Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
1 Samueli 17:1

Davide ndi Goliati

17 Afilisti anasonkhanitsa ankhondo awo ku Soko mʼdziko la Yuda. Iwo anamanga misasa yawo ku Efesi-Damimu, pakati pa Soko ndi Azeka.

1 Samueli 17:4-11

Tsono munthu wina wamphamvu, dzina lake Goliati wochokera ku Gati anatuluka ku misasa ya Afilisti. Msinkhu wake unali pafupipafupi mamita atatu. Iye ankavala chipewa chamkuwa ndi malaya achitsulo olemera makilogalamu 57. Ankavalanso zokuta miyendo yake zamkuwa, ndipo ankanyamula nthungo ya mkuwa pa phewa pake. Thunthu la mkondo wake linali ngati mkombero wowombera nsalu, ndipo mutu wa mkondowo unkalemera makilogalamu asanu ndi awiri. Patsogolo pake pamakhala munthu wonyamula zida zake za nkhondo.

Goliatiyo anayimirira ndi kufuwula kwa ankhondo a Israeli, nati, “Nʼchifukwa chiyani mwakonzekera nkhondo chotere? Kodi sindine Mfilisiti ndipo inu sindinu akapolo a Sauli? Sankhani munthu kuti abwere kwa ine. Ngati angathe kumenyana nane ndi kundipha, ife tidzakhala akapolo anu, koma ngati ine ndimugonjetsa ndi kumupha, inu mudzakhala akapolo athu ndi kumatitumikira.” 10 Ndipo Mfilisitiyo anati, “Bwerani lero timenyane basi! Patseni munthu kuti ndimenyane naye.” 11 Atamva mawu a Mfilisitiyo, Sauli ndi Aisraeli onse anataya mtima nachita mantha kwambiri.

1 Samueli 17:19-23

19 Sauli, abale akowo ndi asilikali onse a Israeli ali ku chigwa cha Ela, akumenyana ndi Afilisti.”

20 Mʼmamawa mwake Davide anasiya nkhosa mʼmanja mwa munthu wina ndipo anatenga zakudyazo nanyamuka monga momwe Yese abambo ake anamulamulira. Anakafika ku misasa pamene asilikali ankapita kukandanda pa mzere ku nkhondo, nʼkufuwula mfuwu wankhondo. 21 Aisraeli ndi Afilisti anandanda pa mzere wankhondo moyangʼanana. 22 Tsono Davide anasiyira zakudya zija munthu wosunga katundu nathamangira kumene kunali ankhondo kuja ndi kukalonjera abale ake. 23 Pamene iye ankayankhula nawo anangoona Goliati wa ku Gati uja akuchoka pa mzere wa Afilisti akufuwula mawu onyoza monga mwa masiku onse, ndipo Davide ankawamva.

1 Samueli 17:32-49

32 Davide anati kwa Sauli, “Munthu aliyense asataye mtima chifukwa cha Mfilisitiyu. Ine kapolo wanu ndipita kukamenyana naye.”

33 Sauli anayankha Davide kuti, “Iwe sungathe kupita kukamenyana ndi Mfilisitiyu. Iwe ukanali mnyamata, koma iyeyu ndi amene wakhala akumenya nkhondo kuyambira unyamata wake.”

34 Koma Davide anati kwa Sauli, “Kapolo wanune ndinkaweta nkhosa za abambo anga. Ndipo mkango kapena chimbalangondo chikamabwera ndi kugwira mwana wankhosa pakati pa nkhosazo, 35 ine ndinkatsatira ndi kupha chirombocho. Choncho ndinkapulumutsa mwana wankhosa uja mʼkamwa mwake. Ndipo chinkati chikandiwukira, ine ndinkagwira tchowa lake, nʼkuchikantha mpaka kuchipha. 36 Ine kapolo wanu ndinapha mkango ngakhalenso chimbalangondo. Tsono Mfilisiti wosachita mdulidweyu adzaphedwa monga zinazo chifukwa wanyoza ankhondo a Mulungu wamoyo. 37 Yehova amene anandilanditsa mʼkamwa mwa mkango ndi chimbalangondo adzandilanditsa mʼmanja mwa Mfilisiti uyu.”

