Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Salimo la Davide.
138 Ndidzakuyamikani Yehova ndi mtima wanga wonse;
ndidzayimba nyimbo zokutamandani pamaso pa “milungu.”
2 Ndidzagwada kuyangʼana ku Nyumba yanu yoyera
ndipo ndidzayamika dzina lanu
chifukwa cha chikondi chanu ndi kukhulupirika kwanu,
pakuti Inu mwakuza dzina lanu ndi mawu anu
kupambana zinthu zonse.
3 Pamene ndinayitana, munandiyankha;
munandisandutsa wamphamvu ndi wolimba mtima.
4 Mafumu onse a dziko lapansi akuyamikeni Yehova,
pamene amva mawu a pakamwa panu.
5 Iwo ayimbe za njira za Yehova,
pakuti ulemerero wa Yehova ndi waukulu.
6 Ngakhale kuti Yehova ngokwezeka, amasamalira odzichepetsa,
koma anthu onyada amawadziwira chapatali.
7 Ngakhale ndiyende pakati pa masautso,
mumasunga moyo wanga;
mumatambasula dzanja lanu kutsutsana ndi mkwiyo wa adani anga,
mumandipulumutsa ndi dzanja lanu lamanja.
8 Yehova adzakwaniritsa cholinga chake pa ine;
chikondi chanu chosasinthika Yehova, ndi chosatha
musasiye ntchito ya manja anu.
4 Ndipo mawu a Samueli anafika kwa Aisraeli onse.
Afilisti Alanda Bokosi la Chipangano
Aisraeli anapita kukamenya nkhondo ndi Afilisti. Aisraeli anamanga misasa yawo ku Ebenezeri, ndipo Afilisti anamanga ku Afeki. 2 Afilisti anandanda kuyangʼana Aisraeli nayamba kumenyana. Nkhondo inakula ndipo Afilisti anagonjetsa Aisraeli napha anthu 4,000 pa malo a nkhondopo. 3 Asilikali atabwerera ku misasa, akuluakulu a Israeli anafunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani Yehova walola kuti tigonjetsedwe lero pamaso pa Afilisti? Tiyeni tikatenge Bokosi la Chipangano cha Yehova ku Silo kuti Yehovayo abwere kukhala pakati pathu ndi kutipulumutsa mʼmanja mwa adani athu.”
4 Choncho anatuma anthu ku Silo ndipo anakatenga Bokosi la Chipangano cha Yehova Wamphamvuzonse amene amakhala pa akerubi. Ndipo ana awiri a Eli, Hofini ndi Finehasi anatsagana nalo Bokosi la Chipangano cha Mulungu.
5 Bokosi la Chipangano cha Yehova litafika ku msasa, Aisraeli onse anafuwula kwambiri mpaka nthaka inagwedezeka. 6 Atamva kufuwulaku, Afilisti anafunsa, “Kodi kufuwula kwakukulu kumeneku ku misasa ya Ahebri ndi kwachiyani?”
Atamva kuti Bokosi la Yehova lafika ku msasako, 7 Afilisti anachita mantha pakuti iwo ankanena kuti, “Milungu yafika ku msasa. Iwo anati, ‘Tili pamavuto. Chinthu choterechi sichinachitikepo nʼkale lomwe. 8 Atsoka ife! Adzatipulumutsa ndani mʼmanja mwa milungu yamphamvuyi? Iyi ndi milungu imene inakantha Aigupto ndi miliri yosiyanasiyana mʼchipululu. 9 Limbani mtima Afilisti! Chitani chamuna, kuti mungakhale akapolo a Ahebri monga iwowa alili akapolo anu. Chitani chamuna ndipo menyani nkhondo!’ ”
10 Choncho Afilisti anamenya nkhondo, ndipo anagonjetsa Aisraeli. Iwo anathawa aliyense kwawo. Ankhondo a Aisraeli oyenda pansi okwanira 30,000 anaphedwa. 11 Ndipo Bokosi la Chipangano la Yehova linalandidwa, ndiponso ana awiri Eli, Hofini ndi Finehasi anaphedwa.
Imfa ya Eli
12 Tsiku lomwelo munthu wina wa fuko la Benjamini anathawa ku nkhondo ndipo anafika ku Silo. Iyeyu zovala zake zinali zongʼamba ndipo anadzithira dothi kumutu kuonetsa chisoni. 13 Atafika, anapeza Eli atakhala pa mpando wake mʼmbali mwa msewu, akungoyangʼana, pakuti ankadera nkhawa Bokosi la Mulungu. Munthuyo atalowa mu mzindamo ndi kufotokoza zimene zinachitika ku nkhondo, anthu onse a mu mzindamo anayamba kulira.
