Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 119:113-128

Samekhi

113 Ndimadana ndi anthu apawiripawiri,
    koma ndimakonda malamulo anu.
114 Inu ndinu pothawirapo panga ndi chishango changa;
    chiyembekezo changa chili mʼmawu anu.
115 Chokani kwa ine, inu anthu ochita zoyipa,
    kuti ndisunge malamulo a Mulungu wanga!
116 Mundichirikize molingana ndi lonjezo lanu, ndipo ndidzakhala ndi moyo;
    musalole kuti chiyembekezo changa chipite pachabe.
117 Gwirizizeni, ndipo ndidzapulumutsidwa;
    nthawi zonse ndidzasamalira zophunzitsa zanu.
118 Inu mumakana onse amene amasochera kuchoka pa zophunzitsa zanu,
    pakuti chinyengo chawo ndi chopanda phindu.
119 Anthu onse oyipa a pa dziko lapansi mumawayesa ngati zinthu zakudzala;
    nʼchifukwa chake ndimakonda umboni wanu.
120 Thupi langa limanjenjemera chifukwa cha kuopa Inu;
    ndimachita mantha ndi malamulo anu.

Ayini

121 Ndachita zolungama ndi zabwino;
    musandisiye mʼmanja mwa ondizunza.
122 Onetsetsani kuti mtumiki wanu akukhala bwino,
    musalole kuti anthu odzikuza andipondereze.
123 Maso anga alefuka, kufunafuna chipulumutso chanu,
    kufunafuna lonjezo lanu lolungama.
124 Muchite naye mtumiki wanu molingana ndi chikondi chanu chosasinthika,
    ndipo mundiphunzitse malamulo anu.
125 Ine ndine mtumiki wanu; patseni mzimu wondizindikiritsa,
    kuti ndimvetsetse umboni wanu.
126 Yehova, ndi nthawi yoti muchitepo kanthu;
    malamulo anu akuswedwa.
127 Chifukwa choti ndimakonda malamulo anu
    kuposa golide, kuposa golide woyengeka bwino,
128 ndiponso chifukwa choti ndimaona kuti malangizo anu onse ndi wowongoka,
    ndimadana ndi njira iliyonse yoyipa.

1 Samueli 18:6-30

Anthu akubwerera kwawo Davide atapha Mfilisiti uja, amayi anatuluka mʼmizinda yonse ya Israeli, akuyimba ndi kuvina kukachingamira mfumu Sauli. Ankayimba ndi kuvina mokondwa, kwinaku ngʼoma ndi zitoliro zikulira. Amayiwo ankalandizana nyimbo mokondwera namati:

“Sauli wapha 1,000,
    Koma Davide wapha miyandamiyanda.”

Koma Sauli anapsa mtima kwambiri ndipo mawu amenewa anamuyipira. Iye anati, “Iwo amuwerengera Davide miyandamiyanda, koma ine 1,000 okha. Nanga chatsalanso nʼchiyani kuti atenge? Si ufumu basi?” Ndipo kuyambira tsiku limeneli Sauli ankamuchitira nsanje Davide.

10 Mmawa mwake mzimu woyipa uja unabwera mwamphamvu pa Sauli. Sauli anayamba kubwebweta mʼnyumba mwake. Davide ankamuyimbira zeze monga nthawi zonse. Sauli anali ndi mkondo mʼdzanja lake. 11 Tsono anawuponya mkondowo, namati mu mtima mwake, “Ndimubaya Davide ndi kumukhomera ku khoma.” Koma Davide anawulewa kawiri konse.

12 Pambuyo pake Sauli amamuopa Davide chifukwa Yehova anali ndi Davideyo, nʼkumusiya Sauli. 13 Kotero Sauli anamuchotsa Davide pamaso pake ndi kumuyika kukhala mtsogoleri wa ankhondo 1,000. Choncho Davide ankapita ndi kubwera akutsogolera ankhondowa. 14 Davide ankapambana kwambiri pa chilichonse chimene amachita chifukwa Yehova anali naye. 15 Sauli ataona momwe Davide ankapambanira, iye anamuopa kwambiri. 16 Koma Aisraeli onse ndi anthu a Yuda ankamukonda Davide chifukwa ankawatsogolera pa nkhondo zawo.

