Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Chenjezo Pomwe Tikana Nzeru
20 Nzeru ikufuwula mu msewu,
ikuyankhula mokweza mawu mʼmisika;
21 ikufuwula pa mphambano ya misewu,
ikuyankhula pa zipata za mzinda kuti,
22 “Kodi inu anthu osachangamukanu, mudzakondwera ndi kusachangamuka mpaka liti?
Nanga anthu onyogodola adzakondabe kunyogodola mpaka liti?
Kapena opusa adzadana ndi nzeru mpaka liti?
23 Tamverani mawu anga a chidzudzulo.
Ine ndikukuwuzani maganizo anga
ndi kukudziwitsani mawu anga.
24 Popeza ndinakuyitanani koma inu munakana kumvera.
Ndinayesa kukuthandizani koma panalibe amene anasamala.
25 Uphungu wanga munawunyoza.
Kudzudzula kwanga simunakusamale.
26 Ndiye inenso ndidzakusekani mukadzakhala mʼmavuto;
ndidzakunyogodolani chikadzakugwerani chimene mumachiopacho.
27 Chiwonongeko chikadzakugwerani ngati namondwe,
tsoka likadzakufikirani ngati kamvuluvulu,
mavuto ndi masautso akadzakugwerani.
28 “Tsono mudzandiyitana koma sindidzayankha;
mudzandifunafuna, koma simudzandipeza.
29 Popeza iwo anadana ndi chidziwitso
ndipo sanasankhe kuopa Yehova,
30 popeza iwo sanasamale malangizo anga
ndipo ananyoza chidzudzulo changa.
31 Tsono adzadya zipatso zoyenera mayendedwe awo
ndi kukhuta ndi ntchito zimene anachita kwa ena.
32 Pakuti anthu osachangamuka amaphedwa chifukwa cha kusochera kwawo,
ndipo zitsiru zimadziwononga zokha chifukwa cha mphwayi zawo.
33 Koma aliyense wondimvera adzakhala mwa bata;
adzakhala mosatekeseka posaopa chilichonse.”
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.
19 Zakumwamba zimalengeza za ulemerero wa Mulungu;
thambo limalalikira ntchito za manja ake.
2 Tsiku ndi tsiku zimayankhula mawu ambiri,
usiku ndi usiku zimaonetsa poyera nzeru.
3 Palibe kuyankhula, palibe mawu aliwonse;
liwu lawo silimveka.
4 Koma uthenga wawo umapita pa dziko lonse lapansi,
mawuwo amafika mpaka
kumalekezero a dziko lapansi.
5 Dzuwa lili ngati mkwatibwi wobwera kuchokera ku nsanja yake,
ngati katswiri wokondwerera kuthamanga pa mpikisano.
6 Limatuluka kuyambira mbali ina ya thambo
ndi kuzungulira mpaka mbali inanso;
palibe chinthu chotha kupewa kutentha kwake.
7 Lamulo la Yehova ndi langwiro,
kutsitsimutsa moyo.
Maumboni a Yehova ndi odalirika,
amapereka nzeru kwa wopanda nzeru.
8 Malangizo a Yehova ndi olungama,
amapereka chimwemwe mu mtima.
Malamulo a Yehova ndi onyezimira,
amapereka kuwala.
9 Kuopa Yehova ndiye chinthu changwiro,
chimakhala mpaka muyaya.
Maweruzo a Yehova ndi owona
ndipo onse ndi olungama;
10 ndi a mtengowapatali kuposa golide,
kuposa golide weniweni;
ndi otsekemera kuposa uchi,
kuposa uchi wochokera pa chisa chake.
11 Mtumiki wanu amachenjezedwa nawo;
powasunga pali mphotho yayikulu.
12 Ndani angathe kudziwa zolakwa zake?
Mundikhululukire zolakwa zanga zobisika.
13 Muteteze mtumiki wanunso ku machimo ochita akudziwa;
iwo asandilamulire.
Kotero ndidzakhala wosalakwa,
wopanda mlandu wa tchimo lalikulu.
14 Mawu a mʼkamwa mwanga ndi zolingalira za mu mtima mwanga
zikhale zokondweretsa pamaso panu,
Inu Yehova, Thanthwe langa ndi Mpulumutsi wanga.
