Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 22:25-31

25 Ndidzakutamandani pa msonkhano waukulu chifukwa cha zimene mwandichitira.
    Ndidzakwaniritsa lonjezo langa pamaso pa amene amaopa Inu.
26 Osauka adzadya ndipo adzakhuta;
    iwo amene amafunafuna Yehova adzamutamanda.
    Mitima yanu ikhale ndi moyo mpaka muyaya!
27 Malekezero onse a dziko lapansi
    adzakumbukira Yehova ndi kutembenukira kwa Iye,
ndipo mabanja a mitundu ya anthu
    adzawerama pamaso pake,
28 pakuti ulamuliro ndi wake wa Yehova
    ndipo Iye amalamulira anthu a mitundu yonse.

29 Anthu olemera onse a dziko lapansi adzachita phwando ndi kulambira;
    onse amene amapita ku fumbi adzagwada pamaso pake;
    iwo amene sangathe kudzisunga okha ndi moyo.
30 Zidzukulu zamʼtsogolo zidzamutumikira Iye;
    mibado ya mʼtsogolo idzawuzidwa za Ambuye.
31 Iwo adzalengeza za chilungamo chake
    kwa anthu amene pano sanabadwe
    pakuti Iye wachita zimenezi.

Amosi 9:7-15

“Kodi kwa Ine, inu Aisraeli, simuli
    chimodzimodzi ndi Akusi?”
            Akutero Yehova.
“Kodi sindine amene ndinatulutsa Israeli ku Igupto,
    Afilisti ku Kafitori
    ndi Aaramu ku Kiri?

“Taonani, maso a Ambuye Yehova
    ali pa ufumu wochimwawu.
Ndidzawufafaniza
    pa dziko lapansi.
Komabe sindidzawononga kotheratu
    nyumba ya Yakobo,”
            akutero Yehova.
“Pakuti ndidzalamula,
    ndipo ndidzagwedeza nyumba ya Israeli
    pakati pa mitundu yonse ya anthu
monga momwe amasefera ufa mʼsefa,
    koma palibe nʼkamwala kamodzi komwe kamene kadzagwe pansi.
10 Anthu onse ochimwa pakati pa anthu anga
    adzaphedwa ndi lupanga,
onse amene amanena kuti,
    ‘Tsoka silidzatigwera ife kapena kutiwononga.’

Kubwezeretsedwa kwa Israeli

11 “Tsiku limenelo ndidzabwezeretsa
    nyumba ya Davide imene inagwa.
Ndidzakonzanso malo amene anagumuka,
    ndi kuyimanganso
    monga inalili poyamba,
12 kuti adzatengenso otsala a Edomu
    ndi mitundu yonse imene imatchedwa ndi dzina langa,”
            akutero Yehova amene adzachita zinthu izi.

13 Yehova akunena kuti

“Nthawi ikubwera pamene mlimi wotipula adzapyola wokolola
    ndipo woponda mphesa adzapyola wodzala mbewu.
Mapiri adzachucha vinyo watsopano
    ndi kuyenderera pa zitunda zonse.
14 Ndidzawabwezeranso pabwino anthu anga Aisraeli;
    mizinda imene inali mabwinja idzamangidwanso ndipo azidzakhalamo.
Adzalima minda ya mpesa ndipo adzamwa vinyo wake;
    adzalima minda ndipo adzadya zipatso zake.
15 Ndidzakhazika Aisraeli mʼdziko mwawo,
    ndipo sadzachotsedwamonso mʼdziko
    limene Ine ndawapatsa,”

            akutero Yehova Mulungu wako.

Marko 4:30-32

Fanizo la Mbewu ya Mpiru

30 Ndipo anatinso, “Kodi tinene kuti ufumu wa Mulungu ufanana ndi chiyani, kapena ndi fanizo lotani limene tidzagwiritsa ntchito pakuwufotokozera? 31 Uli ngati mbewu ya mpiru imene ndi mbewu yayingʼono kwambiri yomwe mumadzala mʼnthaka. 32 Koma ikadzalidwa, imakula ndi kukhala yayikulu koposa mbewu zina zonse za mʼmunda ndipo mʼnthambi zake zazikulu mbalame zamlengalenga zimadzapuma pa mthunzi wake.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.