Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 119:113-128

Samekhi

113 Ndimadana ndi anthu apawiripawiri,
    koma ndimakonda malamulo anu.
114 Inu ndinu pothawirapo panga ndi chishango changa;
    chiyembekezo changa chili mʼmawu anu.
115 Chokani kwa ine, inu anthu ochita zoyipa,
    kuti ndisunge malamulo a Mulungu wanga!
116 Mundichirikize molingana ndi lonjezo lanu, ndipo ndidzakhala ndi moyo;
    musalole kuti chiyembekezo changa chipite pachabe.
117 Gwirizizeni, ndipo ndidzapulumutsidwa;
    nthawi zonse ndidzasamalira zophunzitsa zanu.
118 Inu mumakana onse amene amasochera kuchoka pa zophunzitsa zanu,
    pakuti chinyengo chawo ndi chopanda phindu.
119 Anthu onse oyipa a pa dziko lapansi mumawayesa ngati zinthu zakudzala;
    nʼchifukwa chake ndimakonda umboni wanu.
120 Thupi langa limanjenjemera chifukwa cha kuopa Inu;
    ndimachita mantha ndi malamulo anu.

Ayini

121 Ndachita zolungama ndi zabwino;
    musandisiye mʼmanja mwa ondizunza.
122 Onetsetsani kuti mtumiki wanu akukhala bwino,
    musalole kuti anthu odzikuza andipondereze.
123 Maso anga alefuka, kufunafuna chipulumutso chanu,
    kufunafuna lonjezo lanu lolungama.
124 Muchite naye mtumiki wanu molingana ndi chikondi chanu chosasinthika,
    ndipo mundiphunzitse malamulo anu.
125 Ine ndine mtumiki wanu; patseni mzimu wondizindikiritsa,
    kuti ndimvetsetse umboni wanu.
126 Yehova, ndi nthawi yoti muchitepo kanthu;
    malamulo anu akuswedwa.
127 Chifukwa choti ndimakonda malamulo anu
    kuposa golide, kuposa golide woyengeka bwino,
128 ndiponso chifukwa choti ndimaona kuti malangizo anu onse ndi wowongoka,
    ndimadana ndi njira iliyonse yoyipa.

1 Samueli 19:8-17

Panabukanso nkhondo ina ndipo Davide anapita ndi kukamenyana ndi Afilisti. Iye anawakantha mwamphamvu kotero kuti Afilisti anathawa.

Tsiku lina mzimu woyipa uja unafikanso pa Sauli. Nthawi imeneyi nʼkuti Sauli uja ali mʼnyumba mwake, mkondo uli mʼdzanja lake ndi Davide akuyimba zeze, 10 Sauli anafuna kumubaya Davide ndi kumukhomera kukhoma, koma Davide anapewa mkondowo kotero Sauli anakabaya pa khoma. Usiku womwewo Davide anathawa.

11 Usiku womwewo Sauli anatumiza anthu ku nyumba ya Davide kuti akamubisalire ndi kumupha mmamawa. Koma Mikala mkazi wake anamuchenjeza nati, “Ngati usiku uno supulumutsa moyo wako, mawa udzaphedwa.” 12 Choncho Mikala anamutulutsira Davide pa zenera, ndipo anathawa ndi kupulumuka. 13 Kenaka Mikala anatenga fano naligoneka pa bedi nayika pilo wa ubweya wa mbuzi ku mutu kwa fanolo ndipo analifunditsa nsalu.

14 Pamene amithenga a Sauli aja anafika kuti akamugwire Davide, Mikala anati, “Davide akudwala.”

15 Koma Sauli anatumanso anthuwo kuti akamuone Davide, nati, “Mubwere naye kuno ali pa bedi pomwepo kuti ndidzamuphe.” 16 Koma pamene anthuwo analowa, anangoona fano pa bedipo ndi pilo wa ubweya wa mbuzi ku mutu kwake.

17 Tsono Sauli anafunsa Mikala kuti, “Nʼchifukwa chiyani wandinamiza chotere polola kuti mdani wanga athawe?”

Mikala anayankha kuti, “Davide anandiwuza kuti, ‘Ukapanda kutero ndikupha.’ ”

Marko 6:45-52

Yesu Ayenda pa Nyanja

45 Nthawi yomweyo Yesu anawuza ophunzira ake kuti alowe mʼbwato ndi kuti atsogole kupita ku Betisaida, pamene Iye ankawuza anthu kuti azipita. 46 Atawasiya, Iye anakwera ku phiri kukapemphera.

47 Pofika madzulo, bwato linali pakati pa nyanja, ndipo Iye anali yekha pa mtunda. 48 Iye anaona ophunzira ake akuvutika popalasa bwato, chifukwa mphepo imawomba mokumana nawo. Pa nthawi ya mʼbandakucha Iye anafika kwa iwo akuyenda pa nyanja. Anali pafupi kuwapitirira, 49 koma atamuona Iye akuyenda pa nyanja, anaganiza kuti anali mzukwa. Iwo anafuwula, 50 pakuti onse anamuona ndipo anachita mantha.

Nthawi yomweyo Iye anawayankhula nati, “Limbani mtima! Ndine. Musachite mantha.” 51 Ndipo Iye anakwera mʼbwato pamodzi nawo, ndipo mphepo inaleka. Iwo anadabwa kwambiri, 52 popeza sanazindikire zimene zinachitika pa malofu a buledi; pakuti mitima yawo inali yowuma.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.