Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 111

111 Tamandani Yehova.

Ndidzathokoza Yehova ndi mtima wanga wonse
    mʼbwalo la anthu olungama mtima ndi pa msonkhano.

Ntchito za Yehova nʼzazikulu;
    onse amene amakondwera nazo amazilingalira.
Zochita zake ndi za ulemerero ndi zaufumu,
    ndipo chilungamo chake ndi chosatha.
Iye wachititsa kuti zodabwitsa zake zikumbukirike;
    Yehova ndi wokoma mtima ndi wachifundo.
Amapereka chakudya kwa amene amamuopa Iye;
    amakumbukira pangano lake kwamuyaya.
Waonetsa anthu ake mphamvu ya ntchito zake,
    kuwapatsa mayiko a anthu a mitundu ina.
Ntchito za manja ake ndi zokhulupirika ndi zolungama;
    malangizo ake onse ndi odalirika.
Malamulo ndi okhazikika ku nthawi za nthawi,
    ochitidwa mokhulupirika ndi molungama.
Iyeyo amawombola anthu ake;
    anakhazikitsa pangano lake kwamuyaya
    dzina lake ndi loyera ndi loopsa.

10 Kuopa Yehova ndicho chiyambi cha nzeru;
    onse amene amatsatira malangizo ake amamvetsa bwino zinthu.
    Iye ndi wotamandika mpaka muyaya.

1 Mafumu 2:1-11

Davide Alangiza Solomoni

Davide ali pafupi kumwalira, analangiza mwana wake Solomoni kuti:

“Ndatsala pangʼono kupita kumene munthu wina aliyense amayenera kupitako. Tsono khala wamphamvu, uvale zilimbe, ndipo uzichita zimene Yehova Mulungu wako amafuna, uziyenda mʼnjira zake, uzisunga malangizo ndi malamulo ake monga momwe zinalembedwera mʼMalamulo a Mose, kuti zonse zimene udzachite zidzakuyendere bwino kulikonse kumene udzapite. Ndipo Yehova akwaniritse zimene anandilonjeza kuti, ‘Ngati zidzukulu zako zidzakhala mosamala, niziyenda mokhulupirika pamaso panga ndi mtima wawo wonse ndi moyo wawo wonse, sudzasowa munthu wokhala pa mpando waufumu wa Israeli.’

“Tsono iwe ukudziwanso zoyipa zimene Yowabu mwana wa Zeruya anandichitira pakupha atsogoleri awiri a ankhondo a Israeli, Abineri mwana wa Neri ndi Amasa mwana wa Yeteri. Iye anawapha ndi kukhetsa magazi nthawi ya mtendere ngati nthawi ya nkhondo, ndipo anapaka magazi amenewo pa lamba wa mʼchiwuno mwake ndi pa nsapato za ku mapazi ake. Iwe uchite kwa iye molingana ndi nzeru zako, koma usalole kuti afe ndi ukalamba ndi kupita ku manda mwamtendere.

“Koma ana a Barizilai wa ku Giliyadi uwakomere mtima ndipo uwalole kuti akhale mʼgulu la anthu amene azidya pamodzi nawe. Pakuti anandisamalira pamene ndinkathawa mʼbale wako Abisalomu.

“Ndipo kumbukira kuti uli ndi Simei mwana wa Gera, wa fuko la Benjamini wochokera ku Bahurimu, amene ananditemberera koopsa tsiku limene ndimapita ku Mahanaimu. Atabwera kudzakumana nane ku Yorodani, ine ndinalumbira mʼdzina la Yehova kuti, ‘Sindidzakupha iwe ndi lupanga.’ Koma tsopano usamuyese ngati munthu wosalakwa. Iwe ndiwe munthu wanzeru. Udzadziwa choti uchite naye. Ngakhale ndi wokalamba, aphedwe ndithu.”

10 Tsono Davide anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda mu Mzinda wa Davide. 11 Iyeyo nʼkuti atalamulira Israeli kwa zaka makumi anayi. Ku Hebroni analamulira zaka zisanu ndi ziwiri ndipo ku Yerusalemu analamulira zaka 33.

Yohane 4:7-26

Mayi wa Chisamariya atabwera kudzatunga madzi, Yesu anati kwa iye, “Kodi ungandipatse madzi akumwa.” (Ophunzira ake nʼkuti atapita mʼmudzi kukagula chakudya).

Mayiyo anati kwa Iye, “Inu ndinu Myuda ndipo ine ndine Msamariya. Bwanji mukundipempha madzi akumwa?” (Popeza Ayuda ndi Asamariya sankayanjana).

10 Yesu anamuyankha kuti, “Koma iwe ukanadziwa mphatso ya Mulungu ndi Iye amene akukupempha madzi akumwa, ukanamupempha ndipo akanakupatsa madzi amoyo.”

11 Mayiyo anati, “Ambuye, Inu mulibe kanthu kotungira madzi ndipo chitsime ndi chakuya. Kodi madzi amoyowo mungawatenge kuti? 12 Kodi Inu ndinu wamkulu kuposa kholo lathu Yakobo, amene anatipatsa chitsimechi ndipo iye ankamwanso monga anachita ana ake ndi ziweto zake?”

13 Yesu anayankha kuti, “Aliyense amene amamwa madzi awa amamvanso ludzu, 14 koma aliyense amene adzamwa madzi amene Ine ndidzamupatsa sadzamvanso ludzu. Ndithudi, madzi amene ndidzamupatsa adzakhala kasupe wamadzi wotumphukira ku moyo wosatha.”

15 Mayiyo anati kwa Iye, “Ambuye, patseni madzi amenewo kuti ndisadzamvenso ludzu ndi kumabwerabe kuno kudzatunga madzi.”

16 Iye anamuwuza kuti, “Pita kayitane mwamuna wako ndipo ubwere naye.”

17 Iye anayankha kuti, “Ine ndilibe mwamuna.”

Yesu anati kwa iye, “Wakhoza ponena kuti ulibe mwamuna. 18 Zoona nʼzakuti iwe wakhala pa banja ndi amuna asanu, ndipo mwamuna amene uli naye tsopano si wako. Zimene wanenazi ndi zoona.”

19 Mayiyo anati, “Ambuye, ine ndazindikira kuti Inu ndinu mneneri. 20 Makolo athu ankapembedza mʼphiri ili koma inu Ayuda mumati malo amene tiyenera kupembedzera ali ku Yerusalemu.”

21 Yesu anati, “Mayi inu khulupirira Ine. Nthawi ikubwera pamene inu simudzapembedza Atate mʼphiri ili kapena mu Yerusalemu. 22 Inu Asamariya mumapembedza chimene simukuchidziwa. Ife timapembedza chimene tikuchidziwa, pakuti chipulumutso nʼchochokera kwa Ayuda. 23 Koma nthawi ikubwera ndipo yafika kale tsopano pamene opembedza woona adzapembedza Atate mu mzimu ndi mʼchoonadi, pakuti opembedza otere ndiwo amene Atate akuwafuna. 24 Mulungu ndi Mzimu, ndipo omupembedza Iye ayenera kumupembedza mu mzimu ndi mʼchoonadi.”

25 Mayiyo anati, “Ine ndikudziwa kuti Mesiya (wotchedwa Khristu) akubwera. Akabwera, Iye adzafotokoza zonse kwa ife.”

26 Ndipo Yesu anamuwuza kuti, “Amene ndikukuyankhulane, ndine amene.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.