Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 101

Salimo la Davide.

101 Ndidzayimba za chikondi ndi chiweruzo chanu cholungama;
    kwa Inu Yehova ndidzayimba matamando.
Ndidzatsata njira yolungama;
    nanga mudzabwera liti kwa ine?

Ndidzayenda mʼnyumba mwanga
    ndi mtima wosalakwa.
Sindidzayika chinthu chilichonse choyipa
    pamaso panga.

Ine ndimadana ndi zochita za anthu opanda chikhulupiriro;
    iwo sadzadziphatika kwa ine.
Anthu a mtima wokhota adzakhala kutali ndi ine;
    ine sindidzalola choyipa chilichonse kulowa mwa ine.

Aliyense wosinjirira mnansi wake mseri
    ameneyo ndidzamuletsa;
aliyense amene ali ndi maso amwano ndi mtima wodzikuza,
    ameneyo sindidzamulekerera.

Maso anga adzakhala pa okhulupirika mʼdziko,
    kuti akhale pamodzi ndi ine;
iye amene mayendedwe ake ndi wosalakwa
    adzanditumikira.

Aliyense wochita chinyengo
    sadzakhala mʼnyumba mwanga.
Aliyense woyankhula mwachinyengo
    sadzayima pamaso panga.

Mmawa uliwonse ndidzatontholetsa anthu
    onse oyipa mʼdziko;
ndidzachotsa aliyense wochita zoyipa
    mu mzinda wa Yehova.

1 Mafumu 3:16-28

Kuweruza Kolungama

16 Nthawi ina amayi awiri adama anabwera kwa mfumu ndipo anayima pamaso pake. 17 Mmodzi mwa amayiwo anati, “Mbuye wanga, mayi uyu ndi ine timakhala nyumba imodzi. Ine ndinabala mwana tili limodzi ndi mnzangayu. 18 Tsiku lachitatu ine nditabala mwana, mnzangayunso anabereka mwana wake. Tinalipo awiriwiri mʼnyumbamo ndipo munalibe wina aliyense.

19 “Nthawi ya usiku mwana wa mnzangayu anafa chifukwa anamugonera. 20 Tsono iyeyu anadzuka pakati pa usiku, natenga mwana wanga ku mimba kwanga pamene ine mdzakazi wanu ndinali mʼtulo. Anamuyika mwanayo ku mimba kwake ndi kuyika mwana wake wakufayo ku mimba kwanga. 21 Mmawa nditadzuka kuti ndiyamwitse mwana wanga ndinapeza kuti ndi wakufa! Koma kutacha nditamuyangʼanitsitsa ndinaona kuti si mwana amene ine ndinabala.”

22 Koma mayi winayo anati, “Ayi! Mwana wamoyoyu ndi wanga, mwana wakufayu ndi wako.”

Koma mayi woyambayo analimbikira kuti. “Ayi! Mwana wakufayu ndi wako; wamoyoyu ndi wanga.” Motero akaziwa anatsutsana pamaso pa mfumu.

23 Pamenepo mfumu inati, “Wina akuti, ‘Mwana wanga ndi wamoyoyu ndipo mwana wako ndi wakufayu,’ pamene winanso akuti, ‘Ayi! Mwana wako ndi wakufayu wanga ndi wamoyoyu.’ ”

24 Pamenepo mfumu inati, “Patseni lupanga.” Ndipo anabwera nalo lupanga kwa mfumu. 25 Tsono mfumu inagamula kuti, “Muduleni pakati mwana wamoyoyu ndipo wina mumupatse gawo limodzi, gawo linalo mumupatse winayo.”

26 Mayi amene mwana wake anali moyo anagwidwa ndi chisoni chifukwa cha mwana wakeyo ndipo anawuza mfumu kuti, “Chonde mbuye wanga, mupatseni mnzangayu mwana wamoyoyu! Musamuphe!”

Koma winayo anati, “Ayi, asandipatse ine kapena iwe. Muduleni pakati!”

27 Choncho mfumu inagamula kuti, “Perekani mwana wamoyoyu kwa mayi woyambayu. Musamuphe, iyeyu ndiye mayi wake wa mwanayu.”

28 Pamene Aisraeli onse anamva za chigamulo chimene mfumu inapereka, anaopa mfumuyo kwambiri, chifukwa anaona kuti mfumu inali ndi nzeru zochokera kwa Mulungu zoweruzira mwachilungamo.

Machitidwe a Atumwi 6:1-7

Asankha Atumiki Asanu ndi Awiri

Mʼmasiku amenewo pamene chiwerengero cha ophunzira chinkachuluka, Ayuda a Chihelene pakati pawo anadandaula chifukwa cha Ayuda a Chihebri chifukwa amasiye awo samawagawira chakudya cha tsiku ndi tsiku. Tsono Atumwi khumi ndi awiriwo anasonkhanitsa ophunzira onse pamodzi ndipo anati, “Nʼkosayenera kuti ife tisiye kulalikira Mawu a Mulungu ndi kuyangʼanira za chakudya. Choncho abale, sankhani pakati panu anthu asanu ndi awiri a mbiri yabwino, odzazidwa ndi Mzimu Woyera ndi anzeru. Ife tidzawapatsa udindo oyangʼanira. Koma ife tidzadzipereka kuti tizipemphera ndi kulalikira mawu.”

Mawu amenewa anakondweretsa gulu lonse la anthu. Iwo anasankha, Stefano, munthu wodzazidwa ndi chikhulupiriro ndiponso Mzimu Woyera; anasankhanso Filipo, Prokoro, Nikanora, Timo, Parmena ndi Nikolao amene anatembenuka mtima ndi kulowa Chiyuda kuchokera kwa Antiokeya. Iwo anapereka anthuwa kwa atumwi amene anawapempherera ndi kuwasanjika manja.

Ndipo Mawu a Mulungu anapitirira kufalikira. Chiwerengero cha ophunzira mu Yerusalemu chinakula mofulumira ndipo ansembe ochuluka anakhulupirira.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.