Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Masomphenya a Yesaya
6 Chaka chimene mfumu Uziya anamwalira, ndinaona Ambuye atakhala pa mpando waufumu, wautali ndi wokwezedwa, ndipo mkanjo wawo unali wautali; kotero kuti unadzaza mʼNyumba ya Yehova. 2 Pamwamba pawo panayimirira Aserafi, aliyense anali ndi mapiko asanu ndi limodzi: awiri anaphimba nkhope zawo, awiri anaphimba mapazi awo, ndipo awiri ankawulukira. 3 Ndipo Aserafiwo amafuwulirana kuti
“Woyera, woyera, woyera Yehova Wamphamvuzonse.
Dziko lonse lapansi ladzaza ndi ulemerero wake.”
4 Chifukwa cha kufuwulako maziko a zitseko ndi ziwundo anagwedezeka ndipo mʼNyumba ya Yehova munadzaza utsi.
5 Tsono ine ndinafuwula kuti, “Tsoka langa ine! Ndatayika! Pakuti ndine munthu wapakamwa poyipa, ndipo ndimakhala pakati pa anthu a pakamwa poyipa, ndipo ndi maso anga ndaona mfumu Yehova Wamphamvuzonse.”
6 Pomwepo mmodzi mwa Aserafi aja anawulukira kwa ine ali ndi khala lamoto mʼdzanja lake, khala limene analichotsa ndi mbaniro pa guwa lansembe. 7 Ndipo anandikhudza pakamwa panga ndi khala lamotolo nati, “Taona ndakhudza pa milomo yako ndi khalali; kulakwa kwako kwachotsedwa, machimo ako akhululukidwa.”
8 Kenaka ndinamva mawu a Ambuye akuti, “Kodi ndidzatuma yani? Ndipo ndani adzapite mʼmalo mwathu?”
Ndipo ine ndinati, “Ndilipo. Tumeni!”
Salimo la Davide.
29 Perekani kwa Yehova, inu anthu amphamvu,
perekani kwa Yehova ulemerero ndi mphamvu.
2 Perekani kwa Yehova ulemerero woyenera dzina lake,
pembedzani Yehova mwa kukongola kwa chiyero chake.
3 Liwu la Yehova lili pamwamba pa madzi;
Mulungu waulemerero abangula,
Yehova abangula pamwamba pa madzi amphamvu.
4 Liwu la Yehova ndi lamphamvu;
liwu la Yehova ndi laulemerero.
5 Liwu la Yehova limathyola mikungudza;
Yehova amathyolathyola mikungudza ya ku Lebanoni.
6 Iye amachititsa Lebanoni kulumphalumpha ngati mwana wangʼombe,
Siriyoni ngati mwana wa njati:
7 Liwu la Yehova limakantha
ngati kungʼanima kwa mphenzi.
8 Liwu la Yehova limagwedeza chipululu;
Yehova amagwedeza chipululu cha Kadesi.
9 Liwu la Yehova limapindapinda mibawa
ndi kuyeretsa nkhalango.
Ndipo mʼNyumba mwake onse amafuwula kuti, “Ulemerero!”
10 Yehova amakhala pamwamba pa madzi osefukira,
Yehova ndiye mfumu kwamuyaya.
11 Yehova amapereka mphamvu kwa anthu ake;
Yehova amadalitsa anthu ake ndi mtendere.
12 Kotero abale, ife tili ndi zoti tikwaniritse, koma osati za khalidwe lathu lauchimo, kumachita zofuna zake. 13 Pakuti ngati inu mukhala monga mwa khalidwe lauchimo, mudzafa. Koma ngati mwa Mzimu mupha ntchito zoyipa zathupi, mudzakhala ndi moyo. 14 Onse amene amatsogozedwa ndi Mzimu wa Mulungu ndi ana a Mulungu. 15 Mzimu amene inu munalandira samakusandutsani akapolo, kuti muzikhalanso amantha, koma Mzimu amakusandutsani ana. Ndipo mwa Iye ife timafuwula kuti, “Abba, Atate.” 16 Mzimu mwini amavomerezana ndi mzimu wathu kuti ife ndife ana a Mulungu. 17 Tsono ngati tili ana ake, ndiye kuti ndife olowa mʼmalo a Mulungu ndi olowa mʼmalo pamodzi ndi Khristu. Ngati ife timva zowawa pamodzi ndi Khristu, tidzalandiranso ndi ulemerero womwe pamodzi naye.
Yesu Aphunzitsa Nekodimo za Kubadwa Kwatsopano
3 Ndipo panali Mfarisi wotchedwa Nekodimo, wa mʼgulu lolamulira la Ayuda. 2 Iye anabwera kwa Yesu usiku ndipo anati, “Rabi, ife tikudziwa kuti ndinu aphunzitsi wochokera kwa Mulungu, pakuti palibe amene angachite zizindikiro zodabwitsa zimene Inu mukuchita ngati Mulungu sali naye.”
3 Poyankha Yesu ananena kuti, “Zoonadi, Ine ndikukuwuza kuti, ngati munthu sabadwanso mwatsopano sangathe kuona ufumu wa Mulungu.”
4 Nekodimo anati, “Kodi munthu angabadwenso bwanji atakalamba? Kodi angalowe kachiwiri mʼmimba ya amayi ake kuti abadwenso?”
5 Yesu anayankha kuti, “Zoonadi, Ine ndikukuwuza kuti ngati munthu sabadwa mwa madzi ndi Mzimu Woyera, sangalowe mu ufumu wa Mulungu. 6 Thupi limabereka thupi, koma Mzimu amabereka mzimu. 7 Iwe usadabwe chifukwa ndakuwuza kuti, ‘Uyenera kubadwanso.’ 8 Mphepo imawomba kulikonse kumene ikufuna. Ungathe kumva kuwomba kwake, koma sungathe kudziwa kumene ikuchokera kapena kumene ikupita. Nʼchimodzimodzi ndi amene abadwa ndi Mzimu Woyera.”
9 Nekodimo anafunsa kuti, “Kodi izi zingatheke bwanji?”
10 Yesu anati, “Iwe mphunzitsi wa Israeli, kodi sukuzindikira zimenezi? 11 Zoonadi, Ine ndikukuwuza kuti ife tiyankhula zimene tikuzidziwa ndi kuchitira umboni zimene taziona, komabe inu simuvomereza umboni wathu. 12 Ine ndikuyankhula kwa iwe zinthu za dziko lapansi ndipo sukukhulupirira. Nanga kodi udzakhulupirira bwanji ngati nditayankhula zinthu zakumwamba? 13 Palibe wina aliyense anapita kumwamba, koma yekhayo amene watsika kuchokera kumwamba, Mwana wa Munthu. 14 Tsono monga Mose anapachika njoka mʼchipululu, moteronso Mwana wa Munthu ayenera kupachikidwa, 15 kuti aliyense amene akhulupirira Iye akhale ndi moyo wosatha.
16 “Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi, kotero anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira Iye asatayike koma akhale ndi moyo wosatha. 17 Pakuti Mulungu sanatume Mwana wake ku dziko lapansi, kuti akaweruze, koma kuti akapulumutse dziko lapansi.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.