Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
24 Mayendedwe aulemu a anthu anu aonekera poyera, Inu Mulungu;
mayendedwe olemekeza Mulungu wanga ndi Mfumu yanga yokalowa mʼmalo opatulika.
25 Patsogolo pali oyimba nyimbo pakamwa, pambuyo pawo oyimba nyimbo ndi zipangizo;
pamodzi ndi iwo pali atsikana akuyimba matambolini.
26 Tamandani Mulungu mu msonkhano waukulu;
tamandani Yehova mu msonkhano wa Israeli.
27 Pali fuko lalingʼono la Benjamini, kuwatsogolera,
pali gulu lalikulu la ana a mafumu a Yuda,
ndiponso pali ana a mafumu a Zebuloni ndi Nafutali.
28 Kungani mphamvu zanu Mulungu;
tionetseni nyonga zanu, Inu Mulungu, monga munachitira poyamba.
29 Chifukwa cha Nyumba yanu ku Yerusalemu,
mafumu adzabweretsa kwa Inu mphatso.
30 Dzudzulani chirombo pakati pa mabango,
gulu la ngʼombe zazimuna pakati pa ana angʼombe a mitundu ya anthu.
Mochititsidwa manyazi, abweretse mitanda ya siliva.
Balalitsani anthu a mitundu ina amene amasangalatsidwa ndi nkhondo.
31 Nthumwi zidzachokera ku Igupto;
Kusi adzadzipereka yekha kwa Mulungu.
32 Imbirani Mulungu Inu mafumu a dziko lapansi
imbirani Ambuye matamando.
Sela
33 Kwa Iye amene amakwera pa mitambo yakalekale ya mmwamba
amene amabangula ndi mawu amphamvu.
34 Lengezani za mphamvu za Mulungu,
amene ulemerero wake uli pa Israeli
amene mphamvu zake zili mʼmitambo.
35 Ndinu woopsa, Inu Mulungu mʼmalo anu opatulika;
Mulungu wa Israeli amapereka mphamvu ndi nyonga kwa anthu ake.
Matamando akhale kwa Mulungu!
12 Kenaka Abineri anatuma amithenga kwa Davide kukanena kuti, “Kodi dzikoli ndi la yani? Uchite mgwirizano ndi ine ndipo ndidzakuthandiza kuti Aisraeli onse azikutsatira.”
13 Davide anati, “Chabwino. Ine ndichita mgwirizano ndi iwe. Koma ndikukupempha chinthu chimodzi: Usabwere pamaso panga pokhapokha utabweretsa Mikala mwana wamkazi wa Sauli, ukamabwera kudzandiona.” 14 Ndipo Davide anatuma amithenga kwa Isi-Boseti mwana wa Sauli, kumulamula kuti, “Patse mkazi wanga Mikala, amene ndinamukwatira ndi makungu 100 a msonga za mavalo a Afilisti.”
15 Kotero Isi-Boseti analamulira ndipo anakamutenga kwa mwamuna wake Palitieli mwana wa Laisi. 16 Koma mwamuna wake anapita naye akulira pambuyo pake njira yonse mpaka ku Bahurimu. Kenaka Abineri anati kwa iye, “Bwerera kwanu!” Ndipo anabwerera kwawo.
Ayuda Achita Chiwembu Paulo
12 Kutacha Ayuda ena anakonza chiwembu ndipo analumbira kuti sadya kapena kumwa mpaka atapha Paulo. 13 Anthu amene anakonza chiwembuchi analipo makumi anayi. 14 Iwo anapita kwa akulu a ansembe ndi akuluakulu a Ayuda nakawawuza kuti, “Ife talumbira kolimba kuti sitidya kalikonse mpaka titapha Paulo. 15 Tsopano inu pamodzi ndi akuluakulu a Bwalo Lalikulu mupemphe mkulu wa asilikali kuti akubweretsereni Paulo ngati kuti mukufuna kudziwa bwino za mlandu wake. Ife takonzeka kudzamupha asanafike kumeneko.”