Sauli anati kwa Davide, “Pita, ndipo Yehova akhale nawe.”

38 Ndipo Sauli anamveka Davide mwinjiro wake. Anamuveka zovala zankhondo ndi chipewa cha mkuwa. 39 Davide anamangirira lupanga pa mwinjirowo. Atayesa kuyenda nazo, analephera chifukwa anali asanazizolowere.

Iye anati kwa Sauli, “Sindingathe kuyenda nazo chifukwa sindinazizolowere.” Ndipo anazivula. 40 Pambuyo pake anatenga ndodo yake mʼmanja. Kenaka anasankha miyala yosalala bwino mu mtsinje ndi kuyiika mʼthumba lake la ku ubusa. Legeni ili mʼmanja mwake, Davide ananyamuka kukakumana ndi Mfilisiti uja.

41 Tsono Mfilisiti uja anayambapo kupita kumene kunali Davide, mnyamata wonyamula zida zake za nkhondo ali patsogolo pake. 42 Mfilisitiyo atangomuona Davide, anamunyoza popeza kuti Davide anali mnyamata chabe wofiirira ndi wa maonekedwe abwino. 43 Iye anati kwa Davide, “Kodi ndine galu, kuti ubwere kwa ine ndi ndodo?” Ndipo Mfilisitiyo anamutemberera Davide potchula mayina a milungu yake. 44 Iye anatinso, “Bwera kuno ndipo ndidzapereka mnofu wako kwa mbalame zamlengalenga ndi kwa zirombo zakuthengo!”

45 Koma Davide anati kwa Mfilisitiyo, “Iwe wabwera kwa ine ndi lupanga, mkondo ndi nthungo, koma ine ndikubwera kwa iwe mʼdzina la Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa ankhondo Aisraeli amene iwe ukuwanyoza. 46 Anatinso lero lino Yehova adzakupereka mʼmanja mwanga. Ndidzakukantha ndi kudula mutu wako. Ndidzapereka mitembo ya asilikali a Afilisti kwa mbalame za mlengalenga, ndi kwa zirombo zakuthengo ndipo dziko lonse lapansi lidzadziwa kuti mu Israeli muli Mulungu. 47 Onse amene asonkhana pano adzadziwa kuti Mulungu sapulumutsa anthu ndi lupanga kapena mkondo, pakuti nkhondo ndi ya Yehova. Iye adzakuperekani mʼmanja mwathu.”

48 Mfilisitiyo akusendera pafupi kuti akumane naye, Davideyo anathamangira mofulumira ku mzere wa nkhondo kukakumana naye. 49 Davideyo anapisa dzanja lake mʼthumba lake natengamo mwala ndipo anawuponya, nalasa pa mphumi pa Mfilisitiyo. Mwalawo unalowa pa chipumi chake, ndipo anagwa chafufumimba.

1 Samueli 17:57-18:5

57 Davide atangobwerako kokapha Mfilisiti kuja, Abineri anamutenga nabwera naye kwa Sauli, mutu wa Mfilisiti uja uli mʼmanja mwake.

58 Sauli anamufunsa, “Mnyamata iwe, kodi paja ndiwe mwana wayani?”

Davide anati, “Ndine mwana wa mtumiki wanu Yese wa ku Betelehemu.”

Sauli Achitira Nsanje Davide

18 Davide atatha kuyankhula ndi Sauli, mtima wa Yonatani unagwirizana ndi mtima wa Davide, ndipo iye ankamukonda Davide monga momwe ankadzikondera yekha. Choncho Sauli anamusunga Davideyo kuyambira tsiku limenelo ndipo sanamulole kuti abwerere ku nyumba ya abambo ake. Ndipo Yonatani anapanga pangano ndi Davide chifukwa ankamukonda monga momwe ankadzikondera. Yonatani anavula mkanjo umene anavala ndipo anamupatsa Davide pamodzi ndi zovala za nkhondo, lupanga, uta ndi lamba.

