Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Samekhi
113 Ndimadana ndi anthu apawiripawiri,
koma ndimakonda malamulo anu.
114 Inu ndinu pothawirapo panga ndi chishango changa;
chiyembekezo changa chili mʼmawu anu.
115 Chokani kwa ine, inu anthu ochita zoyipa,
kuti ndisunge malamulo a Mulungu wanga!
116 Mundichirikize molingana ndi lonjezo lanu, ndipo ndidzakhala ndi moyo;
musalole kuti chiyembekezo changa chipite pachabe.
117 Gwirizizeni, ndipo ndidzapulumutsidwa;
nthawi zonse ndidzasamalira zophunzitsa zanu.
118 Inu mumakana onse amene amasochera kuchoka pa zophunzitsa zanu,
pakuti chinyengo chawo ndi chopanda phindu.
119 Anthu onse oyipa a pa dziko lapansi mumawayesa ngati zinthu zakudzala;
nʼchifukwa chake ndimakonda umboni wanu.
120 Thupi langa limanjenjemera chifukwa cha kuopa Inu;
ndimachita mantha ndi malamulo anu.
Ayini
121 Ndachita zolungama ndi zabwino;
musandisiye mʼmanja mwa ondizunza.
122 Onetsetsani kuti mtumiki wanu akukhala bwino,
musalole kuti anthu odzikuza andipondereze.
123 Maso anga alefuka, kufunafuna chipulumutso chanu,
kufunafuna lonjezo lanu lolungama.
124 Muchite naye mtumiki wanu molingana ndi chikondi chanu chosasinthika,
ndipo mundiphunzitse malamulo anu.
125 Ine ndine mtumiki wanu; patseni mzimu wondizindikiritsa,
kuti ndimvetsetse umboni wanu.
126 Yehova, ndi nthawi yoti muchitepo kanthu;
malamulo anu akuswedwa.
127 Chifukwa choti ndimakonda malamulo anu
kuposa golide, kuposa golide woyengeka bwino,
128 ndiponso chifukwa choti ndimaona kuti malangizo anu onse ndi wowongoka,
ndimadana ndi njira iliyonse yoyipa.
Sauli Ayesanso Kupha Davide
19 Sauli anawuza mwana wake Yonatani ndi nduna zake zonse kuti aphe Davide. Koma Yonatani amamukonda kwambiri Davide. 2 Choncho anawuza Davide kuti, “Abambo anga Sauli akufuna kukupha. Tsono uchenjere. Mmawa upite ukabisale ndipo ukakhale komweko. 3 Ine ndidzapita ndi kukayima pafupi ndi abambo anga ku munda kumene iwe ukabisale. Ndipo ndidzayankhula ndi abambo anga za iwe ndipo chilichonse chimene ndikamve ndidzakuwuza.”
4 Tsono Yonatani anakanena zabwino za Davide kwa abambo ake Sauli ndipo anati, “Mfumu musachimwire mtumiki wanu Davide, sanakuchimwireni, koma amakuchitirani zabwino kwambiri. 5 Iye anayika moyo wake pa chiswe pamene anapha Mfilisiti uja. Choncho Yehova anachita zazikulu popambanitsa Aisraeli pa nkhondo. Inu munaona zonsezo ndipo munakondwera. Nanga nʼchifukwa chiyani mukufuna kuchimwira munthu wosalakwa pofuna kupha Davide?”
6 Sauli anamvera mawu a Yonatani ndipo analumbira kuti, “Pali Yehova, Davide sadzaphedwa.”
7 Pambuyo pake Yonatani anayitana Davide namuwuza zonsezi. Choncho Yonatani anabwera naye Davide kwa Sauli ndipo ankamutumikira Sauliyo monga kale.
39 Kutacha, anthu sanazindikire dzikolo, koma anaona pomwe sitima zimayimapo pamodzi ndi mchenga wa pa gombe. Iwo anaganiza zokocheza sitimayo kumeneko ngati zikanatheka kutero. 40 Atadula anangula aja, nawasiya mʼnyanja, pa nthawi yomweyo anamasula zingwe zimene anamangira zowongolera sitimayo. Kenaka anayimika chinsalu chimene mphepo imakankha kuti sitima iyende, ndipo anayamba kupita ku gombe. 41 Koma sitimayo inagunda mchenga wobisika ndipo inayima. Mbali ya kutsogolo ya sitimayo inakanirira ndipo sinathe kuyendanso, ndipo mbali yakumbuyo inasweka ndi kuwomba kwa mafunde.
42 Asilikali anaganiza za kupha amʼndende onse, kuti angasambire kupita pa mtunda ndi kuthawa. 43 Koma wolamulira asilikali uja anafuna kupulumutsa Paulo ndipo anawaletsa kuchita zimene anakonza. Iye analamulira asilikali kuti amene amatha kusambira kuti adziponye mʼmadzi ndi kuyamba kukafika pa mtunda. 44 Otsalawo anayenera kugwira matabwa kapena tizidutswa ta sitimayo. Motero onse anapulumuka nakafika pa mtunda.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.