Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.
139 Inu Yehova, mwandisanthula
ndipo mukundidziwa.
2 Inu mumadziwa pamene ndikhala pansi ndi pamene ndidzuka;
mumazindikira maganizo anga muli kutali.
3 Mumapenyetsetsa pamene ndikutuluka ndi kugona kwanga;
mumadziwa njira zanga zonse.
4 Mawu asanatuluke pa lilime langa
mumawadziwa bwinobwino, Inu Yehova.
5 Mumandizinga kumbuyo ndi kutsogolo komwe;
mwasanjika dzanja lanu pa ine.
6 Nzeru zimenezi ndi zopitirira nzeru zanga,
ndi zapamwamba kuti ine ndizipeze.
13 Pakuti Inu munalenga za mʼkati mwanga;
munandiwumba pamodzi mʼmimba mwa amayi anga.
14 Ndimakuyamikani chifukwa ndinapangidwa mochititsa mantha ndi modabwitsa;
ntchito zanu ndi zodabwitsa,
zimenezi ndimazidziwa bwino lomwe.
15 Mapangidwe anga sanabisike pamaso panu
pamene ndimapangidwa mʼmalo achinsinsi,
pamene ndinkawumbidwa mwaluso mʼmimba ya amayi anga.
16 Maso anu anaona thupi langa lisanawumbidwe.
Masiku onse amene anapatsidwa kwa ine, analembedwa mʼbuku lanu
asanayambe nʼkuwerengedwa komwe.
17 Zolingalira zanu pa ine ndi zamtengowapatali, Inu Mulungu,
ndi zosawerengeka ndithu!
18 Ndikanaziwerenga,
zikanakhala zochuluka kuposa mchenga;
pamene ndadzuka, ndili nanube.
19 Elikana ndi banja lake anadzuka mmawa mwake nakapemphera pamaso pa Yehova. Pambuyo pake anabwerera kwawo ku Rama. Elikana anakhala pamodzi ndi mkazi wake, ndipo Yehova anamukumbuka Hanayo. 20 Motero Hana anakhala ndi pakati ndipo anabereka mwana wamwamuna. Anamutcha dzina lake Samueli, popeza anati, “Ndinachita kumupempha kwa Yehova.”
Hana Apereka Samueli kwa Yehova
21 Elikana ndi banja lake lonse anapita kukapereka nsembe ya pa chaka kwa Yehova ndi kukakwaniritsa malonjezo ake. 22 Koma Hana sanapite nawo popeza anawuza mwamuna wake kuti, “Mwanayu akadzaleka kuyamwa, ndidzapita naye ndi kukamupereka pamaso pa Yehova ndipo adzakhala kumeneko moyo wake wonse.”
23 Elikana mwamuna wake anamuwuza kuti, “Chita chimene chakukomera. Tsala kuno mpaka utamusiyitsa kuyamwa, Yehova yekha akwaniritse mawu ake.” Choncho mkaziyo anatsala ku nyumba ndi kusamalira mwana wake mpaka atamuletsa kuyamwa.
24 Atamuletsa kuyamwa, Hana anatenga mwanayo ali wachichepere, ndikupita naye ku nyumba ya Yehova ku Silo. Anatenga ngʼombe yamphongo ya zaka zitatu, ufa wa makilogalamu khumi, ndi thumba lachikopa la vinyo. 25 Tsono anapha ngʼombe yamphongo ija ndi kupereka mwana uja kwa Eli. 26 Ndipo Hana anati kwa Eli, “Mbuye wanga, ine ndikunenetsadi pamaso panu kuti ndine mkazi uja amene anayima pamaso panu ndi kumapemphera kwa Yehova. 27 Ndinapempha mwana uyu, ndipo Yehova wandipatsa chimene ndinamupempha.
31 Nanga tsono tidzanena chiyani pa izi? Ngati Mulungu ali mbali yathu, adzatitsutsa ife ndani? 32 Iye amene sanatimane Mwana wake wa Iye yekha, koma anamupereka chifukwa cha ife tonse. Iye adzalekeranjinso pamodzi naye kutipatsa ife zinthu zonse mwaulere? 33 Ndani amene adzabweretsa mlandu kutsutsa amene Mulungu anawasankha? Ndi Mulungu amene amalungamitsa. 34 Ndani amene angatipeze ife olakwa? Palibe. Khristu Yesu amene anafa, kuposera pamenepo, amene anaukitsidwa ndi moyo, amene ali kudzanja lamanja la Mulungu ndiye amene akutipempherera. 35 Ndani amene adzatilekanitsa ife ndi chikondi cha Khristu? Kodi ndi masautso, kapena zowawa, kapena mazunzo, kapena njala, kapena umaliseche, kapena choopsa, kapena lupanga? 36 Monga kwalembedwa:
“Chifukwa cha inu, ife tikuphedwa tsiku lonse:
ife tikutengedwa ngati nkhosa zoti zikaphedwe.”
37 Ayi, mu zonsezi ife ndife oposa agonjetsi mwa Iye amene anatikonda. 38 Pakuti ine ndatsimikiza ndi mtima wonse kuti ngakhale imfa, kapena moyo, ngakhale angelo, kapena ziwanda, ngakhale zinthu zilipo, kapena zili mʼtsogolo, kapena mphamvu zina, 39 ngakhale kutalika, kapena kuya, kapena chilichonse mʼchilengedwe chonse, sizingathe kutisiyanitsa ndi chikondi cha Mulungu chimene chili mwa Khristu Yesu Ambuye athu.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.