Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
1 Samueli 8:4-11

Tsono akuluakulu onse a Israeli anasonkhana pamodzi ndipo anabwera kwa Samueli ku Rama. Iwo anati kwa iye “Taonani, inu mwakula tsopano ndipo ana anu sakutsata makhalidwe anu abwino. Tsono mutipatse mfumu kuti izitilamulira, monga momwe ikuchitira mitundu ina yonseyi.”

Koma mawu oti, “Mutipatse mfumu kuti izitilamulira,” sanakondweretse Samueli. Choncho anapemphera kwa Yehova. Yehova anamuyankha nati, “Mvera zonse zimene anthuwa akukuwuza. Si ndiwe amene akumukana, koma akukana Ine kuti ndikhale mfumu yawo. Kuyambira tsiku limene ndinawatulutsa mʼdziko la Igupto mpaka lero zochita zawo zakhala zondikana Ine nʼkumatumikira milungu ina. Tsopano akukukananso iwe. Tsono amvere zimene akunena, koma uwachenjeze kwambiri ndipo uwawuzitse za khalidwe la mfumu imene idzawalamulire.”

10 Samueli anawawuza anthu amene amamupempha mfumu aja mawu onse a Yehova. 11 Iye anati, “Zimene mfumu imene idzakulamulireniyo idzachite ndi izi: Izidzatenga ana anu aamuna kuti akhale ankhondo ake; ena pa magaleta ake, ena pa akavalo ake ndipo ena othamanga patsogolo pa magaleta akewo.

1 Samueli 8:12-15

12 Ena adzawayika kukhala olamulira asilikali 1,000, ena olamulira asilikali makumi asanu, ndi ena otipula minda yake, ndi kukolola ndiponso ena adzakhala osula zida zankhondo ndi zida za magaleta ake. 13 Iyo idzatenga ana anu akazi kuti akhale oyenga mafuta onunkhira, ophika chakudya ndi kupanga buledi. 14 Idzatenga minda yanu yabwino ya mpesa ndi ya mitengo ya olivi ndipo adzayipereka kwa antchito ake. 15 Idzatenga gawo lakhumi la tirigu wanu ndi mphesa zanu ndi kupereka kwa nduna zake ndi akapitawo ake.

1 Samueli 8:16-20

16 Mfumuyo idzatenga antchito anu aamuna ndi aakazi. Idzatenganso ngʼombe zanu zabwino ndi abulu anu nʼkumazingwiritsa ntchito. 17 Iyo idzatenga gawo lakhumi la zoweta zanu, ndipo inu eni mudzakhala akapolo ake. 18 Nthawi imeneyo ikadzafika inu mudzalira momvetsa chisoni chifukwa cha mfumu imene mwadzisankhira, koma Yehova sadzakuyankhani.”

19 Koma anthu anakana kumumvera Samueli. Iwo anati, “Ayi! Ife tikufuna mfumu yotilamulira. 20 Kotero ifenso tidzakhala ngati mayiko ena. Mfumu yathu idzatiweruza ndiponso idzatuluka nafe kutitsogolera kukamenya nkhondo.”

1 Samueli 11:14-15

14 Ndipo Samueli anati kwa anthuwo, “Tiyeni tipite ku Giligala kuti tikatsimikizenso kuti Sauli ndi mfumu yathu.” 15 Choncho anthu onse anapita ku Giligala ndipo kumeneko Samueli anakalonga Sauli ufumu pamaso pa Yehova. Pambuyo pake anthu anapereka nsembe zachiyanjano pamaso pa Yehova, ndipo Sauli ndi Aisraeli onse anachita chikondwerero chachikulu.

Masalimo 138

Salimo la Davide.

138 Ndidzakuyamikani Yehova ndi mtima wanga wonse;
    ndidzayimba nyimbo zokutamandani pamaso pa “milungu.”
Ndidzagwada kuyangʼana ku Nyumba yanu yoyera
    ndipo ndidzayamika dzina lanu
    chifukwa cha chikondi chanu ndi kukhulupirika kwanu,
pakuti Inu mwakuza dzina lanu ndi mawu anu
    kupambana zinthu zonse.
Pamene ndinayitana, munandiyankha;
    munandisandutsa wamphamvu ndi wolimba mtima.

Mafumu onse a dziko lapansi akuyamikeni Yehova,
    pamene amva mawu a pakamwa panu.
Iwo ayimbe za njira za Yehova,
    pakuti ulemerero wa Yehova ndi waukulu.

