Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 73:21-28

21 Pamene mtima wanga unasautsidwa
    ndi kuwawidwa mu mzimu mwanga,
22 ndinali wopusa ndi wosadziwa;
    ndinali chirombo chopanda nzeru pamaso panu.

23 Komabe ineyo ndili ndi Inu nthawi zonse;
    mumandigwira dzanja langa lamanja.
24 Inu mumanditsogolera ndi malangizo anu
    ndipo pambuyo pake mudzanditenga ku ulemerero.
25 Kodi kumwamba ndili ndi yani kupatula Inu?
    Ndipo dziko lapansi lilibe chilichonse chimene ndimachilakalaka koposa Inuyo.
26 Thupi ndi mtima wanga zitha kufowoka,
    koma Mulungu ndiye mphamvu ya mtima wanga
    ndi cholandira changa kwamuyaya.

27 Iwo amene ali kutali ndi Inu adzawonongeka;
    Inu mumawononga onse osakhulupirika pamaso panu.
28 Koma kunena za Ine ndi kwabwino kukhala pafupi ndi Mulungu.
    Ndatsimikiza kuti Ambuye Yehova ndiwo pothawirapo panga
    ndipo ndidzalalika ntchito zanu zonse.

Miyambo 22:1-21

22 Mbiri yabwino ndi yofunika kuposa chuma chambiri;
    kupeza kuyanja nʼkwabwino kuposa siliva kapena golide.

Wolemera ndi wosauka ndi ofanana;
    onsewa anawalenga ndi Yehova.

Munthu wochenjera akaona choopsa amabisala,
    koma munthu wopusa amangopitirira ndipo amadzanongʼoneza bondo.

Mphotho ya munthu wodzichepetsa
    ndi woopa Yehova ndi chuma, ulemu ndi moyo.

Mʼnjira za anthu oyipa muli minga ndi misampha,
    koma amene amasala moyo wake adzazipewa zonsezo.

Mwana muzimuphunzitsa njira yake,
    ndipo akadzakalamba sadzachokamo.

Wolemera amalamulira wosauka,
    ndipo wokongola zinthu amakhala kapolo wa womukongozayo.

Amene amafesa zoyipa amakolola mavuto,
    ndipo ndodo yaukali wake idzathyoka.

Amene ali ndi diso lachifundo adzadalitsika,
    pakuti iye amagawana chakudya chake ndi anthu osauka.

10 Chotsani munthu wonyoza, ndipo kukangana kudzatha;
    mapokoso ndi zonyoza zidzaleka.

11 Amene amakonda kukhala woyera mtima ndi kumayankhula mawu abwino,
    adzakhala bwenzi la mfumu.

12 Maso a Yehova amakhala pa anthu odziwa bwino zinthu,
    koma Iye adzalepheretsa mawu a anthu osakhulupirika.

13 Munthu waulesi amati,
    “Kunjaku kuli mkango. Ine ndidzaphedwa mʼmisewu!”

14 Pakamwa pa mkazi wachigololo pali ngati dzenje lozama;
    amene Yehova wamukwiyira adzagwamo.

15 Uchitsiru umakhala mu mtima mwa mwana,
    koma ndodo yomulangira mwanayo idzachotsa uchitsiruwo.

16 Amene amapondereza anthu osauka kuti awonjezere chuma chake,
    ndiponso amene amapereka mphatso kwa anthu olemera onsewa adzasauka.

Malangizo a Anthu Anzeru

17 Utchere khutu lako ndipo umvere mawu anzeru;
    uyike mtima wako pa zimene ndikukuphunzitsa kuti udziwe.
18 Zidzakhala zokondweretsa ngati uzisunga mu mtima mwako
    ndi wokonzeka kuziyankhula.
19 Ndakuphunzitsa zimenezi lero
    koma makamaka uziopa Yehova.
20 Kodi suja ndinakulembera malangizo makumi atatu
    okuchenjeza ndi okupatsa nzeru,
21 malangizo okudziwitsa zolungama
    ndi zoona
    ndi kuti ukawayankhe zoona amene akutumawo?

Aroma 3:9-20

Palibe Munthu Wolungama

Kodi timalize bwanji? Kodi Ayuda ndife oposa anthu ena? Ayi. Mʼnjira iliyonse ayi! Ife tinanena kale kuti Ayuda ndi a mitundu ina omwe ndi ochimwa. 10 Monga kwalembedwa kuti,

“Palibe munthu wolungama, inde palibe ndi mmodzi yemwe.
11     Palibe ndi mmodzi yemwe amene amazindikira,
    palibe amene amafunafuna Mulungu.
12 Onse apatukira kumbali,
    onse pamodzi asanduka opandapake.
Palibe ndi mmodzi yemwe amene amachita zabwino,
    palibe ngakhale mmodzi.”
13 “Kummero kwawo kuli ngati manda apululu;
    ndi lilime lawo amayankhula zachinyengo.”
“Ululu wa mamba uli pa milomo yawo.”
14     “Mʼkamwa mwawo ndi modzaza ndi zotemberera ndi mawu owawa.”
15 “Mapazi awo afulumira kukakhetsa magazi.
16     Kusakaza ndi chisoni kumaonekera mʼnjira zawo,
17 ndipo njira ya mtendere sayidziwa.”
18     “Saopa Mulungu ndi pangʼono pomwe.”

19 Tsopano tikudziwa kuti chilichonse Malamulo amanena, amanena kwa amene amalamulidwa ndi Malamulowo, ndi cholinga chakuti aliyense asowe chonena, ndipo dziko lonse lidzayimbidwa mlandu ndi Mulungu. 20 Chifukwa chake palibe mmodzi amene adzayesedwa wolungama pamaso pake chifukwa chosunga Malamulo, kuti ife timazindikira tchimo kupyolera mu Malamulo.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.