Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 53

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a Mahalati. Ndakatulo ya Davide.

53 Chitsiru chimati mu mtima mwake,
    “Kulibe Mulungu.”
Iwo ndi oyipa ndipo njira zawo ndi zonyansa;
    palibe ndi mmodzi yemwe amene amachita chabwino.

Mulungu kumwamba amayangʼana pansi pano
    pa ana a anthu
kuti aone ngati alipo wina wanzeru,
    wofunafuna Mulungu.
Aliyense wabwerera,
    iwo onse pamodzi akhala oyipa;
palibe ndi mmodzi yemwe amene amachita chabwino,
    ngakhale mmodzi.

Kodi anthu ochita zoyipawa adzaphunziradi;
    anthu amene amadya anthu anga monga mmene anthu amadyera buledi,
    ndipo sapemphera kwa Mulungu?
Iwo anali pamenepo atathedwa nzeru ndi mantha aakulu
    pamene panalibe kanthu kochititsa mantha.
Mulungu anamwazamwaza mafupa a anthu amene anakuthirani nkhondo;
    inuyo munawachititsa manyazi, pakuti Mulungu anawanyoza.

Ndithu, chipulumutso cha Israeli nʼchochokera ku Ziyoni!
    Pamene Mulungu adzabwezeretsanso ulemerero wa anthu ake,
    lolani Yakobo akondwere ndi Israeli asangalale!

1 Samueli 13:23-14

Yonatani Athira Nkhondo Afilisti

23 Tsono gulu lina lankhondo la Chifilisti linapita kukalonda mpata wa Mikimasi.

14 Tsiku lina Yonatani mwana wa Sauli anawuza mnyamata wake womunyamulira zida zake za nkhondo kuti, “Tiye tiwoloke tipite ku kaboma ka Afilisti tsidya ilo.” Koma iye sanawuze abambo ake.

Sauli ankakhala mʼmalire a Gibeya pa tsinde pa mtengo wamakangadza ku Migironi. Anthu amene anali naye analipo 600. Pakati pawo panalinso Ahiya amene ankavala efodi. Iye anali mwana wa Ahitubi, mʼbale wake wa Ikabodi mwana wa Finehasi, mwana wa Eli, wansembe wa Yehova wa ku Silo. Koma palibe amene anadziwa kuti Yonatani wachoka.

Pa mpata pamene Yonatani ankafuna kudutsa kukafika ku kaboma ka nkhondo ka Afilisti kunali thanthwe lotsetsereka mbali ina ndi lina lotsetsereka mbali inayo. Thanthwe limodzi linkatchedwa Bozezi ndipo linalo linkatchedwa Seni. Thanthwe limodzi linali chakumpoto kuyangʼanana ndi Mikimasi, ndipo thanthwe linalo linali chakummwera kuyangʼanana ndi Geba.

Yonatani anawuza mnyamata wake womunyamulira zida uja kuti, “Tiye tiwoloke tipite ku kaboma ka anthu osachita mdulidwewo. Mwina Yehova adzatigwirira ntchito. Palibe chomuletsa Yehova kutipulumutsa, ngakhale tikhale ambiri kapena ochepa.”

Mnyamata uja anati, “Chitani chilichonse chimene mtima wanu ukhumba. Ine ndili nanu pamodzi. Chimene mtima wanu ukhumba ndi chomwenso ine ndikhumba.”

Yonatani anati, “Tiye tsono tiwoloke kupita kumene kuli anthuwo ndi kukadzionetsa kwa iwo. Akatiwuza kuti, ‘Imani pomwepo mpaka tikupezeni,’ ife tikangoyima pomwepo osapita kumene kuli iwoko. 10 Koma akadzati, ‘Bwerani kuno,’ ndiye ife tikapitedi, chifukwa ichi chidzakhala chizindikiro chakuti Yehova wapereka mʼmanja mwathu.”

11 Choncho awiriwa anadzionetsa ku kaboma ka nkhondo ka Afilisti. Tsono Afilistiwo anati, “Taonani! Aheberi akutuluka mʼmaenje mʼmene anabisala.” 12 Anthu a ku kaboma kaja anafuwula kwa Yonatani ndi mnyamata wake uja kuti, “Bwerani kuno ndipo tikuphunzitsani phunziro.”

