Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Salimo la Davide.
138 Ndidzakuyamikani Yehova ndi mtima wanga wonse;
ndidzayimba nyimbo zokutamandani pamaso pa “milungu.”
2 Ndidzagwada kuyangʼana ku Nyumba yanu yoyera
ndipo ndidzayamika dzina lanu
chifukwa cha chikondi chanu ndi kukhulupirika kwanu,
pakuti Inu mwakuza dzina lanu ndi mawu anu
kupambana zinthu zonse.
3 Pamene ndinayitana, munandiyankha;
munandisandutsa wamphamvu ndi wolimba mtima.
4 Mafumu onse a dziko lapansi akuyamikeni Yehova,
pamene amva mawu a pakamwa panu.
5 Iwo ayimbe za njira za Yehova,
pakuti ulemerero wa Yehova ndi waukulu.
6 Ngakhale kuti Yehova ngokwezeka, amasamalira odzichepetsa,
koma anthu onyada amawadziwira chapatali.
7 Ngakhale ndiyende pakati pa masautso,
mumasunga moyo wanga;
mumatambasula dzanja lanu kutsutsana ndi mkwiyo wa adani anga,
mumandipulumutsa ndi dzanja lanu lamanja.
8 Yehova adzakwaniritsa cholinga chake pa ine;
chikondi chanu chosasinthika Yehova, ndi chosatha
musasiye ntchito ya manja anu.
Bokosi la Chipangano Libwerera ku Israeli
6 Bokosi la Yehova linakhala mʼdziko la Afilisti kwa miyezi isanu ndi iwiri. 2 Tsono Afilisti anayitana ansembe ndi amawula ndipo anati, “Tichite nalo chiyani Bokosi la Yehova? Tiwuzeni momwe tidzalitumizira ku malo ake.”
3 Iwo anayankha kuti, “Ngati mufuna kubweza Bokosi la Mulungu wa Israeli, musalitumize wopanda kanthu, koma muyesetse kulitumiza pamodzi ndi nsembe yopepesera machimo. Mukatero mudzachiritsidwa, ndipo mudzadziwa chifukwa chiyani chilango cha Yehova sichikukuchokani.”
4 Afilisti anafunsanso kuti “Kodi ife tipereke nsembe yanji yopepesera machimo?”
Iwo anayankha kuti, “Mupereke zifanizo zagolide za zithupsa zisanu ndi zamakoswe asanu malingana ndi chiwerengero cha akalonga a Afilisti popeza mliri womwewo wagwera inu ndi akalonga anu. 5 Mupange zifanizo za zithupsa zisanu ndi za makoswe asanu amene akuwononga dziko lanu ndipo mupereke ulemu kwa Israeli. Mwina adzaleka kuzunza inu, milungu yanu ndi dziko lanu. 6 Nʼchifukwa chiyani mukuwumitsa mitima monga anachita Aigupto ndi Farao? Mulungu atawalanga anthu a ku Igupto aja kodi suja anawalola Aisraeli kuti azipita ndipo anapitadi?
7 “Tsopano konzani galeta latsopano limodzi ndiponso ngʼombe ziwiri zazikazi zamkaka zimene sizinavalepo goli. Muzimangirire ngʼombezo ku ngoloyo, koma ana awo muwachotse ndi kuwasiya kwanu. 8 Mutenge Bokosi la Yehova ndi kuliyika pa galetapo ndipo pambali pake pakhale Bokosi, mʼmene muyikemonso zinthu zagolide zomwe mukutumiza kwa Iye monga nsembe yopepesera machimo. Kenaka, mulisiye lizipita. 9 Koma muziliyangʼana. Ngati lilondola njira yopita kwawo kwa Bokosilo mpaka ku Beti-Semesi ndiye kuti amene watichita zoyipa zazikulu zoterezi ndi Mulungu wa Israeli. Koma ngati silitero, ife tidzadziwa kuti sanali Mulungu wa Israeli amene watizunza koma kuti zinangochitika mwatsoka.”
10 Anthu aja anachitadi zimenezi. Anatenga ngʼombe zamkaka ziwiri nazimanga ku galeta lija. Koma ana awo anawatsekera mʼkhola. 11 Tsono anayika Bokosi la Yehova pa galeta pamodzi ndi bokosi limene munali makoswe agolide ndi zifanizo zawo za zithupsa. 12 Ngʼombe zija zinapita molunjika kutsata msewu wopita ku Beti Semesi zikulira njira yonse. Sizinakhotere kumanja kapena kumanzere. Akalonga a Afilisti anazitsatira mpaka mʼmalire a Beti-Semesi.
