Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 144:9-15

Ndidzakuyimbirani nyimbo yatsopano Inu Mulungu;
    ndidzakuyimbirani nyimbo pa zeze wa nsambo khumi,
10 kwa Iye amene amapambanitsa mafumu,
    amene amapulumutsa Davide mtumiki wake ku lupanga loopsa.

11 Landitseni ndi kundipulumutsa,
    mʼmanja mwa anthu achilendo,
amene pakamwa pawo ndi podzaza ndi mabodza,
    amene dzanja lawo lamanja ndi lachinyengo.

12 Ndipo ana aamuna pa chinyamata chawo
    adzakhala ngati mbewu yosamalidwa bwino,
ana athu aakazi adzakhala ngati zipilala
    zosemedwa bwino, zokongoletsera nyumba yaufumu.
13 Nkhokwe zathu zidzakhala zodzaza
    ndi zokolola za mtundu uliwonse.
Nkhosa zathu zidzaswana miyandamiyanda
    pa mabusa athu.
14     Ngʼombe zathu zidzanyamula katundu wolemera.
Sipadzakhala mingʼalu pa makoma,
    sipadzakhalanso kupita ku ukapolo,
    mʼmisewu mwathu simudzakhala kulira chifukwa cha mavuto.

15 Odala anthu amene adzalandira madalitso awa;
    odala anthu amene Mulungu wawo ndi Yehova.

Nyimbo ya Solomoni 8:5-7

Abwenzi

Kodi ndani uyo akutuluka ku chipululuyo,
    atatsamira wokondedwa wakeyo?

Mkazi

Ndinakudzutsa pa tsinde pa mtengo wa apulosi,
    pamenepo ndi pamene amayi anachirira,
    pamenepo ndi pamene wokubereka anamva ululu pokubala iweyo.
Undiyike pamtima pako ngati chidindo,
    ngati chidindo cha pa dzanja lako;
pakuti chikondi nʼchamphamvu ngati imfa,
    nsanje ndiyaliwuma ngati manda.
Chikondi chimachita kuti lawilawi
    ngati malawi a moto wamphamvu.
Madzi ochuluka sangachizimitse chikondi,
    mitsinje singachikokolole chikondicho.
Ngati wina apereka chuma chonse
    cha mʼnyumba mwake chifukwa cha chikondi,
    adzangonyozeka nazo kotheratu.

Marko 7:9-23

Ndipo anawawuzanso kuti, “Inu muli ndi njira yabwino yokankhira kumbali malamulo a Mulungu kuti mukatsatire miyambo yanuyo! 10 Pakuti Mose anati, ‘Lemekeza abambo ako ndi amayi ako,’ ndipo, ‘aliyense amene atemberera abambo ake kapena amayi ake ayenera kuphedwa.’ 11 Koma inu mumati, ngati munthu anena kwa abambo ake kapena amayi ake kuti, ‘Thandizo lililonse mukanayenera kulandira kuchokera kwa ine ndi Korobani’ (kutanthauza kuti, mphatso yoperekedwa kwa Mulungu), 12 pamenepo inu simumalola kuti achitire kanthu kalikonse abambo kapena amayi ake. 13 Potero mumachepetsa mawu a Mulungu kukhala wopanda mphamvu ndi miyambo yanu imene mumapatsirana. Ndipo mumachita zinthu zina zambiri monga zimenezi.”

14 Yesu anayitananso gulu la anthu ndipo anati, “Tandimverani nonsenu, ndipo zindikirani izi. 15 Palibe kanthu kunja kwa munthu kamene kakalowa mwa iye kangamusandutse wodetsedwa. Koma zimene zituluka mwa munthu ndizo zimupanga kukhala wodetsedwa.” 16 (Ngati wina ali ndi makutu akumva amve).

17 Atalisiya gulu la anthu ndi kulowa mʼnyumba, ophunzira ake anamufunsa za fanizoli 18 Iye anawafunsa kuti, “Kodi nanunso simumvetsetsa? Kodi simukuona kuti palibe kanthu kamene kakalowa mwa munthu kochokera kunja kakhoza kumudetsa? 19 Pakuti sikalowa mu mtima wake koma mʼmimba mwake, ndipo kenaka kamatuluka kunja.” (Ndi mawu amenewa, Yesu anayeretsa zakudya zonse).

20 Anapitiriza kuti, “Chimene chichokera mwa munthu ndi chomwe chimamudetsa. 21 Pakuti kuchokera mʼkati mwa mitima ya anthu, mumatuluka maganizo oyipa, chiwerewere, kuba, kupha, chigololo, 22 dyera, nkhwidzi, chinyengo, machitidwe onyansa, kaduka, chipongwe, kudzikuza ndi kupusa. 23 Zoyipa zonsezi zimatuluka mʼkati ndipo zimadetsa munthu.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.