17 Tsiku lina Sauli anawuza Davide kuti, “Nayu Merabi mwana wanga wamkazi wamkulu. Ine ndakupatsa kuti umukwatire. Koma unditumikire molimba mtima pomenya nkhondo za Yehova.” Poteropo Sauli ankanena kuti, “Ndisamuphe ndi manja angawa koma aphedwe ndi Afilisti!”

18 Ndipo Davide anati kwa Sauli, “Ine ndine yani, ndipo abale anga kapena banja la abambo anga ndife yani mʼdziko la Israeli kuti ndikhale mpongozi wa mfumu?” 19 Koma pa nthawi yoti Merabi mwana wa Sauli akwatiwe ndi Davide, Sauli anamupereka kwa Adrieli wa ku Mehola kuti amukwatire.

20 Koma Mikala mwana wamkazi wa Sauli anamukonda Davide ndipo Sauli atamva za zimenezi, anakondwera. 21 Sauli ankaganiza kuti, “Ndimupatse amukwatire kuti akhale ngati msampha kwa Davideyo, ndipo adzaphedwe ndi Afilisti.” Choncho Sauli anawuza Davide kachiwiri, “Tsopano udzakhala mkamwini wanga.”

22 Sauli analamulanso nduna zake kuti, “Muyankhuleni Davide mwamseri ndi kumuwuza kuti, ‘Taona, mfumu imakondwera nawe, ndipo nduna zake zonse zimakukonda. Tsono ukhale mkamwini wa mfumu.’ ”

23 Iwo anakamuwuza Davide mawu amenewa, koma Davide anati, “Kodi inu mukuganiza kuti ndi chinthu chapafupi kukhala mpongozi wa mfumu? Ine ndine wosauka ndiponso wosatchuka.”

24 Nduna za Sauli zinamuwuza zonse zimene anayankha Davide. 25 Sauli anayankha kuti, “Kamuwuzeni Davide kuti, ‘Mfumu sikufuna malowolo a mtundu wina uliwonse koma timakungu ta msonga za mavalo a Afilisti 100 kuti ilipsire adani ake.’ ” Maganizo a Sauli anali akuti Davide aphedwe ndi Afilisti.

26 Nduna za Saulizo zitamuwuza Davide zimenezi, anakondwera kuti akhale mpongozi wa mfumu. Koma nthawi imene anapatsidwa isanathe, 27 Davide ndi anyamata ake anapita ndi kukapha Afilisti 200. Iye anabwera ndi timakungu tija natipereka tonse kwa mfumu kuti akhale mpongozi wa mfumu. Kotero Sauli anapereka mwana wake wamkazi, Mikala, kwa Davide kuti amukwatire.

28 Sauli atazindikira kuti Yehova anali ndi Davide ndiponso kuti mwana wake Mikala amamukonda Davide, 29 iye anapitirirabe kumuopa Davide ndi kumadana naye moyo wake wonse.

30 Nthawi zonse pamene atsogoleri a Afilisti ankatuluka kukamenya nkhondo, Davide ankapambana kuposa nduna zonse za Sauli. Choncho dzina lake linatchuka kwambiri.

