Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
21 Pamene mtima wanga unasautsidwa
ndi kuwawidwa mu mzimu mwanga,
22 ndinali wopusa ndi wosadziwa;
ndinali chirombo chopanda nzeru pamaso panu.
23 Komabe ineyo ndili ndi Inu nthawi zonse;
mumandigwira dzanja langa lamanja.
24 Inu mumanditsogolera ndi malangizo anu
ndipo pambuyo pake mudzanditenga ku ulemerero.
25 Kodi kumwamba ndili ndi yani kupatula Inu?
Ndipo dziko lapansi lilibe chilichonse chimene ndimachilakalaka koposa Inuyo.
26 Thupi ndi mtima wanga zitha kufowoka,
koma Mulungu ndiye mphamvu ya mtima wanga
ndi cholandira changa kwamuyaya.
27 Iwo amene ali kutali ndi Inu adzawonongeka;
Inu mumawononga onse osakhulupirika pamaso panu.
28 Koma kunena za Ine ndi kwabwino kukhala pafupi ndi Mulungu.
Ndatsimikiza kuti Ambuye Yehova ndiwo pothawirapo panga
ndipo ndidzalalika ntchito zanu zonse.
29 Munthu amene amawumitsabe khosi lake atadzudzulidwa kwambiri,
adzawonongeka mwadzidzidzi popanda chomuchiritsa.
2 Anthu olungama akamalamulira mʼdziko anthu amakondwa,
koma ngati dziko lilamulidwa ndi anthu oyipa mtima anthu amadandaula.
3 Munthu amene amakonda nzeru amasangalatsa abambo ake,
koma woyenda ndi akazi achiwerewere amasakaza chuma chake.
4 Mfumu imalimbitsa dziko poweruza mwachilungamo,
koma mfumu imene imawumiriza anthu kuti ayipatse mphatso imawononga dziko.
5 Munthu woshashalika mnzake,
akudziyalira ukonde mapazi ake.
6 Munthu woyipa amakodwa ndi machimo ake,
koma wochita chilungamo amayimba lokoma.
7 Munthu wolungama amasamalira anthu osauka,
koma woyipa salabadira zimenezi.
8 Anthu onyoza atha kuwutsa ziwawa mu mzinda,
koma anthu anzeru amaletsa ukali.
9 Ngati munthu wanzeru atsutsana ndi chitsiru,
chitsirucho chimachita phokoso ndi kumangoseka ndipo sipakhala mtendere.
10 Anthu okhetsa magazi amadana ndi munthu wangwiro
koma anthu olungama amasamalira moyo wake.
11 Munthu wopusa amaonetsa mkwiyo wake,
koma munthu wanzeru amadzigwira.
12 Ngati wolamulira amvera zabodza,
akuluakulu ake onse adzakhala oyipa.
13 Munthu wosauka ndi munthu wopondereza anzake amafanana pa kuti:
Yehova ndiye anawapatsa maso onsewa.
14 Ngati mfumu iweruza osauka moyenera,
mpando wake waufumu udzakhazikika nthawi zonse.
15 Ndodo ndi chidzudzulo zimapatsa nzeru
koma mwana womulekerera amachititsa amayi ake manyazi.
16 Oyipa akamalamulira zoyipa zimachuluka,
koma anthu olungama adzaona kugwa kwa anthu oyipawo.
17 Umulange mwana wako ndipo adzakupatsa mtendere
ndi kusangalatsa mtima wako.
18 Ngati uthenga wochokera kwa Yehova supezeka anthu amangochita zofuna zawo;
koma wodala ndi amene amasunga malamulo.
19 Munthu wantchito sangalangizidwe ndi mawu okha basi;
ngakhale awamvetse mawuwo sadzatha kuchitapo kanthu.
20 Ngakhale munthu wa uchitsiru nʼkuti ndiponi popeza chikhulupiriro chilipo
kuposa munthu wodziyesa yekha kuti ndi wanzeru poyankhula.
21 Ngati munthu asasatitsa wantchito wake kuyambira ali mwana,
potsirizira adzapeza kuti wantchitoyo wasanduka mlowachuma wake.
22 Munthu wamkwiyo amayambitsa mikangano,
ndipo munthu waukali amachita zolakwa zambiri.
23 Kunyada kwa munthu kudzamutsitsa,
koma munthu wodzichepetsa amalandira ulemu.
24 Woyenda ndi munthu wakuba ndi mdani wa moyo wake womwe;
amalumbira koma osawulula kanthu.
25 Kuopa munthu kudzakhala ngati msampha,
koma aliyense amene amadalira Yehova adzatetezedwa.
26 Anthu ambiri amafunitsitsa kuti wolamulira awakomere mtima,
koma munthu amaweruzidwa mwachilungamo ndi thandizo la Yehova basi.
27 Anthu olungama amanyansidwa ndi anthu achinyengo;
koma anthu oyipa amanyansidwa ndi anthu a mtima wowongoka.
Kodi Yesu ndi Khristu?
25 Pa nthawi imeneyi anthu ena a ku Yerusalemu anayamba kufunsana kuti, “Kodi uyu si munthu uja akufuna kumuphayu? 26 Uyu ali apa, kuyankhula poyera, ndipo iwo sakunena kanthu kwa Iye. Kodi olamulira atsimikizadi kuti Iye ndi Khristu? 27 Koma ife tikudziwa kumene achokera munthuyu; pamene Khristu adzabwere, palibe amene adzadziwa kumene akuchokera.”
28 Kenaka Yesu, akuphunzitsabe mʼbwalo la Nyumba ya Mulungu anafuwula kuti, “Zoona, mukundidziwa Ine, ndipo mukudziwa kumene ndikuchokera. Ine sindili pano mwa Ine ndekha, koma Iye amene anandituma Ine ndi woona. Inu simukumudziwa, 29 koma Ine ndikumudziwa chifukwa ndichokera kwa Iyeyo ndipo ndiye amene anandituma Ine.”
30 Chifukwa cha izi iwo anayesa kumugwira Iye, koma palibe aliyense amene anayika dzanja lake pa Iye, chifukwa nthawi yake inali isanafike. 31 Komabe, ambiri a mʼchigulucho anamukhulupirira Iye. Iwo anati, “Kodi pamene Khristu abwera, adzachita zizindikiro zodabwitsa zambiri kuposa munthu uyu?”
32 Afarisi anamva chigulucho chikunongʼona zinthu zotere za Iye. Kenaka akulu a ansembe ndi Afarisi anatumiza asilikali a mʼNyumba ya Mulungu kuti akamumange Iye.
33 Yesu anati, “Ine ndili ndi inu kwa kanthawi kochepa chabe, ndipo kenaka ndizipita kwa Iye amene anandituma Ine. 34 Inu mudzandifunafuna koma simudzandipeza; ndipo kumene Ine ndili inu simungathe kubwera.”
35 Ayuda anati kwa wina ndi mnzake, “Kodi munthu uyu akuganizira zoti apite kuti kumene ife sitingathe kumupeza Iye? Kodi Iye adzapita kumene anthu amakhala mobalalikana pakati pa Agriki, ndi kuphunzitsa Agriki? 36 Kodi Iye amatanthauza chiyani pamene anati, ‘Inu mudzandifunafuna koma simudzandipeza,’ ndi ‘Kumene Ine ndili, inu simungathe kubwera?’ ”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.