Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 61

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Loyimbidwa ndi zipangizo za zingwe.

61 Imvani kulira kwanga, Inu Mulungu;
    mvetserani pemphero langa.

Kuchokera ku malekezero a dziko lapansi ine ndimayitana Inu
    ndimayitana pomwe mtima wanga ukufowoka;
    tsogolereni ku thanthwe lalitali kuposa ineyo.
Pakuti Inu mwakhala pothawirapo panga,
    nsanja yolimba polimbana ndi adani anga.

Ine ndikulakalaka kukhala mʼtenti yanu kwamuyaya
    ndi kupeza chitetezo mu mthunzi wa mapiko anu.
Pakuti Inu Mulungu mwamva malumbiro anga;
    mwandipatsa cholowa cha iwo amene amaopa dzina lanu.

Wonjezerani masiku a moyo wa mfumu,
    zaka zake kwa mibado yochuluka.
Iye akhale pa mpando waufumu pamaso pa Mulungu kwamuyaya;
    ikani chikondi chanu ndi kukhulupirika kwanu kuti zimuteteze.

Kotero ndidzayimba matamando kwamuyaya pa dzina lanu
    ndi kukwaniritsa malumbiro anga tsiku ndi tsiku.

2 Samueli 8

Kupambana kwa Davide pa Nkhondo

Patapita nthawi, Davide anagonjetsa Afilisti ndi kuwapambana ndipo analanda Metegi Ama kuchoka mʼmanja mwa Afilistiwo.

Davide anagonjetsanso Amowabu. Iye anawalamula kuti agone pansi mʼmizere itatu pa gulu lililonse ndipo anawayeza ndi chingwe. Pa gulu lililonse ankapha anthu amene anali pa mizere iwiri yoyamba, kusiyapo mzere wachitatu. Kotero Amowabu anakhala pansi pa ulamuliro wa Davide ndipo ankapereka msonkho.

Komanso Davide anagonjetsa Hadadezeri mwana wa Rehobu, mfumu ya Zoba, pamene anapita kukakhazikitsa ulamuliro wake mʼmbali mwa mtsinje wa Yufurate. Davide analanda magaleta 1,000, anthu 7,000 okwera magaleta pamodzi ndi asilikali oyenda pansi 20,000. Iye anadula mitsempha ya akavalo onse okoka magaleta, koma anasiyapo akavalo 100 okha.

Aramu wa ku Damasiko atabwera kudzathandiza Hadadezeri mfumu ya Zoba, Davide anakantha asilikali 22,000. Iye anakhazikitsa maboma mu ufumu wa Aramu wa ku Damasiko, ndipo Aaramu anakhala pansi pa ulamuliro wake ndipo ankapereka msonkho. Yehova ankamupatsa chipambano Davide kulikonse kumene ankapita.

Davide anatenga zishango zagolide za akuluakulu ankhondo a Hadadezeri ndi kubwera nazo ku Yerusalemu. Mfumu Davide inatenga mkuwa wambiri kuchokera ku Beta ndi Berotai, mizinda ya Hadadezeri.

Tou, mfumu ya Hamati atamva kuti Davide wagonjetsa gulu lonse lankhondo la Hadadezeri, 10 anatumiza mwana wake Yoramu kwa mfumu Davide kukamulonjera ndi kukamuyamikira chifukwa cha kupambana kwake pa nkhondo yake ndi Hadadezeriyo, amene analinso pa nkhondo ndi Tou. Yoramu anabweretsa ziwiya zasiliva, zagolide ndi zamkuwa.

11 Mfumu Davide inapereka zinthu zimenezi kwa Yehova, monga anachitira ndi siliva ndi golide zochokera ku mayiko onse amene anawagonjetsa: 12 Edomu ndi Mowabu, Aamoni ndi Afilisti, ndi Aamaleki. Iye anaperekanso zolanda ku nkhondo zochokera kwa Hadadezeri mwana wa Rehobu, mfumu ya Zoba.

13 Ndipo Davide anatchuka atabwera kokakantha Aedomu 18,000 mu Chigwa cha Mchere.

14 Iye anayika maboma mʼdera lonse la Edomu, ndipo Aedomu onse anakhala pansi pa Davide. Yehova ankapambanitsa Davide kulikonse kumene ankapita.