Machitidwe a Atumwi 27:13-38

Namondwe pa Nyanja

13 Mphepo yochokera kummwera itayamba kuwomba pangʼonopangʼono, anthuwo anaganiza kuti apeza chimene amafuna; kotero analowetsa nangula ndipo anayamba kuyenda mʼmbali mwa chilumba cha Krete. 14 Pasanathe nthawi yayitali, mphepo yamkuntho yotchedwa Eurokulo, inayamba kuwomba kuchokera ku chilumbacho. 15 Mphepo yamkunthoyo inawomba sitima ija ndipo sinathe kulimbana nayo, kotero ife tinayigonjera ndi kuyamba kutengedwa nayo. 16 Tikudutsa mʼmbali mwa kachilumba kakangʼono kotchedwa Kawuda, tinavutika kuti tisunge bwato lopulumukiramo. 17 Anthuwo atakweza bwatolo mʼsitima, anakulunga zingwe sitimayo kuti ayilimbitse. Poopa kuti angakagunde mchenga wa ku Surti, iwo anatsitsa nangula ndi kuyilola sitima kuti idzingoyenda ndi mphepo. 18 Ife tinavutika kwambiri ndi namondwe kotero kuti mmawa mwake tinayamba kuponya katundu mʼmadzi. 19 Pa tsiku lachitatu anaponya mʼnyanja zipangizo za mʼsitima ndi manja awo. 20 Sitinaone dzuwa kapena nyenyezi kwa masiku ambiri ndipo namondwe anapitirira kuwomba kwambiri, pomaliza ife tonse tinalibenso chiyembekezo choti nʼkupulumuka.

21 Anthu aja atakhala nthawi yayitali osadya, Paulo anayimirira pakati pawo ndipo anati, “Anthu inu, mukanamvera malangizo anga oti tisachoke ku Krete: zonsezi sizikanawonongeka ndi kutayika. 22 Koma tsopano ndikuti limbani mtima, chifukwa palibe aliyense wa inu amene adzataya moyo wake; koma sitima yokhayi idzawonongeka. 23 Usiku wathawu mngelo wa Mulungu, Mulungu amene ine ndili wake ndipo ndimamutumikira, anayima pafupi ndi ine, 24 ndipo iyeyu anati, ‘Usachite mantha, Paulo. Ukuyenera kukayima pamaso pa Kaisara; ndipo Mulungu mwa kukoma mtima kwake wakupatsa miyoyo ya anthu onse amene ukuyenda nawo.’ 25 Tsono limbani mtima, anthu inu, pakuti ine ndili ndi chikhulupiriro mwa Mulungu kuti zichitika monga momwe wandiwuzira. 26 Komabe tiyenera kukatsakamira pa chilumba china chake.”

Kuwonongeka kwa Sitima

27 Pakati pa usiku wa tsiku la khumi ndi chinayi tikukankhidwabe ndi mphepo mʼnyanja ya Adriya, oyendetsa sitimayo anazindikira kuti timayandikira ku mtunda. 28 Iwo anatenga choyezera kuzama kwa nyanja ndi kupeza kuti kuzama kwake kunali mamita 36. Atayendanso pangʼono anatenganso choyezera chija napeza kuti kuzama kwake kunali 27. 29 Poopa kuti tingagunde miyala, iwo anatsitsira anangula anayi mʼmadzi kumbuyo kwa sitimayo ndipo tinapemphera kuti kuche. 30 Pofuna kuthawa mʼsitimayo, oyendetsa aja anatsitsira mʼnyanja bwato lopulumukiramo nʼkumachita ngati akufuna kutsitsira anangula mʼnyanjamo kutsogolo kwa sitimayo. 31 Pamenepo Paulo anawuza wolamulira asilikali uja ndi asilikaliwo kuti, “Ngati anthu awa sakhala mʼsitima muno, inu simungapulumuke.” 32 Pamenepo asilikaliwo anadula zingwe za bwatolo ndipo linagwera mʼmadzi.

33 Kutatsala pangʼono kucha, Paulo anawawumiriza anthu onse kuti adye. Iye anati, “Kwa masiku khumi ndi anayi mwakhala mukuda nkhawa ndipo simumadya kanthu kalikonse. 34 Tsopano ine ndikukupemphani kuti mudye. Muyenera kudya kuti mupulumuke. Palibe ndi mmodzi yemwe wa inu adzataye ngakhale tsitsi limodzi la pamutu pake.” 35 Paulo atanena zimenezi, anatenga buledi nayamika Mulungu pamaso pa onse. Ndipo ananyema bulediyo nayamba kudya. 36 Onse analimba mtima nayamba kudyanso. 37 Tonse pamodzi mʼsitimamo tinalipo anthu 276. 38 Onse atadya, nakhuta anapeputsa sitimayo potaya tirigu mʼnyanja.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.