Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
9 Yehova ndiye kothawirako kwa opsinjika mtima,
linga pa nthawi ya mavuto.
10 Iwo amene amadziwa dzina lanu adzadalira Inu,
pakuti Inu Yehova, simunawatayepo amene amafunafuna inu.
11 Imbani nyimbo zamatamando kwa Yehova, ali pa mpando waufumu mu Ziyoni;
lengezani pakati pa mitundu ya anthu zimene wachita.
12 Pakuti Iye amene amabwezera chilango akupha anzawo wakumbukira;
Iye salekerera kulira kwa ozunzika.
13 Inu Yehova, onani momwe adani anga akundizunzira!
Chitireni chifundo ndipo ndichotseni pa zipata za imfa,
14 kuti ndilengeze za matamando anu
pa zipata za ana aakazi a Ziyoni,
kuti pamenepo ndikondwere ndi chipulumutso chanu.
15 Mitundu ya anthu yagwa mʼdzenje limene yakumba;
mapazi awo akodwa mu ukonde umene anawubisa.
16 Yehova amadziwika ndi chilungamo chake;
oyipa akodwa ndi ntchito za manja awo.
Higayoni. Sela
17 Oyipa amabwerera ku manda,
mitundu yonse imene imayiwala Mulungu.
18 Koma osowa sadzayiwalika nthawi zonse,
kapena chiyembekezo cha ozunzika kutayika nthawi zonse.
19 Dzukani Inu Yehova, musalole munthu kuti apambane;
mitundu yonse iweruzidwe pamaso panu.
20 Akantheni ndi mantha aakulu, Inu Yehova;
mitundu idziwe kuti iwo ndi anthu wamba.
Sela
55 Sauli ataona Davide akupita kukakumana ndi Mfilisitiyo anafunsa Abineri, mkulu wa ankhondo kuti, “Abineri, kodi mnyamatayu ndi mwana wa yani?”
Abineri anayankha kuti, “Ndithu mfumu muli apa ine sindikumudziwa.”
56 Mfumu inati, “Pita kafufuze kuti mnyamata ameneyu ndi mwana wa yani.”
57 Davide atangobwerako kokapha Mfilisiti kuja, Abineri anamutenga nabwera naye kwa Sauli, mutu wa Mfilisiti uja uli mʼmanja mwake.
58 Sauli anamufunsa, “Mnyamata iwe, kodi paja ndiwe mwana wayani?”
Davide anati, “Ndine mwana wa mtumiki wanu Yese wa ku Betelehemu.”
Sauli Achitira Nsanje Davide
18 Davide atatha kuyankhula ndi Sauli, mtima wa Yonatani unagwirizana ndi mtima wa Davide, ndipo iye ankamukonda Davide monga momwe ankadzikondera yekha. 2 Choncho Sauli anamusunga Davideyo kuyambira tsiku limenelo ndipo sanamulole kuti abwerere ku nyumba ya abambo ake. 3 Ndipo Yonatani anapanga pangano ndi Davide chifukwa ankamukonda monga momwe ankadzikondera. 4 Yonatani anavula mkanjo umene anavala ndipo anamupatsa Davide pamodzi ndi zovala za nkhondo, lupanga, uta ndi lamba.
5 Davide ankapita kulikonse kumene Sauli ankamutuma kuti apite kukamenya nkhondo, ndipo ankapambana. Choncho Sauli anamupatsa udindo woyangʼanira gulu lankhondo. Ichi chinakondweretsa anthu onse ngakhalenso atsogoleri a nkhondo a Sauli.
Paulo Apita ku Yerusalemu
21 Titalawirana nawo, tinachoka kumeneko mʼsitima ya pamadzi, ndipo tinayenda molunjika mpaka kufika ku Kosi. Mmawa mwake tinapita ku Rode, kuchokera kumeneko tinapita ku Patara. 2 Kumeneko tinapeza sitima yapamadzi yopita ku Foinike. Choncho tinalowamo nʼkunyamuka. 3 Tinaona chilumba cha Kupro ndipo tinadutsa kummwera kwake nʼkupita ku Siriya. Tinakayima ku Turo chifukwa sitima yathuyo imayenera kusiya katundu kumeneko. 4 Tinafunafuna ophunzira kumeneko, ndipo titawapeza tinakhala nawo masiku asanu ndi awiri. Iwowa, mwa Mzimu Woyera anakakamiza Paulo kuti asapite ku Yerusalemu. 5 Koma nthawi yathu itatha, tinachokako ndi kupitiriza ulendo wathu. Ophunzira onse pamodzi ndi akazi awo ndi ana anatiperekeza mpaka kunja kwa mzinda. Ndipo kumeneko tinagwada mʼmbali mwa nyanja ndi kupemphera. 6 Titatsanzikana, tinalowa mʼsitima ija, iwowo anabwerera ku nyumba zawo.
7 Ife tinapitiriza ulendo wathu wochokera ku Turo mpaka tinafika ku Ptolemayi. Kumeneko tinalonjera abale ndi kukhala nawo tsiku limodzi. 8 Tinachoka mmawa mwake, mpaka tinakafika ku Kaisareya. Tinapita kukakhala mʼnyumba ya mlaliki Filipo, amene anali mmodzi mwa atumiki a mpingo asanu ndi awiri aja. 9 Iye anali ndi ana aakazi anayi osakwatiwa amene anali ndi mphatso ya uneneri.
10 Titakhala kumeneko masiku ambiri, kunabwera mneneri wina wochokera ku Yudeya dzina lake Agabu. 11 Atafika kwa ife, anatenga lamba wa Paulo, nadzimanga naye manja ake ndi mapazi ake ndipo anati, “Mzimu Woyera akuti, ‘Mwini lambayu, Ayuda adzamumanga chomwechi ku Yerusalemu, ndipo adzamupereka mʼmanja mwa anthu a mitundu ina.’ ”
12 Titamva zimenezi, ife pamodzi ndi anthu kumeneko tinamudandaulira Paulo kuti asapite ku Yerusalemu. 13 Koma Paulo anayankha kuti, “Chifukwa chiyani mukulira ndi kunditayitsa mtima? Ndine wokonzeka osati kumangidwa kokha ayi, komanso kufa ku Yerusalemu chifukwa cha dzina la Ambuye Yesu.” 14 Titalephera kumuletsa tinamuleka ndipo tinati, “Chifuniro cha Ambuye chichitike.”
15 Pambuyo pake, ife tinakonzeka ndi kunyamuka kumapita ku Yerusalemu. 16 Ena mwa ophunzira a ku Kaisareya anatiperekeza mpaka kukatifikitsa ku nyumba ya Mnasoni, kumene tinakonza kuti tizikhalako. Iye anali wa ku Kupro ndiponso mmodzi wa ophunzira oyambirira.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.