Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.
21 Inu Yehova, mfumu ikusangalala mu mphamvu yanu,
chimwemwe chake nʼchachikuludi pa kupambana kumene mumapereka!
2 Inu mwayipatsa zokhumba za mtima wake
ndipo simunayimane zopempha za pa milomo yake.
Sela
3 Inu munayilandira ndi madalitso ochuluka
ndipo munayiveka chipewa chaufumu chagolide weniweni pa mutu wake.
4 Iye anakupemphani moyo, ndipo munamupatsa
masiku ochuluka kwamuyaya.
5 Kudzera mʼzigonjetso zimene munapereka, ulemerero wake ndi waukulu;
Inu mwapereka pa iyo ulemerero ndi ufumu.
6 Zoonadi Inu mwayipatsa madalitso amuyaya,
Inu mwayipatsa chisangalalo ndi chimwemwe chimene chili pamaso panu.
7 Pakuti mfumu imadalira Yehova;
kudzera mʼchikondi chake chosatha cha Wammwambamwamba,
iyo sidzagwedezeka.
8 Dzanja lanu lidzayimitsa adani anu onse;
dzanja lanu lamanja lidzagwira adani anu.
9 Pa nthawi ya kuonekera kwanu
mudzawasandutsa ngʼanjo yamoto yotentha.
Mu ukali wake Yehova adzawameza,
ndipo moto wake udzawatha.
10 Inu mudzawononga ana awo pa dziko lapansi,
zidzukulu zawo pakati pa anthu.
11 Ngakhale iwo akukonzereni chiwembu mwa kuchenjera kwawo
sadzapambana;
12 pakuti mudzawapirikitsa ndipo adzaonetsa misana yawo
pamene mudzawaloza ndi mivi yanu.
13 Mukwezeke Inu Yehova mʼmphamvu yanu,
ife tidzayimba nyimbo ndi kutamanda mphamvu yanu.
Davide Agonjetsa Afilisti
17 Afilisti atamva kuti Davide wadzozedwa kukhala mfumu ya Israeli, iwo anapita mwamphamvu kukamusakasaka. Koma Davide atamva zimenezi anakalowa mu linga. 18 Ndipo Afilisti anabwera ndi kukhala momwazika mʼChigwa cha Refaimu. 19 Davide anafunsa Yehova kuti, “Kodi ndipite kukathira nkhondo Afilisti? Kodi mukawapereka mʼmanja mwanga?”
Yehova anamuyankha kuti, “Pita, Ine ndidzawapereka ndithu mʼmanja mwako.”
20 Choncho Davide anapita ku Baala-Perazimu ndi kugonjetsa Afilistiwo. Iye anati, “Monga amasefukira madzi, Yehova waphwanya adani anga ine ndikuona.” Choncho anawatcha malowa Baala Perazimu. 21 Afilisti anasiya mafano awo kumeneko ndipo Davide ndi ankhondo ake anawatenga.
22 Nthawi inanso Afilisti anabweranso namwazikana mʼChigwa cha Refaimu; 23 Davide anafunsa Yehova ndipo Yehovayo anayankha kuti, “Usapite molunjika koma uzungulire kumbuyo kwawo ndipo ukawathire nkhondo patsogolo pa mitengo ya mkandankhuku. 24 Mukakangomva phokoso pa msonga za mitengo ya mkandankhuku, mukayende mofulumira, chifukwa izi zikasonyeza kuti Yehova ali patsogolo panu kukantha ankhondo a Afilisti.” 25 Kotero Davide anachita zimene Yehova anamulamulira ndipo anakantha Afilisti njira yonse kuchokera ku Geba mpaka ku Gezeri.
Yesu Apita Kuphwando Lamisasa
7 Zitatha izi Yesu anayendayenda mu Galileya, ndi cholinga chakuti asafike ku Yudeya chifukwa Ayuda kumeneko amadikira kuti amuphe. 2 Koma phwando la Ayuda lamisasa litayandikira, 3 abale a Yesu anati kwa Iye, “Inu muyenera kuchoka kuno ndi kupita ku Yudeya, kuti ophunzira anu akaone zodabwitsa zomwe mumachita. 4 Palibe wina aliyense amene amafuna kukhala wodziwika amachita zinthu mseri. Popeza Inu mukuchita zinthu izi, mudzionetsere nokha ku dziko la pansi.” 5 Pakuti ngakhale abale ake omwe sanamukhulupirire.
6 Choncho Yesu anawawuza iwo kuti, “Nthawi yanga yoyenera sinafike; kwa inu nthawi ina iliyonse ndi yoyenera. 7 Dziko lapansi silingakudeni inu, koma limandida Ine chifukwa Ine ndimachitira umboni kuti zomwe limachita ndi zoyipa. 8 Inu pitani kuphwando. Ine sindipita tsopano kuphwando ili chifukwa kwa Ine nthawi yoyenera sinafike.” 9 Atanena izi, Iye anakhalabe mu Galileya.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.