Davide ankapita kulikonse kumene Sauli ankamutuma kuti apite kukamenya nkhondo, ndipo ankapambana. Choncho Sauli anamupatsa udindo woyangʼanira gulu lankhondo. Ichi chinakondweretsa anthu onse ngakhalenso atsogoleri a nkhondo a Sauli.

1 Samueli 18:10-16

10 Mmawa mwake mzimu woyipa uja unabwera mwamphamvu pa Sauli. Sauli anayamba kubwebweta mʼnyumba mwake. Davide ankamuyimbira zeze monga nthawi zonse. Sauli anali ndi mkondo mʼdzanja lake. 11 Tsono anawuponya mkondowo, namati mu mtima mwake, “Ndimubaya Davide ndi kumukhomera ku khoma.” Koma Davide anawulewa kawiri konse.

12 Pambuyo pake Sauli amamuopa Davide chifukwa Yehova anali ndi Davideyo, nʼkumusiya Sauli. 13 Kotero Sauli anamuchotsa Davide pamaso pake ndi kumuyika kukhala mtsogoleri wa ankhondo 1,000. Choncho Davide ankapita ndi kubwera akutsogolera ankhondowa. 14 Davide ankapambana kwambiri pa chilichonse chimene amachita chifukwa Yehova anali naye. 15 Sauli ataona momwe Davide ankapambanira, iye anamuopa kwambiri. 16 Koma Aisraeli onse ndi anthu a Yuda ankamukonda Davide chifukwa ankawatsogolera pa nkhondo zawo.

Masalimo 9:9-20

Yehova ndiye kothawirako kwa opsinjika mtima,
    linga pa nthawi ya mavuto.
10 Iwo amene amadziwa dzina lanu adzadalira Inu,
    pakuti Inu Yehova, simunawatayepo amene amafunafuna inu.

11 Imbani nyimbo zamatamando kwa Yehova, ali pa mpando waufumu mu Ziyoni;
    lengezani pakati pa mitundu ya anthu zimene wachita.
12 Pakuti Iye amene amabwezera chilango akupha anzawo wakumbukira;
    Iye salekerera kulira kwa ozunzika.

13 Inu Yehova, onani momwe adani anga akundizunzira!
    Chitireni chifundo ndipo ndichotseni pa zipata za imfa,
14 kuti ndilengeze za matamando anu
    pa zipata za ana aakazi a Ziyoni,
    kuti pamenepo ndikondwere ndi chipulumutso chanu.
15 Mitundu ya anthu yagwa mʼdzenje limene yakumba;
    mapazi awo akodwa mu ukonde umene anawubisa.
16 Yehova amadziwika ndi chilungamo chake;
    oyipa akodwa ndi ntchito za manja awo.
            Higayoni. Sela
17 Oyipa amabwerera ku manda,
    mitundu yonse imene imayiwala Mulungu.
18 Koma osowa sadzayiwalika nthawi zonse,
    kapena chiyembekezo cha ozunzika kutayika nthawi zonse.

19 Dzukani Inu Yehova, musalole munthu kuti apambane;
    mitundu yonse iweruzidwe pamaso panu.
20 Akantheni ndi mantha aakulu, Inu Yehova;
    mitundu idziwe kuti iwo ndi anthu wamba.
            Sela

Masalimo 133

Salimo la Davide. Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.