Za Lilime
3 Abale anga, ambiri musakhale aphunzitsi chifukwa mumadziwa kuti aphunzitsife tidzaweruzidwa mowuma kuposa anthu ena onse. 2 Tonsefe timapunthwa mʼnjira zambiri. Ngati wina salakwa poyankhula, ameneyo ndi munthu wangwiro, wodziwa kuyangʼanira bwino thupi lake lonse.
3 Tikayika tizitsulo mʼkamwa mwa akavalo kuti atimvere, timatha kuwongolera thupi lake lonse. 4 Taonani sitima zapamadzi. Ngakhale ndi zazikulu kwambiri ndipo zimakankhidwa ndi mphepo yamphamvu, zimawongoleredwa ndi tsigiro lalingʼono kulikonse kumene woyendetsayo akufuna kupita. 5 Momwemonso, lilime ndi kachiwalo kakangʼono ka thupi koma limadzitama kuti nʼkuchita zikuluzikulu. Tangoganizirani za nkhalango yayikulu imene ingapse ndi kalawi kamoto koyamba mochepa. 6 Lilime nalonso ndi moto, dziko la zoyipa pakati pa ziwalo za thupi. Limawononga munthu yense wathunthu. Limayika zonse za moyo wake pa moto, ndipo moto wake ndi wochokera ku gehena.
7 Mitundu yonse ya nyama, ya mbalame, ya zokwawa ndi ya zolengedwa za mʼnyanja, zikuwetedwa ndipo munthu wakhala akuziweta, 8 koma palibe munthu amene angaweta lilime. Lilime ndipo silitha kupuma, ndi lodzaza ndi ululu wakupha.
9 Ndi lilime lomwelo timatamanda Ambuye ndi Atate athu, komanso ndi lilime lomwelo timalalatira anthu, amene anapangidwa mʼchifanizo cha Mulungu. 10 Mʼkamwa momwemo mutuluka matamando ndi kulalata. Abale anga, zisamatero ayi. 11 Kodi madzi abwino ndi a mchere angatuluke pa kasupe mmodzi? 12 Abale anga, kodi mtengo wa mkuyu nʼkubala mphesa, kapena mtengo wampesa nʼkubala nkhuyu? Kasupe wa madzi a mchere sangatulutsenso madzi abwino.
Petro Avomereza Khristu
27 Yesu ndi ophunzira ake anapita ku midzi yozungulira Kaisareya wa Filipo. Ali panjira, Iye anawafunsa kuti, “Kodi anthu amati ndine yani?”
28 Iwo anayankha kuti, “Ena amati Yohane Mʼbatizi; ena amati Eliya; ndipo enanso amati ndinu mmodzi wa aneneri.”
29 Iye anafunsa kuti, “Koma nanga inu, mumati ndine yani?”
Petro anayankha kuti, “Inu ndinu Khristu.”
30 Yesu anawachenjeza kuti asawuze wina aliyense za Iye.
Yesu Aneneratu za Imfa Yake
31 Iye anayamba kuwaphunzitsa kuti, “Mwana wa Munthu ayenera kumva zowawa zambiri ndi kukanidwa ndi akulu a ansembe, ndi aphunzitsi a malamulo, ndi kuti ayenera kuphedwa ndipo patatha masiku atatu adzaukanso.” 32 Izi anaziyankhula momveka bwino, ndipo Petro anamutengera pambali ndipo anayamba kumudzudzula.
33 Koma Yesu atatembenuka ndi kuyangʼana ophunzira ake, anamudzudzula Petro nati, “Choka pamaso panga Satana! Suganizira zinthu za Mulungu koma za anthu.”
Njira ya Mtanda
34 Kenaka anayitana gulu la anthu pamodzi ndi ophunzira ake nati: “Ngati wina aliyense afuna kunditsata Ine, ayenera kudzikana yekha ndi kunyamula mtanda wake ndi kunditsata. 35 Pakuti aliyense amene afuna kupulumutsa moyo wake adzawutaya, koma aliyense amene ataya moyo wake chifukwa cha Ine ndi cha Uthenga Wabwino, adzawupulumutsa. 36 Kodi munthu adzapindulanji akalandira dziko lonse lapansi, koma ndi kutaya moyo wake? 37 Kapena nʼchiyani chomwe munthu angapereke chosinthana ndi moyo wake? 38 Ngati wina achita manyazi chifukwa cha Ine ndi mawu anga mu mʼbado uno wachigololo ndi wochimwa, Mwana wa Munthu adzachita naye manyazi pamene adzabwera mu ulemerero wa Atate ake pamodzi ndi angelo oyera.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.