14 Eli atamva kulirako anafunsa kuti, “Kodi phokosoli likutanthauza chiyani?”
Tsono munthu wa fuko la Benjamini uja anapita msanga kwa Eli kukamufotokozera. 15 Nthawiyo nʼkuti Eli ali wa zaka 98 ndipo maso ake anali atachita khungu kotero kuti samatha kuona. 16 Munthuyo anamuwuza Eli kuti, “Ine ndabwera kuchokera ku nkhondo, ndathawako lero lomwe lino.”
Eli anafunsa, “Nanga nkhondo yayenda bwanji mwana wanga?”
17 Iye anayankha kuti, “Aisraeli athawa pamaso pa Afilisti. Anthu ambirimbiri aphedwa. Ana anunso Hofini ndi Finehasi aphedwa. Bokosi la Mulungu nalonso lalandidwa.”
18 Atangotchula Bokosi la Yehova, Eli anagwa chagada, kuchoka pa mpando wake umene unali mʼmbali mwa chitseko cha mpanda. Khosi lake linathyoka ndipo anafa, pakuti anali okalamba ndi onenepa kwambiri. Iye anatsogolera Israeli zaka makumi anayi.
19 Nthawiyo, mpongozi wa Eli, mkazi wa Finehasi anali woyembekezera ndipo anali pafupi kuchira. Atamva kuti Bokosi la Mulungu lalandidwa ndi kuti mpongozi wake Eli ndi mwamuna wake amwalira, ululu wa pobereka mwana unamufikira modzidzimutsa ndipo anabereka mwana. 20 Popeza mkaziyo anali pafupi kumwalira, akazi amene amamuthandiza anati, “Usaope, wabereka mwana wamwamuna” Koma iye sanayankhe kapena kulabadirako.
21 Tsono iye anatcha mwanayo dzina loti Ikabodi kutanthauza kuti, “Ulemerero wachoka mu Israeli,” chifukwa cha kulandidwa Bokosi la Mulungu ndi imfa ya mpongozi wake Eli ndi mwamuna wake. 22 Ananena momwemo kuti, “Ulemerero wachoka mu Israeli, pakuti Bokosi la Mulungu lalandidwa.”
7 Chimaliziro cha zinthu zonse chili pafupi. Choncho khalani maso ndi odziletsa kuti muthe kupemphera. 8 Koposa zonse muzikondana wina ndi mnzake kwambiri, chifukwa chikondi chimaphimba machimo ambiri. 9 Muzisamalirana wina ndi mnzake osamanyinyirika. 10 Aliyense agwiritse ntchito mokhulupirika mphatso iliyonse imene anayilandira potumikira ena ngati adindo ogwiritsa bwino ntchito mphatso za Mulungu za mitundumitundu. 11 Ngati wina ayankhula, ayankhuledi mawu enieni a Mulungu. Ngati wina atumikira, atumikire ndi mphamvu imene Mulungu amapereka, kuti pa zonse Mulungu alemekezedwe mwa Yesu Khristu. Kwa Iye kukhale ulemerero ndi mphamvu mpaka muyaya, Ameni.
Kumva Zowawa Chifukwa cha Chikhristu
12 Abale okondedwa musadabwe ndi mayesero owawa amene mukukumana nawo ngati kuti china chake chachilendo chakuchitikirani. 13 Koma kondwerani popeza mukumva zowawa pamodzi ndi Khristu, kuti mudzakondwere kwakukulu pamene ulemerero wake udzaonekera. 14 Ngati akuchitani chipongwe chifukwa cha dzina la Khristu, ndinu odala, ndiye kuti Mzimu waulemerero wa Mulungu uli pa inu. 15 Ngati mumva zowawa, zisakhale chifukwa cha kupha munthu, kapena kuba, kapena kuchita choyipa, kapena kulowerera za anthu ena, 16 koma ngati mumva zowawa chifukwa ndinu Mkhristu, musachite manyazi, koma muyamike Mulungu chifukwa cha dzinalo. 17 Pakuti nthawi yafika kuti chiweruzo chiyambe mʼnyumba ya Mulungu, ndipo ngati chiyamba ndi ife nanga podzafika kwa osamvera Uthenga Wabwino wa Mulungu, chidzakhala chotani? 18 Monga Malemba akuti,
“Ngati kuli kovuta kuti olungama apulumuke,
nanga munthu wochimwa, wosasamala za Mulungu adzatani?”
19 Nʼchifukwa chake, iwo amene akumva zowawa monga mwa chifuniro cha Mulungu, adzipereke okha mʼmanja mwa Mlengi wawo wokhulupirika ndi kumapitiriza kuchita zabwino.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.