Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 24

Salimo la Davide.

24 Dziko lapansi ndi la Yehova ndi zonse zimene zili mʼmenemo,
    dziko ndi onse amene amakhala mʼmenemo;
pakuti Iye ndiye anayika maziko ake pa nyanja
    ndi kulikhazika pamwamba pa madzi.

Ndani angakwere phiri la Yehova?
    Ndani angathe kuyima pa malo ake opatulika?
Iye amene ali ndi mʼmanja moyera ndi mtima woyera,
    amene sapereka moyo wake kwa fano
    kapena kulumbira mwachinyengo.
Iyeyo adzalandira madalitso kwa Yehova
    ndipo Mulungu mpulumutsi wake adzagamula kuti alibe mlandu.
Umenewo ndiwo mʼbado wa amene amafunafuna Yehova;
    amene amafunafuna nkhope yanu, Inu Mulungu wa Yakobo.
            Sela

Tukulani mitu yanu inu zipata;
    tsekukani, inu zitseko zakalekalenu,
    kuti Mfumu yaulemerero ilowe.
Kodi Mfumu yaulemereroyo ndani?
    Yehova Wamphamvuzonse,
    Yehova ndiye wamphamvu pa nkhondo.
Tukulani mitu yanu, inu zipata;
    tsekukani, inu zitseko zakalekalenu,
    kuti Mfumu yaulemerero ilowe.
10 Kodi Mfumu yaulemereroyo ndani?
    Yehova Wamphamvuzonse,
    Iye ndiye Mfumu yaulemerero.
            Sela

Eksodo 25:10-22

Bokosi la Chipangano

10 “Tsono apange bokosi lamatabwa amtengo wa mkesha, ndipo kutalika kwake kukhale masentimita 114, mulifupi mwake masentimita 69, msinkhu wake masentimita 69. 11 Bokosilo ulikute ndi golide wabwino kwambiri, mʼkati mwake ndi kunja komwe, ndipo upange mkombero wagolide kuzungulira bokosilo. 12 Upange mphete zinayi zagolide ndipo uzimangirire ku miyendo yake inayi ya bokosilo, mbali ina ziwiri ndi mbali inanso ziwiri. 13 Kenaka upange mizati yamtengo wa mkesha ndi kuzikuta ndi golide. 14 Ndipo ulowetse nsichizo mʼmphete zija za mbali zonse ziwiri za bokosilo kuti azinyamulira. 15 Nsichizo zizikhala mʼmphete za bokosilo nthawi zonse, zisamachotsedwe. 16 Ndipo udzayike mʼbokosilo miyala iwiri yolembedwapo malamulo imene Ine ndidzakupatse.

17 “Upange chivundikiro cha bokosilo cha golide wabwino kwambiri, kutalika kwake masentimita 114, mulifupi mwake masentimita 69. 18 Ndipo upange Akerubi awiri agolide osula ndi nyundo, uwayike mbali ziwiri za chivundikirocho, 19 kerubi mmodzi mbali ina ndi wina mbali inayo. Akerubiwa uwapangire limodzi ndi chivundikirocho mʼmapeto mwa mbali ziwirizo. 20 Mapiko a Akerubiwo adzatambasukire pamwamba pa chivundikiro cha bokosilo kuti achiphimbe. Akerubiwo adzakhale choyangʼanana, aliyense kuyangʼana chivundikirocho. 21 Uyike chivundikirocho pamwamba pa bokosi ndipo mʼbokosilo uyikemo miyala ya malamulo, imene ndidzakupatse. 22 Ndizidzakumana nawe pamenepo, pamwamba pa chivundikiro cha bokosilo, pakati pa Akerubi awiriwo, ndikumadzakupatsa malamulo onse okhudzana ndi Aisraeli.

Akolose 2:1-5

Ndikufuna mudziwe kuti ndikukuvutikirani kwambiri, inuyo pamodzi ndi anzanu a ku Laodikaya, ndi ena onse amene sitinaonane maso ndi maso. Cholinga changa nʼchakuti alimbikitsidwe ndi kuyanjana pamodzi mʼchikondi, akhale odzaza ndi nzeru zomvetsa zinthu, ndi kuti azindikire chinsinsi cha Mulungu, chimene ndi Khristu. Mwa Iyeyu muli chuma chonse chobisidwa cha nzeru ndi chidziwitso. Ndikukuwuzani zimenezi kuti wina aliyense asakunamizeni ndi kukukopani ndi mawu ake. Pakuti ngakhale sindili pakati panu mʼthupi, ndili nanu pamodzi mu mzimu, ndipo ndikukondwa kuona kuti mukulongosola bwino zonse ndiponso kuti chikhulupiriro chanu mwa Khristu ndi chokhazikika ndithu.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.