Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
135 Tamandani Yehova.
Tamandani dzina la Yehova;
mutamandeni, inu atumiki a Yehova,
2 amene mumatumikira mʼnyumba ya Yehova,
mʼmabwalo a nyumba ya Mulungu wathu.
3 Tamandani Yehova, pakuti Yehova ndi wabwino;
imbani nyimbo zotamanda dzina lake, pakuti nʼkokoma kutero,
4 Pakuti Yehova wasankha Yakobo kuti akhale wake,
Israeli kuti akhale chuma chake chapamtima.
5 Ndikudziwa kuti Yehova ndi wamkulu,
kuti Ambuye athu ndi wamkulu kuposa milungu yonse.
6 Yehova amachita chilichonse chimene chimamukomera,
kumwamba ndi dziko lapansi,
ku nyanja zazikulu ndi ku malo ake onse akuya.
7 Iye amatulutsa mitambo kuchokera ku malekezero a dziko lapansi,
amatumiza zingʼaningʼani pamodzi ndi mvula
ndipo amatulutsa mphepo ku malo ake osungiramo.
8 Anakantha ana oyamba kubadwa a Igupto,
ana oyamba kubadwa a anthu ndi nyama.
9 Iye anatumiza zizindikiro zozizwitsa ndi zodabwitsa pakati pako, iwe Igupto,
kutsutsana ndi Farao pamodzi ndi atumiki ake onse.
10 Iye anakantha mitundu yambiri ya anthu
ndi kupha mafumu amphamvu:
11 Sihoni mfumu ya Aamori,
Ogi mfumu ya Basani,
ndi maufumu onse a ku Kanaani;
12 ndipo anapereka dziko lawo ngati cholowa,
cholowa cha anthu ake Aisraeli.
13 Dzina lanu, Inu Yehova, ndi losatha mpaka muyaya,
mbiri yanu, Inu Yehova, idziwika mibado yonse.
14 Pakuti Yehova adzaonetsa kuti anthu ake ngosalakwa,
ndipo adzachitira chifundo atumiki ake.
15 Mafano a mitundu ya anthu ndi siliva ndi golide,
opangidwa ndi manja a anthu.
16 Pakamwa ali napo koma sayankhula
maso ali nawo, koma sapenya;
17 makutu ali nawo, koma sakumva
ndipo mʼkamwa mwawo mulibe mpweya uliwonse.
18 Iwo amene amapanga mafanowo adzakhala ngati mafanowo,
chimodzimodzinso iwo amene amadalira mafanowo.
19 Inu nyumba ya Israeli, tamandani Yehova;
inu nyumba ya Aaroni, tamandani Yehova;
20 Inu nyumba ya Levi, tamandani Yehova;
Inu amene mumaopa Iye, tamandani Yehova.
21 Wodalitsika ndi Yehova kuchokera mʼZiyoni,
amene amakhala mu Yerusalemu.
Tamandani Yehova.
Nyimbo ya Matamando
26 Tsiku limenelo anthu a mʼdziko la Yuda adzayimba nyimbo iyi.
Tili ndi mzinda wolimba.
Mulungu amawuteteza ndi zipupa
ndi malinga.
2 Tsekulani zipata za mzinda
kuti mtundu wolungama
ndi wokhulupirika ulowemo.
3 Inu mudzamupatsa munthu
wa mtima wokhazikika
mtendere weniweni.
4 Mudalireni Yehova mpaka muyaya,
chifukwa Yehova Mulungu ndiye Thanthwe losatha.
5 Iye amatsitsa anthu amene amadziyika pamwamba,
iye amagwetsa pansi mzinda wodzitukumula,
amagumula makoma ake
ndi kuwagwetsa pansi pa fumbi penipeni.
6 Mapazi a anthu akuwupondereza,
mapazi a anthu oponderezedwa,
mapazi anthu osauka.
7 Njira ya munthu wolungama ndi yosalaza,
Inu Wolungamayo, mumasalaza njira ya wolungama.
8 Inde Yehova, timayenda mʼnjira zanu zolungama,
ife timayembekezera Inu;
mitima yathu imakhumba kukumbukira
ndi kulemekeza dzina lanu.
9 Moyo wanga umalakalaka Inu usiku wonse;
nthawi yammawa ndimafunafuna Inu.
Pamene muweruza dziko lapansi
anthu amaphunzira kuchita chilungamo.
10 Ngakhale mukomere mtima anthu oyipa,
saphunzira chilungamo.
Amachita zoyipa mʼdziko la chilungamo,
ndipo sazindikira ululu wa Yehova.
11 Inu Yehova, mwatukula dzanja lanu kuti muwalange,
koma iwo sakuliona dzanjalo.
Aloleni anthu aone ndi kuchita manyazi poona mmene mukondera anthu anu;
ndipo moto umene mwasonkhera adani anu uwapsereze.
12 Yehova, mumatipatsa mtendere;
ndipo zonse zimene ife tinazichita munatichitira ndinu.
13 Inu Yehova Mulungu wathu, ngakhale takhala tikulamulidwa ndi ena mʼmalo mwanu,
koma ife timalemekeza dzina lanu lokha.
14 Iwo tsopano sadzadzukanso;
mizimu yawo sidzabwera kudzativutitsa
pakuti mwawalanga ndipo mwawawononga;
palibenso amene amawakumbukira.
15 Inu Yehova, mwaukulitsa mtundu wathu;
mwauchulukitsa ndithu
ndipo mwalandirapo ulemu;
mwaukuza mbali zonse za dziko.
Za Ukwati ndi Kuuka kwa Akufa
18 Kenaka Asaduki, amene amati kulibe kuuka kwa akufa, anabwera kwa Iye ndi funso. 19 Iwo anati, “Aphunzitsi, Mose anatilembera kuti munthu akamwalira ndi kusiya mkazi wopanda ana, mʼbale wa munthu womwalirayo akuyenera kukwatira mkaziyo kuti amuberekere ana mʼbale wakeyo. 20 Tsopano panali abale asanu ndi awiri. Woyamba anakwatira namwalira wosabereka ana. 21 Wachiwiri anakwatira mkazi wamasiyeyo, koma iye anamwalira wosabereka mwana. Zinali chimodzimodzi ndi wachitatu. 22 Kunena zoona, palibe ndi mmodzi yemwe wa asanu ndi awiriwo anasiya ana. Pomaliza, mkaziyo anamwaliranso. 23 Pa kuuka kwa akufa, adzakhala mkazi wa yani pakuti anakwatiwa ndi onse asanu ndi awiri?”
24 Yesu anawafunsa kuti, “Kodi si pamenepa nanga pomwe mumalakwira chifukwa simukudziwa malemba kapena mphamvu za Mulungu? 25 Pamene akufa auka, sadzakwatira kapena kukwatiwa; adzakhala ngati angelo kumwamba. 26 Tsopano kunena zakuti akufa amauka, kodi simunawerenge mʼbuku la Mose, pa nkhani yachitsamba choyaka moto, mmene Mulungu anati kwa iye, ‘Ine ndine Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isake, ndi Mulungu wa Yakobo?’ 27 Iye si Mulungu wa anthu akufa, koma wa amoyo. Inu mwalakwitsa kwambiri!”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.