Ndipo Yonatani anati kwa mnyamata wake. “Nditsate pakuti Yehova wapereka Afilistiwa mʼmanja mwa Aisraeli.”

13 Choncho Yonatani anakwera mokwawa, ndipo mnyamata wake uja ankamutsata. Tsono Yonatani anathira nkhondo Afilisti aja namawagwetsa, ndipo mnyamata wake uja ankawapha pambuyo pa iyeyo. 14 Nthawi yoyambayo Yonatani ndi mnyamata wake uja anapha anthu makumi awiri ndipo anawaphera pa malo ochepa okwanira ngati theka la ekala.

Aisraeli Agonjetsa Afilisti

15 Tsono gulu lonse la ankhondo, ndiye kuti iwo amene anali mʼmisasa ndi mʼminda ndiponso iwo amene anali ku kaboma ka ankhondo kaja, onse anagwidwa ndi mantha aakulu. Dzikonso linagwedezeka, choncho anthu anachita mantha koopsa.

16 Alonda a Sauli a ku Gibeya dziko la Benjamini atangomwaza maso anangoona chigulu cha asilikali chikumwazikana uku ndi uku. 17 Kenaka Sauli anawawuza anthu amene anali naye kuti, “Awerengeni asilikali kuti muona amene wachoka.” Atawawerenga anapeza kuti Yonatani ndi mnyamata wake womunyamulira zida zake za nkhondo palibe.

18 Tsono Sauli anawuza Ahiya kuti, “Bwera nalo Bokosi la Mulungulo.” (Nthawi imeneyo nʼkuti efodiyo ili ndi Ahiya pamaso pa Aisraeli). 19 Pamene Sauli amayankhula ndi wansembe, phokoso limanka likulirakulira mu msasa wa Afilisti, Kotero Sauli anati kwa wansembe, “Leka kuwombeza.”

20 Ndipo Sauli ndi asilikali onse amene anali naye anasonkhana kupita kukamenya nkhondo, ndipo anangoona chisokonezo chachikulu kwambiri. Afilisti akuphana okhaokha. 21 Aheberi ena amene kale anali ndi Afilisti mpaka kukakhala ku misasa yawo, iwonso anatembenuka nakhala pamodzi ndi Aisraeli amene ankatsata Sauli ndi Yonatani. 22 Ngakhale Aisraeli amene ankabisala ku dziko lamapiri la Efereimu atamva kuti Afilisti akuthawa, nawonso anawathamangitsa Afilistiwo nawathira nkhondo. 23 Nkhondo inapitirira mpaka kufika ku Beti-Aveni. Choncho Yehova anapulumutsa Aisraeli tsiku limenelo.

Agalatiya 6:11-18

Osati Mdulidwe koma Kulengedwa Mwatsopano

11 Onani zilembo zazikulu zimene ine ndikulemba ndi dzanja langa.

12 Onse amene akufuna kuoneka abwino pamaso pa anthu akukukakamizani kuti muchite mdulidwe. Akuchita izi ndi cholinga chimodzi chokha, chakuti apewe kuzunzidwa chifukwa cha mtanda wa Khristu. 13 Pakuti ngakhale iwowa amene anachita mdulidwe satsata Malamulo, komabe akufuna kuti muchite mdulidwe kuti anyadire mdulidwe wanuwo. 14 Ine sindingathe kunyadira kanthu kena koma mtanda wa Ambuye athu Yesu Khristu, kudzera mwa mtandawo dziko lapansi linapachikidwa kwa ine ndi ine ku dziko lapansi. 15 Pakuti kaya mdulidwe kapena kusachita mdulidwe, sizitanthauza kanthu; chofunika ndi kulengedwa mwatsopano. 16 Mtendere ndi chifundo zikhale kwa onse amene amatsata chiphunzitso ichi, ndi pa Israeli wa Mulungu.

17 Pomaliza wina asandivutitse, pakuti mʼthupi mwanga muli zizindikiro za Yesu.

18 Chisomo cha Ambuye athu Yesu Khristu zikhale ndi mzimu wanu abale. Ameni.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.