Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Salimo la Davide.
29 Perekani kwa Yehova, inu anthu amphamvu,
perekani kwa Yehova ulemerero ndi mphamvu.
2 Perekani kwa Yehova ulemerero woyenera dzina lake,
pembedzani Yehova mwa kukongola kwa chiyero chake.
3 Liwu la Yehova lili pamwamba pa madzi;
Mulungu waulemerero abangula,
Yehova abangula pamwamba pa madzi amphamvu.
4 Liwu la Yehova ndi lamphamvu;
liwu la Yehova ndi laulemerero.
5 Liwu la Yehova limathyola mikungudza;
Yehova amathyolathyola mikungudza ya ku Lebanoni.
6 Iye amachititsa Lebanoni kulumphalumpha ngati mwana wangʼombe,
Siriyoni ngati mwana wa njati:
7 Liwu la Yehova limakantha
ngati kungʼanima kwa mphenzi.
8 Liwu la Yehova limagwedeza chipululu;
Yehova amagwedeza chipululu cha Kadesi.
9 Liwu la Yehova limapindapinda mibawa
ndi kuyeretsa nkhalango.
Ndipo mʼNyumba mwake onse amafuwula kuti, “Ulemerero!”
10 Yehova amakhala pamwamba pa madzi osefukira,
Yehova ndiye mfumu kwamuyaya.
11 Yehova amapereka mphamvu kwa anthu ake;
Yehova amadalitsa anthu ake ndi mtendere.
15 Ndipo munthu aliyense adzatsitsidwa,
anthu onse adzachepetsedwa,
anthu odzikuza adzachita manyazi.
16 Koma Yehova Wamphamvuzonse adzalemekezedwa chifukwa cha chiweruzo chake cholungama.
Ndipo Mulungu woyera adzadzionetsa kuti ndi woyera pochita chilungamo chake.
17 Tsono nkhosa zidzadya pamenepo ngati pabusa pawo;
ana ankhosa adzadya mʼmabwinja a anthu olemera.
18 Tsoka kwa amene amadzikokera tchimo ndi zingwe zachinyengo,
ndipo amadzikokera zoyipa ndi zingwe zokokera ngolo,
19 amene amanena kuti, “Yehova afulumire,
agwire ntchito yake mwamsanga
kuti ntchitoyo tiyione.
Ntchito zionekere,
zimene Woyerayo wa Israeli akufuna kuchita,
zichitike kuti tizione.”
20 Tsoka kwa amene zoyipa amaziyesa zabwino
ndipo zabwino amaziyesa zoyipa,
amene mdima amawuyesa kuwala
ndipo kuwala amakuyesa mdima,
amene zowawasa amaziyesa zotsekemera
ndipo zotsekemera amaziyesa zowawasa.
21 Tsoka kwa amene amadziona ngati anzeru
ndipo amadziyesa ochenjera.
22 Tsoka kwa zidakwa zimene zimayika mtima pa vinyo
ndipo ndi akatswiri posakaniza zakumwa,
23 amene amamasula olakwa chifukwa cha chiphuphu
koma amayipitsa mlandu wa munthu wosalakwa.
24 Nʼchifukwa chake monga momwe moto umawonongera chiputu
ndipo monga momwe udzu wowuma umapsera mʼmalawi a moto,
momwemonso mizu yawo idzawola
ndipo maluwa awo adzafota ndi kuwuluka ngati fumbi;
chifukwa akana malamulo a Yehova Wamphamvuzonse,
ndipo anyoza mawu a Woyerayo wa Israeli.
Dziko Lapansi Limada Ophunzira a Yesu
18 “Ngati dziko lapansi lidana nanu, dziwani kuti linayamba kudana ndi Ine. 19 Inu mukanakhala anthu a dziko lapansi, dziko lapansi likanakukondani ngati anthu ake omwe. Koma mmene zilili, inu si anthu a dziko lapansi. Ine ndakusankhani kuchokera mʼdziko lapansi, nʼchifukwa chake dziko lapansi limakudani. 20 Kumbukirani mawu amene ndinayankhula nanu akuti, ‘Palibe wantchito amene amaposa bwana wake.’ Ngati anandizunza Ine, iwo adzakuzunzaninso inu. Ngati anamvera chiphunzitso changa, iwo adzamvera chanunso.
Ntchito ya Mzimu Woyera
26 “Nkhoswe ikadzabwera imene Ine ndidzakutumizireni kuchokera kwa Atate, ndiye Mzimu Woyera wachoonadi amene achokera kwa Atate, Iyeyo adzandichitira umboni Ine. 27 Inunso mudzandichitira umboni Ine, popeza mwakhala nane kuchokera pachiyambi.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.