Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 21

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.

21 Inu Yehova, mfumu ikusangalala mu mphamvu yanu,
    chimwemwe chake nʼchachikuludi pa kupambana kumene mumapereka!
Inu mwayipatsa zokhumba za mtima wake
    ndipo simunayimane zopempha za pa milomo yake.
            Sela
Inu munayilandira ndi madalitso ochuluka
    ndipo munayiveka chipewa chaufumu chagolide weniweni pa mutu wake.
Iye anakupemphani moyo, ndipo munamupatsa
    masiku ochuluka kwamuyaya.
Kudzera mʼzigonjetso zimene munapereka, ulemerero wake ndi waukulu;
    Inu mwapereka pa iyo ulemerero ndi ufumu.
Zoonadi Inu mwayipatsa madalitso amuyaya,
    Inu mwayipatsa chisangalalo ndi chimwemwe chimene chili pamaso panu.
Pakuti mfumu imadalira Yehova;
    kudzera mʼchikondi chake chosatha cha Wammwambamwamba,
    iyo sidzagwedezeka.

Dzanja lanu lidzayimitsa adani anu onse;
    dzanja lanu lamanja lidzagwira adani anu.
Pa nthawi ya kuonekera kwanu
    mudzawasandutsa ngʼanjo yamoto yotentha.
Mu ukali wake Yehova adzawameza,
    ndipo moto wake udzawatha.
10 Inu mudzawononga ana awo pa dziko lapansi,
    zidzukulu zawo pakati pa anthu.
11 Ngakhale iwo akukonzereni chiwembu mwa kuchenjera kwawo
    sadzapambana;
12 pakuti mudzawapirikitsa ndipo adzaonetsa misana yawo
    pamene mudzawaloza ndi mivi yanu.

13 Mukwezeke Inu Yehova mʼmphamvu yanu,
    ife tidzayimba nyimbo ndi kutamanda mphamvu yanu.

2 Samueli 5:11-16

11 Tsono Hiramu mfumu ya Turo inatumiza amithenga ake kwa Davide, pamodzi ndi mitengo ya mkungudza ndi amisiri a matabwa ndi amisiri a miyala, ndipo anamumangira Davide nyumba yaufumu. 12 Choncho Davide anazindikira kuti Yehova wamukhazikitsa kukhala mfumu ya Israeli ndipo wakuza ufumu wake chifukwa cha anthu ake, Aisraeli.

13 Davide atafika ku Yerusalemu kuchokera ku Hebroni, anakwatira azikazi natenganso akazi ena kumeneko, ndipo anabereka ana aamuna ndi aakazi ambiri. 14 Mayina a ana amene anabereka ku Yerusalemu ndi awa: Samua, Sobabu, Natani, Solomoni, 15 Ibihari, Elisua, Nefegi, Yafiya, 16 Elisama, Eliada ndi Elifeleti.

Yakobo 5:7-12

Kupirira Mʼmasautso

Tsono abale, pirirani mpaka kubwera kwa Ambuye. Onani mmene amachitira mlimi. Amadikirira kuti zipatso zabwino zioneke mʼmunda mwake. Amayembekezera mokhazikika mtima kuyambira nthawi ya mvula yoyamba mpaka yotsiriza. Inunso mukhale owugwira mtima ndi osasinthika chifukwa Ambuye ali pafupi kubwera. Abale, musamanenezane zoyipa kuopa kuti mungadzaweruzidwe. Woweruza ali pa khomo!

10 Abale, tengerani chitsanzo cha aneneri amene anayankhula mʼdzina la Ambuye. Iwowo anakumana ndi zovuta koma anapirira. 11 Monga mukudziwa, tinawatenga ngati odalitsika anthu amene anapirira. Munamva za kupirira kwa Yobu ndipo mwaona zimene Ambuye anamuchitira potsiriza pake. Ambuye ndi wodzaza ndi chisoni ndi chifundo.

12 Koposa zonse, abale anga, musamalumbire. Polumbira osamatchula kumwamba kapena dziko lapansi, kapena china chilichonse. “Inde” wanu azikhala “Inde,” ndipo “Ayi” wanu azikhala “Ayi,” kuopa kuti mungadzapezeke olakwa.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.