Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 21

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.

21 Inu Yehova, mfumu ikusangalala mu mphamvu yanu,
    chimwemwe chake nʼchachikuludi pa kupambana kumene mumapereka!
Inu mwayipatsa zokhumba za mtima wake
    ndipo simunayimane zopempha za pa milomo yake.
            Sela
Inu munayilandira ndi madalitso ochuluka
    ndipo munayiveka chipewa chaufumu chagolide weniweni pa mutu wake.
Iye anakupemphani moyo, ndipo munamupatsa
    masiku ochuluka kwamuyaya.
Kudzera mʼzigonjetso zimene munapereka, ulemerero wake ndi waukulu;
    Inu mwapereka pa iyo ulemerero ndi ufumu.
Zoonadi Inu mwayipatsa madalitso amuyaya,
    Inu mwayipatsa chisangalalo ndi chimwemwe chimene chili pamaso panu.
Pakuti mfumu imadalira Yehova;
    kudzera mʼchikondi chake chosatha cha Wammwambamwamba,
    iyo sidzagwedezeka.

Dzanja lanu lidzayimitsa adani anu onse;
    dzanja lanu lamanja lidzagwira adani anu.
Pa nthawi ya kuonekera kwanu
    mudzawasandutsa ngʼanjo yamoto yotentha.
Mu ukali wake Yehova adzawameza,
    ndipo moto wake udzawatha.
10 Inu mudzawononga ana awo pa dziko lapansi,
    zidzukulu zawo pakati pa anthu.
11 Ngakhale iwo akukonzereni chiwembu mwa kuchenjera kwawo
    sadzapambana;
12 pakuti mudzawapirikitsa ndipo adzaonetsa misana yawo
    pamene mudzawaloza ndi mivi yanu.

13 Mukwezeke Inu Yehova mʼmphamvu yanu,
    ife tidzayimba nyimbo ndi kutamanda mphamvu yanu.

2 Samueli 5:1-10

Davide Adzozedwa Kukhala Mfumu ya Israeli

Mafuko onse a Israeli anabwera kwa Davide ku Hebroni ndipo anati, “Ife ndife mafupa ndi mnofu wanu. Kale lija, pamene Sauli anali mfumu yathu, inu ndinu amene munkatsogolera Aisraeli pa nkhondo zawo. Ndipo Yehova anakuwuzani kuti, ‘Udzaweta anthu anga Aisraeli, ndipo udzakhala mfumu yawo.’ ”

Akuluakulu onse a Israeli atafika kwa Mfumu Davide ku Hebroni, mfumu inachita nawo pangano ku Hebroni pamaso pa Yehova, ndipo anamudzoza Davide kukhala mfumu ya Israeli.

Davide anali ndi zaka makumi atatu pamene anakhala mfumu, ndipo analamulira zaka makumi anayi. Analamulira Yuda ali ku Hebroni kwa zaka zisanu ndi ziwiri ndi miyezi isanu ndi umodzi, ndipo ali ku Yerusalemu analamulira Israeli yense ndi Yuda kwa zaka 33.

Davide Alanda Mzinda wa Yerusalemu

Mfumu ndi ankhondo ake anapita ku Yerusalemu kukathira nkhondo Ayebusi amene ankakhala kumeneko. Ayebusiwo anamuwuza Davide kuti, “Inu simulowa muno. Ngakhale osaona ndi olumala akhoza kukuthamangitsani.” Iwo ankaganiza kuti, “Davide sangathe kulowa momwemo.” Komabe Davide analanda linga la Ziyoni, limene ndi mzinda wa Davide.

Pa tsiku limenelo Davide anati, “Aliyense wogonjetsa Ayebusi ayenera kudzera mʼngalande ya madzi kuti akafike kwa iwo amene ndi ‘olumala ndi osaona,’ amene ndi adani a Davide.” Nʼchifukwa chake amanena kuti, “Olumala ndi osaona sadzalowa mʼnyumba yaufumu.”