Akuluakulu a Davide

15 Davide analamulira dziko lonse la Israeli ndipo ankachita zonse mwachilungamo ndi molondola pamaso pa anthu ake onse. 16 Yowabu mwana wa Zeruya anali mkulu wa ankhondo; Yehosafati mwana wa Ahiludi anali mlembi wa zochitika. 17 Zadoki mwana wa Ahitubi ndi Ahimeleki mwana wa Abiatara anali ansembe; Seraya anali mlembi; 18 Benaya mwana wa Yehoyada anali mtsogoleri wa Akereti ndi Apeleti; ndipo ana a Davide anali ansembe.

Machitidwe a Atumwi 20:17-38

17 Paulo ali ku Mileto, anatumiza mawu ku Efeso kuyitana akulu ampingo. 18 Iwo atafika, Paulo anati, “Inu mukudziwa mmene ndinakhalira nanu nthawi yonse imene ndinali nanu kuyambira tsiku loyamba limene ndinafika ku Asiya. 19 Ndinatumikira Ambuye modzichepetsa kwambiri ndiponso ndi misozi, ngakhale ndinayesedwa kwambiri ndi ziwembu za Ayuda. 20 Inu mukudziwa kuti, sindinakubisireni kanthu kalikonse kopindulitsa koma ndinakuphunzitsani poyera komanso nyumba ndi nyumba. 21 Ine ndinawuza Ayuda komanso Agriki kuti ayenera kutembenukira kwa Mulungu polapa ndikuti akhulupirire Ambuye athu Yesu.

22 “Ndipo tsopano, mokakamizidwa ndi Mzimu, ndikupita ku Yerusalemu, sindikudziwa zimene zikandichitikire kumeneko.” 23 Chimene ndikudziwa ndi chakuti Mzimu Woyera wandichenjeza mu mzinda uliwonse kuti ndende ndi mavuto zikundidikira. 24 Koma sindilabadira konse za moyo wanga ngati kuti ndi wa mtengo wapatali kwa ine, malingana ndikatsirize ntchito yanga ndi utumiki umene Ambuye Yesu anandipatsa, ntchito yochitira umboni Uthenga Wabwino wachisomo cha Mulungu.

25 “Tsopano ndikudziwa kuti inu nonse amene ndinakuyenderani ndi kumakulalikirani ufumu wa Mulungu simudzaonanso nkhope yanga. 26 Chifukwa chake, ine ndikukuwuzani lero kuti ndilibe mlandu ndi munthu aliyense. 27 Pakuti sindinakubisireni pokulalikirani chifuniro chonse cha Mulungu. 28 Mudziyangʼanire nokha ndiponso muyangʼanire gulu lankhosa limene Mzimu Woyera anakuyikani kuti mukhale oyangʼanira ake. Khalani abusa a mpingo wa Mulungu umene Iye anawugula ndi magazi ake. 29 Ndikudziwa kuti ndikachoka ine, padzafika mimbulu yolusa pakati panu imene sidzalekerera gulu lankhosalo. 30 Ngakhale pakati pa inu nokha padzapezeka anthu oyankhula zonama ndi cholinga chofuna kukhala ndi ophunzira kuti awatsate. 31 Tsono inu, samalani! Kumbukirani kuti kwa zaka zitatu, usana ndi usiku ndiponso ndi misozi sindinaleke kuchenjeza aliyense wa inu.

32 “Tsopano ine ndikukuperekani kwa Mulungu ndiponso kwa mawu a chisomo chake, amene ali ndi mphamvu zokulitsa inu ndi kukupatsani chuma pakati pa onse amene anayeretsedwa. 33 Ine sindinasirire siliva kapena golide kapena zovala za munthu aliyense. 34 Inu nomwe mukudziwa kuti manja angawa ananditumikira kuti tipeze zimene ine ndi anzanga tinkazifuna. 35 Pa zonse zimene ndinachita, ndinakuonetsani kuti pogwira ntchito molimbika motere tiyenera kuthandiza ofowoka, pokumbukira mawu a Ambuye Yesu akuti, ‘Kupereka kumadalitsa kuposa kulandira.’ ”

36 Atanena zimenezi, anagwada pansi pamodzi ndi ena onse, napemphera. 37 Onse analira pamene amamukumbatira ndi kupsompsona. 38 Chimene chinamvetsa chisoni kwambiri ndi mawu ake akuti sadzaonanso nkhope yake. Kenaka iwo anamuperekeza ku sitima yapamadzi.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.