Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 48

Nyimbo. Salimo la ana a Kora.

48 Wamkulu ndi Yehova, ndi woyenera kwambiri matamando
    mu mzinda wa Mulungu wathu, phiri lake loyera.
Lokongola mu utali mwake,
    chimwemwe cha dziko lonse lapansi.
Malo aatali kwambiri a Zafoni ndiye Phiri la Ziyoni,
    mzinda wa Mfumu yayikulu.
Mulungu ali mu malinga ake;
    Iye wadzionetsa yekha kuti ndiye malinga akewo.

Pamene mafumu anasonkhana pamodzi,
    pamene anayendera pamodzi kudzalimbana nafe,
iwo anaona mzindawo ndipo anadabwa kwambiri;
    anathawa ndi mantha aakulu.
Pomwepo anagwidwa nako kunjenjemera,
    ululu wonga wa mkazi woyembekezera pa nthawi yochira.
Inu munawawononga monga sitima zapamadzi za ku Tarisisi
    zitawonongeka ndi mphepo ya kummawa.

Monga momwe tinamvera,
    kotero ife tinaona
mu mzinda wa Yehova Wamphamvuzonse,
    mu mzinda wa Mulungu wathu.
    Mulungu adzawuteteza kwamuyaya.

Mʼkati mwa Nyumba yanu Mulungu,
    ife timalingaliramo zachikondi chanu chosasinthika.
10 Monga dzina lanu, Inu Mulungu,
    matamando anu amafika ku malekezero a dziko lapansi
    dzanja lanu lamanja ladzaza ndi chilungamo.
11 Phiri la Ziyoni likukondwera,
    midzi ya Yuda ndi yosangalala
    chifukwa cha maweruzo anu.

12 Yendayendani mu Ziyoni, uzungulireni mzindawo,
    werengani nsanja zake.
13 Yangʼanitsitsani bwino mipanda yake,
    penyetsetsani malinga ake,
    kuti mudzafotokoze za izo ku mʼbado wotsatira.
14 Pakuti Mulungu uyu ndi Mulungu wathu ku nthawi zosatha;
    Iye adzakhala mtsogoleri wathu mpaka ku mapeto.

2 Samueli 2:1-11

Davide Adzozedwa Kukhala Mfumu ya Yuda

Patapita nthawi, Davide anafunsa Yehova kuti, “Kodi ndipite ku umodzi mwa mizinda ya Yuda?”

Yehova anayankha kuti, “Pita.”

Davide anafunsanso kuti, “Kodi ndipite kuti?”

Yehova anayankha kuti, “Ku Hebroni.”

Choncho Davide anapita kumeneko ndi akazi ake awiri, Ahinoamu wa ku Yezireeli ndi Abigayeli mkazi wamasiye uja wa Nabala wa ku Karimeli. Davide anatenganso anthu amene anali nawo aliyense ndi banja lake, ndipo anakakhala ku midzi ya ku Hebroni. Kenaka amuna a ku Yuda anabwera ku Hebroni ndipo kumeneko anadzoza Davide kukhala mfumu ya fuko la Yuda.

Davide atawuzidwa kuti anthu a ku Yabesi Giliyadi ndi amene anayika mʼmanda Sauli, iye anatuma amithenga kwa anthu a ku Yabesi Giliyadi kuti akayankhule nawo kuti, “Yehova akudalitseni poonetsa kukoma mtima kwanu kwa Sauli mbuye wanu pomuyika mʼmanda. Tsopano Yehova akuonetseni kukoma mtima ndi kukhulupirika kwake ndipo inenso ndidzakukomerani mtima chifukwa munachita zimenezi. Tsopano khalani amphamvu ndi olimba mtima, pakuti Sauli mbuye wanu wafa, ndipo fuko la Yuda landidzoza kukhala mfumu yawo.”

Nkhondo Pakati pa Otsatira Davide ndi Otsatira Sauli

Pa nthawi imeneyi Abineri mwana wa Neri, wolamulira ankhondo a Sauli, anatenga Isi-Boseti mwana wa Sauli ndi kubwera naye ku Mahanaimu. Iye anamuyika kuti akhale mfumu yoyangʼanira Giliyadi, Asuri ndi Yezireeli, pamodzi ndi Efereimu, Benjamini ndi Israeli yense.

10 Isi-Boseti mwana wa Sauli anali wa zaka makumi anayi pamene anakhala mfumu ya Israeli ndipo analamulira zaka ziwiri. Koma fuko la Yuda linatsatira Davide. 11 Davide anakhala mfumu ku Hebroni akulamulira fuko la Yuda, kwa zaka zisanu ndi chimodzi ndi miyezi isanu ndi umodzi.

1 Akorinto 4:8-13

Inu muli nazo kale zonse zimene mufuna! Inu mwalemera kale! Inu mwayamba kale kulamulira ife! Ndilakalaka mukanakhaladi mafumu kuti ife tikhale nawo mafumu pamodzi ndi inu. Pakuti kwa ine zikuoneka ngati kuti Mulungu watiyika ife atumwi pachionetsero, kumapeto kwa mndandanda, monga anthu oweruzidwa kuti akaphedwe mʼmabwalo. Ife tayikidwa kuti tionekere ku dziko lonse, kwa angelo ndi anthu. 10 Ife ndife opusa chifukwa cha Khristu, koma inu ndinu anzeru mwa Khristu! Ife ndife ofowoka koma inu ndinu amphamvu! Inu ndinu olemekezeka koma ife ndife opeputsidwa! 11 Mpaka pano tili ndi njala ndi ludzu, tili ndi sanza, tikuzunzidwa, tilibe nyumba. 12 Timagwira ntchito molimbika ndi manja athu. Akamatitemberera, ife timadalitsa; tikasautsidwa, ife timapirira. 13 Pamene atilalatira timayankha mwachifundo. Mpaka pano takhala ngati zinyalala za dziko, monga zakudzala za dziko lapansi.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.