Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 84

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a Gititi. Salimo la ana a Kora.

84 Malo anu okhalamo ndi okomadi,
    Inu Yehova Wamphamvuzonse!
Moyo wanga ukulakalaka, mpaka kukomoka,
    kufuna mabwalo a Yehova;
Mtima wanga ndi thupi langa zikufuwulira
    Mulungu wamoyo.

Ngakhale timba wapeza nyumba yokhalamo,
    ndiponso namzeze wadzipezera yekha chisa,
    kumene amagonekako ana ake
pafupi ndi guwa lanu la nsembe,
    Inu Yehova Wamphamvuzonse, Mfumu yanga ndi Mulungu wanga.
Odala amene amakhala mʼNyumba yanu;
    nthawi zonse amakutamandani.
            Sela

Odala amene mphamvu yawo ili mwa Inu,
    mitima yawo ikufunitsitsa kuyenda mʼmisewu yopita ku Ziyoni.
Pamene akudutsa chigwa cha Baka,
    amachisandutsa malo a akasupe;
    mvula ya chizimalupsa imadzazanso mayiwe ake.
Iwo amanka nakulirakulira mphamvu
    mpaka aliyense ataonekera pamaso pa Mulungu mu Ziyoni.

Imvani pemphero langa, Inu Yehova Mulungu Wamphamvuzonse;
    mvereni Inu Mulungu wa Yakobo.
            Sela
Yangʼanani chishango chathu, Inu Mulungu;
    yangʼanani mokoma mtima pa wodzozedwa wanu.

10 Nʼkwabwino kukhala mʼmabwalo anu tsiku limodzi
    kuposa kukhala kwina kwake kwa zaka 1,000;
Ine ndingakonde kukhala mlonda wa pa khomo la Nyumba ya Mulungu wanga
    kuposa kukhala mʼmatenti a anthu oyipa.
11 Pakuti Yehova Mulungu ndi dzuwa ndi chishango;
    Yehova amapereka chisomo ndi ulemu;
Iye sawamana zinthu zabwino
    iwo amene amayenda mwangwiro.

12 Inu Yehova Wamphamvuzonse,
    wodala ndi munthu amene amakhulupirira Inu.

1 Mafumu 5:1-12

Kukonzekera Kumanga Nyumba ya Mulungu

Hiramu mfumu ya ku Turo atamva kuti Solomoni wadzozedwa kukhala mfumu mʼmalo mwa abambo ake Davide, anatumiza akazembe ake kwa Solomoni, chifukwa mfumu Hiramu inali pa ubale wabwino ndi Davide nthawi zonse. Solomoni anabweza mawu awa kwa Hiramu:

“Inu mukudziwa kuti chifukwa cha nkhondo zimene zinkachokera ku mbali zonse kulimbana ndi abambo anga, iwo sanathe kumangira Nyumba Yehova Mulungu wawo, mpaka Yehova atawayika adani awo pansi pa ulamuliro wawo. Koma tsopano Yehova Mulungu wanga wandipatsa mtendere mbali zonse za dziko ndipo ndilibe mdani kapena chovuta chilichonse. Choncho ine ndikufuna kumangira nyumba Yehova Mulungu wanga, monga momwe Iye anawuzira abambo anga Davide kuti, ‘Mwana wako amene ndidzamukhazike pa mpando waufumu mʼmalo mwako ndiye adzandimangire Nyumba.’

“Choncho lamulani kuti andidulire mikungudza ya ku Lebanoni. Anthu anga adzagwira ntchito imeneyo pamodzi ndi anthu anuwo, ndipo ine ndidzalipira anthu anuwo malipiro amene inu mungakhazikitse. Inu mukudziwa kuti ife tilibe anthu aluso locheka matabwa monga Asidoni.”

Hiramu anakondwa kwambiri atamva uthenga wa Solomoni ndipo anati, “Lero Yehova atamandike chifukwa wapatsa Davide mwana wanzeru kuti alamulire mtundu waukuluwu.”

Tsono Hiramu anabweza mawu awa kwa Solomoni:

“Ndalandira uthenga umene mwanditumizira ndipo ine ndidzachita zonse zimene mukufuna pokupatsani mitengo ya mkungudza ndi payini. Anthu anga adzatsika nayo kuchokera ku Lebanoni mpaka ku nyanja, ndipo adzayiyandamitsa pa nyanja mpaka ku malo amene munene. Kumeneko ndidzayimasula ndipo mudzayitenga. Ndipo inu mudzakwaniritsa chokhumba changa pondipatsa chakudya cha banja langa laufumu.”

10 Motero Hiramu anapereka kwa Solomoni mitengo yonse ya mkungudza ndi payini imene ankayifuna, 11 ndipo Solomoni anamupatsa Hiramu mitanga ya tirigu 20,000 ngati chakudya cha pa nyumba yake, kuwonjezera pa migolo ya mafuta a olivi yokwana 20,000. Solomoni anapitiriza kupereka zimenezi chaka ndi chaka. 12 Yehova anamupatsa Solomoni nzeru monga momwe analonjezera. Panali ubale wa mtendere pakati pa Solomoni ndi Hiramu, ndipo awiriwa anachita pangano.

Luka 11:5-13

Kenaka anawawuza kuti, “Tiyerekeze: Mmodzi mwa inu atakhala ndi bwenzi lake, ndipo iye nʼkupita ku nyumba yake pakati pa usiku, nakanena kuti, ‘Mnzanga, bwereke malofu atatu abuledi, chifukwa ndalandira bwenzi langa amene ali pa ulendo ndipo ine ndilibe choti ndimupatse.’

“Ndipo yerekezani kuti amene ali mʼnyumbamo ndi kuyankha kuti, ‘Usandivutitse ine, ndatseka kale chitseko, ndipo ine ndi ana anga tagona. Ine sindingadzukenso kuti ndidzakupatse.’ Ine ndikukuwuzani kuti adzadzuka ndi kumupatsa bulediyo, osati chifukwa ndi bwenzi lake, koma chifukwa cha liwuma la munthu wopemphayo, ndipo kudzamupatsa zonse zimene akuzifuna.

“Choncho Ine ndikunena kwa inu kuti: Pemphani ndipo adzakupatsani. Funafunani ndipo mudzapeza. Gogodani ndipo adzakutsekulirani. 10 Pakuti aliyense amene amapempha amalandira. Munthu amene amafunafuna amapeza. Iye amene amagogoda amamutsekulira.

11 “Ndani mwa inu abambo, kodi mwana wanu atapempha nsomba, mʼmalo mwake mungamupatse njoka? 12 Kapena atapempha dzira, kodi mungamupatse chinkhanira? 13 Tsono ngati inu, anthu oyipa, mumadziwa kupereka mphatso zabwino kwa ana anu, koposa kotani Atate anu akumwamba, angalephere bwanji kupereka Mzimu Woyera kwa amene awapempha!”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.