Ngakhale kuti Yehova ngokwezeka, amasamalira odzichepetsa,
    koma anthu onyada amawadziwira chapatali.
Ngakhale ndiyende pakati pa masautso,
    mumasunga moyo wanga;
mumatambasula dzanja lanu kutsutsana ndi mkwiyo wa adani anga,
    mumandipulumutsa ndi dzanja lanu lamanja.
Yehova adzakwaniritsa cholinga chake pa ine;
    chikondi chanu chosasinthika Yehova, ndi chosatha
    musasiye ntchito ya manja anu.

2 Akorinto 4:13-5:1

13 Kwalembedwa kuti, “Ndinakhulupirira; nʼchifukwa chake ndinayankhula.” Popeza ife tili ndi mtima womwewo wokhulupirira, ifenso timakhulupirira ndi kuyankhula, 14 chifukwa timadziwa kuti amene anaukitsa Ambuye Yesu kwa akufa adzatiukitsanso ife pamodzi ndi Yesu, natipereka ife ndi inu pamaso pake. 15 Zonsezi nʼkuti inu mupindule, kuti chisomochi chifikire anthu ochuluka kwambiri, amenenso adzathokoza mochuluka kwambiri ndi kupereka ulemerero kwa Mulungu.

16 Nʼchifukwa chake ife sititaya mtima. Ngakhale thupi lathu likunka lifowokerafowokera, koma mʼkatimu tikulimbikitsidwa mwatsopano tsiku ndi tsiku. 17 Pakuti masautso athu ndi opepuka ndi a kanthawi, koma akutitengera ulemerero wamuyaya umene ndi wopambana kwambiri. 18 Motero sitiyangʼana zinthu zimene ndi zooneka ndi maso, koma zinthu zimene ndi zosaoneka. Pakuti zimene zimaoneka ndi zosakhalitsa, koma zimene sizioneka ndi zamuyaya.

Matupi Atsopano

Popeza tikudziwa kuti ngati msasa wa dziko lapansi umene tikukhalamo uwonongeka, tili ndi nyumba yochokera kwa Mulungu, nyumba yamuyaya yakumwamba, osati yomangidwa ndi manja a anthu.

Marko 3:20-35

Yesu ndi Belezebabu

20 Pambuyo pake Yesu analowa mʼnyumba, ndipo gulu la anthu linasonkhananso, kotero kuti Iye pamodzi ndi ophunzira ake sanapeze mpata kuti adye. 21 Anthu a ku banja lake atamva zimenezi, anapita kuti akamutenga, pakuti ankanena kuti, “Wazungulira mutu.”

22 Ndipo aphunzitsi amalamulo omwe anachokera ku Yerusalemu anati, “Iye wagwidwa ndi Belezebabu! Ndi ulamuliro wa mkulu wa ziwanda akutulutsa ziwanda.”

23 Pamenepo Yesu anawayitana nawayankhula mʼmafanizo nati: “Kodi Satana angatulutse bwanji Satana? 24 Ngati ufumu ugawanikana mwa iwo okha, ufumu umenewo sungakhalitse. 25 Ngati nyumba igawanikana mwa iyo yokha, nyumba imeneyo singathe kuyima. 26 Ndipo ngati Satana adzitsutsa yekha sangathe kuyima; ulamuliro wake watha. 27 Kunena zoona, palibe munthu angalowe mʼnyumba ya munthu wamphamvu ndi kutenga katundu wake pokhapokha atayamba wamumanga munthu wamphamvuyo. Pamenepo akhoza kumubera. 28 Ndikukuwuzani zoona kuti machimo onse ndi zamwano zonse za anthu zidzakhululukidwa, 29 koma aliyense amene achitira mwano Mzimu Woyera sadzakhululukidwa pakuti wachita tchimo losatha.”

30 Ananena izi chifukwa anati, “Ali ndi mzimu woyipa.”

Amayi ndi Abale ake a Yesu

31 Pamenepo amayi ndi abale ake a Yesu anafika. Atayima kunja, anatuma wina kuti akamuyitane Iye. 32 Gulu la anthu linakhala momuzungulira Iye, ndipo anamuwuza kuti, “Amayi ndi abale anu ali panja akukufunani.”

33 Iye anafunsa kuti, “Amayi ndi abale anga ndi ndani?”

34 Pamenepo anayangʼana anthu amene anakhala momuzungurira ndipo anati, “Awa ndi amayi anga ndi abale anga! 35 Aliyense amene achita chifuniro cha Mulungu ndi mʼbale wanga ndi mlongo wanga ndi amayi anga.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.