16 Koma mwana wa mlongo wake wa Paulo atamva za chiwembuchi, anapita ku malo a asilikali aja namufotokozera Paulo.
17 Paulo anayitana mmodzi wa wolamulira asilikali 100 aja, namuwuza kuti, “Pita naye mnyamatayu kwa mkulu wa asilikali. Iyeyu ali ndi mawu oti akamuwuze.” 18 Anamutengadi mnyamatayo napita naye kwa mkulu wa asilikali uja, nati, “Wamʼndende uja Paulo anandiyitana, nandipempha kuti ndibweretse mnyamatayu kwa inu chifukwa ali ndi kanthu koti akuwuzeni.”
19 Mkulu wa asilikali uja anagwira dzanja mnyamatayo napita naye paseli ndipo anamufunsa kuti, “Kodi ukufuna kuti undiwuze chiyani?”
20 Mnyamatayo anati, “Ayuda agwirizana zoti akupempheni kuti mawa mubwere ndi Paulo ku Bwalo Lalikulu, ngati kuti akufuna kudziwa bwino za iye. 21 Inu musawamvere, chifukwa pali anthu opitirira makumi anayi amene akumudikirira pa njira. Iwo alumbira kuti sadya kapena kumwa mpaka atapha Paulo. Panopa ndi okonzeka kale, akungodikira kuti muwavomere pempho lawo.”
22 Mkulu wa asilikaliyo anawuza mnyamatayo kuti apite koma anamuchenjeza kuti, “Usawuze munthu aliyense kuti wandifotokozera zimenezi.”
Paulo Apita ku Kaisareya
23 Kenaka mkulu wa asilikaliyo anayitana awiri a asilikali olamulira asilikali 100 nawalamula kuti, “Uzani asilikali 200, asilikali 70 okwera pa akavalo ndi 200 onyamula mikondo kuti akonzeke kupita ku Kaisareya usiku omwe uno nthawi ya 9 koloko. 24 Mumukonzerenso Paulo akavalo woti akwerepo kuti akafike bwino kwa bwanamkubwa Felike.”
25 Iye analemba kalata iyi:
26 Ine Klaudiyo Lusiya,
Kwa wolemekezeka, bwanamkubwa Felike:
Ndikupereka moni.
27 Munthuyo Ayuda anamugwira ndipo anali pafupi kumupha, koma ine ndinapita ndi asilikali nʼkukamulanditsa pakuti ndinamva kuti ndi nzika ya Chiroma. 28 Ndinkafuna kudziwa mlandu umene anapalamula, choncho ndinapita naye ku Bwalo lawo Lalikulu. 29 Ine ndinapeza kuti amamuyimba mlandu wa nkhani ya malamulo awo, koma panalibe mlandu woyenera kumuphera kapena kumuyika mʼndende. 30 Nditawuzidwa kuti amukonzera chiwembu munthuyu, ine ndamutumiza kwa inu msanga. Ine ndalamulanso amene akumuyimba mlanduwo kuti abwere kwa inu kudzafotokoza nkhaniyo.
31 Pamenepo asilikali aja anatenga Paulo monga anawalamulira napita naye ku Antipatri usiku. 32 Mmawa mwake iwo anabwerera ku malo a asilikali nasiya okwera pa akavalo kuti apitirire ndi Paulo. 33 Asilikali okwera pa akavalowo atafika ku Kaisareya anapereka kalatayo kwa bwanamkubwa, namuperekanso Paulo. 34 Bwanamkubwayo anawerenga kalatayo ndipo anamufunsa Paulo za dera limene amachokera. Atazindikira kuti amachokera ku Kilikiya, 35 iye anati, “Ndidzamva mlandu wako okuyimba mlandu akabwera kuno.” Ndipo analamulira kuti asilikali adzimulondera Paulo ku nyumba ya mfumu Herode.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.