 Kotero anthu oyipa sadzatha kuyima pa chiweruzo,
kapena anthu ochimwa mu msonkhano wa anthu olungama.
6 Pakuti Yehova amayangʼanira mayendedwe a anthu olungama,
koma mayendedwe a anthu oyipa adzawonongeka.
Mitundu Iwiri ya Nzeru
13 Ndani mwa inu amene ndi wanzeru ndi womvetsa zinthu? Mulekeni aonetse ndi makhalidwe ake abwino kuti nzeru ndiye zikutsogolera kudzichepetsa kwake ndi zochita zake 14 Koma ngati muli ndi mtima wakaduka ndi odzikonda, musadzitamandire kapena kukana choonadi. 15 “Nzeru” zotere sizochokera kumwamba koma ndi za mʼdziko lapansi, si zauzimu koma ndi za ziwanda. 16 Pakuti pamene pali kaduka ndi kudzikonda pomweponso pamakhala chisokonezo ndi zochitika zoyipa zonse.
17 Koma nzeru imene imachoka kumwamba, poyamba ndi yangwiro, ndi yokonda mtendere, yoganizira za ena, yogonjera, yodzaza ndi chifundo ndi chipatso chabwino, yosakondera ndi yoona mtima. 18 Anthu amtendere amene amadzala mtendere amakolola chilungamo.
Kugonjera Mulungu
4 Nʼchiyani chimene chimayambitsa ndewu ndi mapokoso pakati panu? Kodi sizichokera ku zilakolako zimene zimalimbana mʼkati mwanu? 2 Mumalakalaka zinthu koma simuzipeza, choncho mumapha. Mumasirira zinthu koma simutha kuzipeza zimene mukufuna, choncho mumakangana ndi kumenyana. Mulibe zinthuzo chifukwa simupempha kwa Mulungu. 3 Koma ngakhale mumapempha simulandira, chifukwa mumapempha ndi zolinga zoyipa. Mumapempha kuti muzigwiritse ntchito pa zokusangalatsani nokha.
7 Dziperekeni nokha kwa Mulungu. Mukaneni Mdierekezi ndipo adzakuthawani. 8 Sendezani kufupi ndi Mulungu ndipo Iye adzasendeza kwa inu. Sambani mʼmanja mwanu, inu anthu ochimwa. Yeretsani mitima yanu, inu anthu okayikira.
Yesu aneneratu za Imfa yake Kachiwiri
30 Anachoka malo amenewo nadutsa ku Galileya. Yesu sanafune kuti wina aliyense adziwe kumene anali, 31 chifukwa amaphunzitsa ophunzira ake. Anati kwa iwo, “Mwana wa Munthu adzaperekedwa mʼmanja mwa anthu. Adzamupha, ndipo patatha masiku atatu adzauka.” 32 Koma sanazindikire chimene amatanthauza, ndipo anachita mantha kuti amufunse.
Wamkulu Ndani mu Ufumu wa Mulungu?
33 Anafika ku Kaperenawo. Pamene anali mʼnyumba, anawafunsa kuti, “Kodi mumatsutsana chiyani mʼnjira muja?” 34 Koma anakhala chete chifukwa ali mʼnjira amatsutsana za kuti wamkulu kuposa onse ndani.
35 Atakhala pansi, Yesu anayitana khumi ndi awiriwo nati, “Ngati wina aliyense afuna kukhala woyamba, ayenera kukhala wotsiriza ndi wotumikira onse.”
36 Anatenga kamwana nakayimiritsa pakati pawo ndipo anawawuza kuti, 37 “Aliyense wolandira mmodzi wa ana angʼono awa mʼdzina langa alandira Ine; ndipo aliyense wolandira Ine salandira Ine koma amene anandituma.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.