Tsono Davide anakhazikika mu lingamo ndipo mzindawu anawutcha, Mzinda wa Davide. Iye anamanga malo onse ozungulira kuyambira ku matsitso ozungulira khoma. 10 Ndipo mphamvu za Davide zinkakulirakulira chifukwa anali ndi Yehova Mulungu Wamphamvuzonse.

2 Akorinto 11:16-33

Paulo Anyadira Mazunzo Ake

16 Ndibwereze kunena kuti, wina aliyense asandiyese chitsiru. Koma ngati mutero, mundilandire monga mmene mukhoza kulandirira chitsiru, kuti ndinyadirepo pangʼono. 17 Kudzinyadira kwangaku, sindikuyankhula monga mmene Ambuye akufunira koma ngati chitsiru. 18 Popeza ambiri akudzitama monga dziko lapansi limachitira, inenso ndidzitamanso. 19 Inu mumalolera kukhala ndi zitsiru mokondwera chifukwa mumati ndinu anzeru! 20 Kunena zoona mumangololera aliyense; amene amakusandutsani akapolo, kapena amene amakudyerani masuku pamutu, kapena amene amakupezererani, kapena amene amadzitukumula, kapena amene amakumenyani khofi. 21 Ndikuvomera mwamanyazi kuti ife sitinali olimba mtima kuti nʼkuchita zinthu zimenezi.

Ndikuyankhula ngati chitsiru kuti chimene wina aliyense akhoza kudzitama nacho, Inenso ndikhoza kudzitama nachonso. 22 Kodi iwo ndi Ahebri? Inenso ndine Mhebri. Kodi iwo ndi Aisraeli? Inenso ndine Mwisraeli. Kodi iwo ndi zidzukulu za Abrahamu? Inenso ndine mdzukulu wa Abrahamu. 23 Kodi iwo ndi atumiki a Khristu? Ndikuyankhula ngati wamisala. Ine ndine woposa iwowo. Ndagwira ntchito kwambiri kupambana iwo, ndakhala ndikuyikidwa mʼndende kawirikawiri, ndakwapulidwapo kwambiri, kawirikawiri ndinali pafupi kufa. 24 Andikwapulapo kasanu zikoti zija za Ayuda, makumi anayi kuchotsapo chimodzi. 25 Katatu anandimenya ndi ndodo. Kamodzi anandigendapo miyala. Katatu sitima yathu ya panyanja inasweka, ndipo ndinakhala usiku ndi usana ndi kuyandama pa nyanja. 26 Ndakhala ndikuyenda maulendo ataliatali. Moyo wanga wakhala ukukumana ndi zoopsa pa mitsinje, zoopsa za achifwamba, zoopsa zochokera kwa abale anga Ayuda, zoopsa zochokera kwa anthu akunja. Ndinakumana ndi zoopsa mʼmizinda, mʼmidzi, pa nyanja, ndi pakati pa abale onyenga. 27 Ndakhala ndikugwira ntchito molimbika ndipo kawirikawiri ndakhala ndikuchezera usiku wonse osagona. Ndakhala ndikumva njala ndi ludzu ndipo kawirikawiri ndakhala wopanda chakudya. Ndakhala ndi kuzizidwa ndi wosowa zovala. 28 Kuwonjezera pa zonsezi, tsiku ndi tsiku ndimakhala pa chipsinjo cha nkhawa ya mipingo yonse. 29 Ndani ali wofowoka, ine wosakhala naye mʼkufowoka kwakeko? Ndani amene mnzake amuchimwitsa, ine wosavutika mu mtima?

30 Ngati nʼkoyenera kudzitamandira, ndidzadzitamandira pa zinthu zimene zimaonetsa kufowoka kwanga. 31 Mulungu, Atate a Ambuye Yesu, amene tiyenera kumutamanda nthawi zonse, akudziwa kuti sindikunama. 32 Ku Damasiko, bwanamkubwa woyimira Mfumu Areta, anayika alonda kuzungulira mzinda wonse kuti andigwire. 33 Koma abale anandiyika mʼdengu nanditsitsira pa chipupa kudzera pa zenera la mpandawo, motero ndinapulumuka mʼmanja mwake.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.