Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide mtumiki wa Yehova. Iye anayimbira Yehova nyimbo iyi pamene Yehovayo anamupulumutsa mʼdzanja la adani ake onse ndiponso mʼdzanja la Sauli.
18 Davide anati: Ine ndimakukondani Inu Yehova, mphamvu zanga.
2 Yehova ndiye thanthwe langa, chitetezo changa ndi mpulumutsi wanga;
Mulungu wanga ndi thanthwe langa mʼmene ndimathawiramo.
Chishango changa ndi ndodo yachipulumutso changa, ndi linga langa.
3 Ndimayitana Yehova amene ndi woyenera matamando,
ndipo ndapulumutsidwa kwa adani anga.
4 Zingwe za imfa zinandizinga;
mitsinje yothamanga yachiwonongeko inandiopsa kwambiri.
5 Anandimanga ndi zingwe za ku manda;
misampha ya imfa inalimbana nane.
6 Mʼmasautso anga ndinapemphera kwa Yehova;
ndinalirira kwa Mulungu wanga kuti andithandize.
Ali mʼNyumba yake, anamva mawu anga;
kulira kwanga kunafika pamaso pake ndi mʼmakutu mwake.
43 Inu mwandipulumutsa mʼmanja mwa anthu;
mwandisandutsa kukhala mtsogoleri wa anthu a mitundu ina.
Anthu amene sindikuwadziwa ali pansi pa ulamuliro wanga.
44 Alendo amadzipereka okha pamaso panga;
akangomva za ine amandigonjera.
45 Iwo onse anataya mtima;
anatuluka mʼmalinga awo akunjenjemera.
46 Yehova ndi wamoyo! Litamandidwe Thanthwe langa!
Akuzike Mulungu Mpulumutsi wanga!
47 Iye ndi Mulungu amene amabwezera chilango,
amene amagonjetsa anthu a mitundu yonse amene ali pansi pa ulamuliro wanga,
48 amene amandipulumutsa mʼmanja mwa adani anga.
Inu munandikuza kuposa adani anga;
munandilanditsa mʼmanja mwa anthu ankhanza.
49 Choncho ine ndidzakutamandani pakati pa anthu a mitundu ina, Inu Yehova;
ndidzayimba nyimbo zotamanda dzina lanu.
50 Iye amapereka chipambano chachikulu kwa mfumu yake;
amaonetsa chikondi chosasinthika kwa wodzozedwa wake,
kwa Davide ndi zidzukulu zake kwamuyaya.
14 Davide ankakhala mʼmapanga mʼdziko lamapiri ku chipululu cha Zifi. Sauli ankamufufuza tsiku ndi tsiku, koma Mulungu sanapereke Davide mʼmanja mwake.
15 Davide anaona kuti Sauli akufunafuna kuti amuphe. Nthawiyi nʼkuti Davide ali mʼchipululu cha Zifi ku Horesi. 16 Ndipo Yonatani mwana wa Sauli anapita kwa Davide ku Horesi ndipo anamulimbitsa mtima pomuwuza kuti Yehova ali naye. 17 Iye anamuwuza kuti, “Usaope, abambo anga sadzakupha. Iwe udzakhala mfumu ya Israeli ndipo ine ndidzakhala wachiwiri wako. Ngakhale abambo anga Sauli akudziwa zimenezi.” 18 Awiriwa anachita pangano pamaso pa Yehova. Ndipo Yonatani anabwerera kwawo, koma Davide anakhalabe ku Horesi.
Tito Atumidwa ku Korinto
16 Tithokoze Mulungu amene anayika mu mtima wa Tito changu chomwecho chimene ine ndili nacho pa inu. 17 Pakuti Tito sanangovomera kokha pempho lathu, koma yekha anafunitsitsa kwambiri kubwera kwa inu mwa iye yekha. 18 Ndipo tikumutumiza pamodzi ndi mʼbale amene mipingo yonse yamuyamikira chifukwa cha utumiki wake wa Uthenga Wabwino. 19 Chowonjezera china nʼchakuti anasankhidwa ndi mipingo kuti atiperekeze pamene ife tikukapereka zopereka, zimene tikuchita pofuna kupereka ulemu kwa Ambuye mwini ndi kuonetsa kufunitsitsa kwathu pothandiza. 20 Tikufuna kupewa kutikayikira kulikonse za mmene tikuyendetsera mphatso zochulukazi. 21 Pakuti tikuyesetsa kuchita zolondola, osati pamaso pa Ambuye pokha komanso pamaso pa anthu.
22 Kuwonjezera apo, tikuwatumiza pamodzi ndi mʼbale wathu, amene nthawi zambiri watitsimikizira mʼnjira zosiyanasiyana kuti ndi wachangu ndiponso chifukwa ali ndi chikhulupiriro chachikulu mwa inu. 23 Kunena za Tito, ndiye mnzanga ndi wogwira naye ntchito pakati panu. Kunena za abale athu, ndiwo oyimirira mipingo ndi olemekezetsa Khristu. 24 Choncho anthu amenewa atsimikizireni za chikondi chanu ndipo adziwe chifukwa chimene ife timakunyadirani, kuti mipingo yonse iwone chimenechi.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.