Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a “Musawononge.” Ndakatulo ya Davide, pamene anathawa Sauli kupita ku phanga.
57 Mundichitire chifundo, Inu Mulungu mundichitire chifundo,
pakuti mwa Inu moyo wanga umathawiramo.
Ndidzathawira mu mthunzi wa mapiko anu
mpaka chiwonongeko chitapita.
2 Ine ndikufuwulira kwa Mulungu Wammwambamwamba,
kwa Mulungu amene amakwaniritsa cholinga chake pa ine.
3 Mulungu amanditumizira kuchokera kumwamba ndi kundipulumutsa,
kudzudzula iwo amene akundithamangitsa kwambiri.
Mulungu amatumiza chikondi chake ndi kukhulupirika kwake.
4 Ine ndili pakati pa mikango,
ndagona pakati pa zirombo zolusa;
anthu amene mano awo ndi milomo yawo ndi mivi,
malilime awo ndi malupanga akuthwa.
5 Mukwezekedwe Inu Mulungu, kuposa mayiko onse akumwamba;
mulole kuti ulemerero wanu ukhale pa dziko lonse lapansi.
6 Iwo anatchera mapazi anga ukonde
ndipo ndinawerama pansi mosautsidwa.
Anakumba dzenje mʼnjira yanga
koma agweramo okha mʼmenemo.
7 Mtima wanga ndi wokhazikika, Inu Mulungu
mtima wanga ndi wokhazikika.
Ndidzayimba nyimbo, nyimbo yake yamatamando.
8 Dzuka moyo wanga!
Dzukani zeze ndi pangwe!
Ndidzadzuka mʼbandakucha.
9 Ndidzakutamandani Ambuye, pakati pa mitundu ya anthu,
ndidzayimba za Inu pakati pa mayiko.
10 Pakuti chikondi chanu nʼchachikulu, kufikira ku mayiko akumwamba;
kukhulupirika kwanu kwafika ku mitambo.
11 Mukwezekedwe Inu Mulungu kuposa mayiko akumwamba,
mulole kuti ulemerero wanu ukhale pa dziko lonse lapansi.
Davide Alira Abisalomu
19 Tsono Ahimaazi mwana wa Zadoki anati, “Ndiloleni ndithamange ndi kukapereka uthenga kwa mfumu kuti Yehova wayipulumutsa mʼdzanja la adani ake.”
20 Yowabu anamuwuza iye kuti, “Iwe si amene uti ukanene zimenezi lero. Ukapereka uthenga nthawi ina, koma usatero lero, chifukwa mwana wa mfumu wafa.”
21 Kenaka Yowabu anawuza Mkusi kuti, “Pita ukawuze mfumu zimene waona.” Mkusiyo anawerama pamaso pa Yowabu ndipo anathamanga kupita.
22 Ahimaazi mwana wa Zadoki ananenanso kwa Yowabu kuti, “Zivute zitani, chonde mundilole kuti ndipite pambuyo pa Mkusiyo.”
Koma Yowabu anayankha kuti, “Mwana wanga, nʼchifukwa chiyani ukufuna kupita? Ulibe nkhani yoti ukalandire nayo mphotho.”
23 Iye anati, “Zivute zitani ine ndikufuna kuti ndipite.”
Choncho Yowabu anati “Pita!” Ndipo Ahimaazi anathamanga kudzera njira ya ku chigwa ndipo anamupitirira Mkusi uja.
24 Nthawi imeneyo nʼkuti Davide atakhala pakati pa zipata ziwiri, chakubwalo ndi chamʼkati. Mlonda anakwera pa khoma nakayimirira pa denga la chipata. Anati atayangʼana, anaona munthu akuthamanga yekhayekha. 25 Mlonda uja anapita kwa mfumu ndipo anafotokoza.
Mfumu inati, “Ngati ali yekha ali ndi nkhani yabwino” Ndipo munthuyo anayandikira.
26 Mlonda uja anaonanso munthu wina akuthamanga, ndipo anayitana woyangʼanira pa chipata, “Taona, munthu winanso akuthamanga ali yekha!”
Mfumu inati, “Iye akubweretsanso nkhani yabwino.”
27 Mlonda uja anati, “Munthu akuthamanga patsogoloyo, kathamangidwe kake kakufanafana ndi mmene amathamangira Ahimaazi, mwana wa Zadoki.”
Mfumu inati, “Ameneyo ndi munthu wabwino, ndipo akubwera ndi nkhani yabwino.”
28 Ndipo Ahimaazi anafuwula kwa mfumu, “Zonse zili bwino!” Iye anagwada pamaso pa mfumu nkhope yake atagunditsa pansi ndipo anati, “Yehova Mulungu wathu alemekezedwe! Iye wapereka mʼdzanja lathu anthu amene anawukira inu mbuye wanga mfumu.”
29 Mfumu inafunsa, “Kodi mnyamata uja Abisalomu watetezedwa?”
Ahimaazi anayankha, “Pamene Yowabu amati azindituma ine mtumiki wanu ndinaona chipiringu cha anthu, koma sindikudziwa chinali chiyani.”
30 Mfumu inati, “Ima apo ndipo udikire.” Kotero iye anapita pa mbali nayima pamenepo.
31 Kenaka Mkusi uja anafika ndipo anati, “Mbuye wanga mfumu imvani nkhani yabwino! Yehova wakupulumutsani inu lero kwa onse amene anakuwukirani.”
32 Mfumu inafunsa Mkusiyo kuti, “Kodi mnyamata uja Abisalomu watetezedwa?”
Mkusiyo anayankha kuti, “Adani anu mbuye wanga mfumu, pamodzi ndi anthu onse amene amakuwukirani, ziwaonekere zomwe zamuonekera mnyamatayo.”
33 Mfumu inanthunthumira. Inapita ku chipinda cha mmwamba cha pa chipata kukalira. Pamene imapita, inkati: “Iwe mwana wanga Abisalomu! Mwana wanga! Mwana wanga Abisalomu! Zikanakhala bwino ndikanafa ndine mʼmalo mwako! Iwe Abisalomu, mwana wanga, mwana wanga!”
14 Chomwecho okondedwa, popeza inu mukudikira zimenezi, chitani changu kuti mukhale wopanda chilema kuti mukhale pa mtendere ndi Iye. 15 Zindikirani kuti kuleza mtima kwa Ambuye kukutanthauza chipulumutso, monga momwe mʼbale wathu wokondedwa Paulo anakulemberaninso ndi nzeru zimene Mulungu anamupatsa. 16 Iye walemba chimodzimodzi makalata ake onse, kuyankhula za zinthu izi. Mʼmakalata ake mumakhala zinthu zina zovuta kuzimvetsa, zimene anthu osadziwa ndi osakhazikika amazipotoza, monga amachita ndi malemba ena onse, potero akudziwononga okha.
17 Nʼchifukwa chake, abale okondedwa, popeza mukuzidziwa kale zimenezi, chenjerani kuti musatengeke ndi zolakwa za anthu osaweruzika, mungagwe ndi kuchoka pamalo otetezedwa. 18 Koma kulani mu chisomo ndi mʼchidziwitso cha Ambuye ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu. Kwa Iye kukhale ulemerero tsopano mpaka muyaya. Ameni.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.