13 Nthawi imeneyi anthu a ku Beti-Semesi amakolola tirigu mʼchigwa ndipo pamene anayangʼana ndi kuona Bokosi la Chipangano likubwera anakondwa. 14 Galeta lija linafika ku munda wa Yoswa ku Beti-Semesi ndipo linayima. Kumeneko kunali mwala waukulu. Tsono anthu anawaza nkhuni galetalo, ndipo anapha ngʼombe zija ndi kuzipereka ngati nsembe zopsereza kwa Yehova. 15 Alevi nʼkuti atatsitsa Bokosi la Yehova, pamodzi ndi bokosi mmene munali zinthu zagolide, ndipo anawayika pa mwala uja waukulu. Tsiku limenelo anthu a ku Beti-Semesi anapereka nsembe yopsereza ndi nsembe zina kwa Yehova. 16 Atsogoleri asanu a Afilisti ataona izi anabwerera ku Ekroni tsiku lomwelo.
17 Zifanizo zagolide za zithupsa zimene Afilisti anatumiza ngati nsembe zopepesera machimo kwa Yehova zinkayimirira mizinda isanu iyi motere: chimodzi cha ku Asidodi, china cha ku Gaza ndi zina za ku Asikeloni, Gati ndi Ekroni. 18 Ndipo chiwerengero cha zifanizo za makoswe chinali chofanana ndi chiwerengero cha mizinda ya akalonga asanu a Afilisti. Mizindayi inali yotetezedwa bwino ndi ina yapamtetete. Mwala waukulu umene anayikapo Bokosi la Chipangano la Yehova mʼmunda mwa Yoswa ku Beti-Semesi uli ngati mboni mpaka lero.
4 Anthu ambiri ankasonkhana, ndipo pamene anthu ankabwera kwa Yesu kuchokera ku midzi, Iye anawawuza fanizo ili, 5 “Mlimi anapita kukafesa mbewu zake. Akufesa mbewuzo, zina zinagwa mʼmbali mwa njira; zinapondedwa, ndipo mbalame zamlengalenga zinadya. 6 Zina zinagwa pa thanthwe, ndipo pamene zinamera, zinafota chifukwa panalibe chinyezi. 7 Mbewu zina zinagwera pakati pa minga, zinakulira pamodzi ndi mingazo ndipo zinalepheretsa mmerawo kukula. 8 Mbewu zina zinagwera pa nthaka yabwino. Zinamera ndipo zinabala mowirikiza 100 kuposa zimene zinafesedwa zija.”
Atanena izi, anafuwula kuti, “Amene ali ndi makutu, amve.”
9 Ophunzira ake anamufunsa tanthauzo lake la fanizolo. 10 Iye anati, “Kudziwa zinsinsi za ufumu wa Mulungu kwapatsidwa kwa inu, koma kwa ena ndimawayankhula mʼmafanizo kuti,
“ngakhale akuona, asapenye;
ngakhale akumva, asazindikire.”
11 “Tanthauzo la fanizoli ndi ili: Mbewu ndi mawu a Mulungu. 12 Mbewu za mʼmbali mwa njira ndi anthu amene amamva mawu, ndipo kenaka mdierekezi amabwera ndi kuchotsa mawuwo mʼmitima mwawo kuti asakhulupirire ndi kupulumutsidwa. 13 Mbewu za pa thanthwe ndi anthu amene amalandira mawu mwachimwemwe pamene akumva, koma mawuwo sazika mizu. Iwo amakhulupirira kwa kanthawi, koma pa nthawi ya mayesero, amagwa. 14 Mbewu zimene zinagwa pakati pa minga zikuyimira anthu amene amamva mawu, koma akamayenda mʼnjira zawo amatsamwitsidwa ndi zodandaulitsa za moyo uno, chuma ndi zosangalatsa, ndipo iwo samakhwima. 15 Koma mbewu za pa nthaka yabwino zikuyimira anthu amene ali ndi mtima woona ndi wabwino, amene amamva mawu nawasunga, ndipo amalimbikira mpaka amabala zipatso.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.