133 Onani, nʼkokoma ndi kokondweretsa ndithu
    pamene abale akhala pamodzi mwachiyanjano!
Zili ngati mafuta amtengowapatali othiridwa pa mutu,
    otsikira ku ndevu,
ku ndevu za Aaroni,
    oyenderera mpaka mʼkhosi mwa mkanjo wake.
Zili ngati mame a ku Heremoni
    otsikira pa Phiri la Ziyoni.
Pakuti pamenepo Yehova amaperekapo dalitso,
    ndiwo moyo wamuyaya.

2 Akorinto 6:1-13

Pogwira naye ntchito pamodzi, tikukudandaulirani kuti musangolandira chisomo cha Mulungu pachabe. Pakuti akunena kuti,

“Pa nthawi yanga yabwino yokomera anthu mtima ndinakumvera,
    ndipo pa nthawi yopulumutsa ndinakuthandiza.

Taonani, ndikukuwuzani kuti, ino ndiyo nthawi yabwino ya Ambuye, lero ndiye tsiku la chipulumutso.”

Masautso a Paulo

Ife sitikuyika chokhumudwitsa pa njira ya wina aliyense, kuti utumiki wathu usanyozeke. Mʼmalo mwake, mwanjira iliyonse timasonyeza kuti ndife atumiki a Mulungu popirira kwambiri mʼmasautso, mʼzowawa ndi mʼzodetsa nkhawa. Pomenyedwa, kuponyedwa mʼndende ndi mʼzipolowe. Pogwira ntchito mwamphamvu, posagona usiku onse, posowa chakudya; pokhala moyo woyera mtima, pomvetsa zinthu, wokoma mtima ndi wachifundo mwa Mzimu Woyera ndi mwachikondi choonadi ndi poyankhula choonadi mwamphamvu ya Mulungu. Zida zimene zili mʼdzanja lamanja ndi lamanzere ndizo chilungamo. Timatumikira Mulungu ngakhale ena amatinyoza ndi ena amatilemekeza, ena amatinenera chipongwe, enanso amatiyamikira. Ena amatitenga kukhala ngati onena zoona, ndipo enanso amatitenga kukhala ngati onena zabodza. Amatiyesa osadziwika komatu ndife odziwika kwambiri. Amatiyesa wooneka ngati tikufa, koma tikupitirirabe ndi moyo, okanthidwa, koma osaphedwa. 10 Amatiyesa achisoni, koma ndife achimwemwe nthawi zonse, aumphawi, koma olemeretsa ambiri; wopanda kanthu, koma tili ndi zonse.

11 Tayankhula momasuka kwa inu, Akorinto, ndipo tanena zonse za kumtima kwathu. 12 Ife sitikukubisirani chikondi chathu pa inu, koma inu mukubisa chikondi chanu pa ife. 13 Pofuna kufanana zochita ndi kuyankhula monga kwa ana anga, nanunso muzinena za kukhosi kwanu.

Marko 4:35-41

Yesu Aletsa Namondwe

35 Tsiku limenelo atafika madzulo, anawuza ophunzira ake kuti, “Tiyeni tiwolokere tsidya lina.” 36 Atasiya gulu la anthu mʼmbuyo, anamutenga Iye, napita naye monga momwe anali mʼbwatolo. Panalinso mabwato ena pamodzi ndi Iye. 37 Mphepo yamkuntho inabuka, ndipo mafunde anawomba bwatolo, kotero kuti linali pafupi kumira. 38 Pa nthawi imeneyi Yesu anali akugona atatsamira pilo kumbuyo kwa bwato. Ophunzira anamudzutsa nati kwa Iye, “Aphunzitsi, kodi simukusamala kuti timira?”

39 Yesu anauka nadzudzula mphepo nati kwa mafunde, “Chete! Khala bata!” Pamenepo mphepo inaleka ndipo kunachita bata.

40 Iye anati kwa ophunzira ake, “Muli ndi mantha chifukwa chiyani? Kodi mukanalibe chikhulupiriro?”

41 Iwo anachita mantha nafunsana wina ndi mnzake kuti, “Uyu ndani? Ngakhale mphepo ndi nyanja zimumvera Iye!”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.