Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 118:1-2

118 Yamikani Yehova chifukwa ndi wabwino;
    pakuti chikondi chake chosasinthika ndi chosatha.

Israeli anene kuti:
    “Chikondi chake ndi chosatha.”

Masalimo 118:14-24

14 Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga;
    Iye wakhala chipulumutso changa.

15 Mfuwu wachimwemwe ndi chipambano
    ukumveka mʼmatenti a anthu olungama mtima kuti:
“Dzanja lamanja la Yehova lachita zamphamvu!
16     Dzanja lamanja la Yehova latukulidwa mmwamba
    Dzanja lamanja la Yehova lachita zamphamvu!”

17 Sindidzafa koma ndidzakhala ndi moyo
    ndipo ndidzalalika za ntchito ya Yehova.
18 Yehova wandilanga koopsa,
    koma sanandipereke ku imfa.

19 Tsekulireni zipata zachilungamo,
    kuti ndifike kudzayamika Yehova.
20 Ichi ndicho chipata cha Yehova
    chimene olungama mtima okha adzalowerapo.
21 Ndidzakuyamikani chifukwa Inu munandiyankha;
    mwakhala chipulumutso changa.

22 Mwala umene amisiri omanga nyumba anawukana
    wasanduka wapangodya;
23 Yehova ndiye wachita zimenezi
    ndipo nʼzodabwitsa pamaso pathu.
24 Lero ndiye tsiku limene Yehova walipanga;
    tiyeni tikondwere ndi kusangalala nalo.

Genesis 1:1-19

Chiyambi cha Chilengedwe

Pachiyambi Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi. Dziko lapansi linali losakonzedwa ndi lopanda kanthu. Mdima wandiweyani unakuta nyanja ndipo Mzimu wa Mulungu unkayendayenda pamwamba pa madziwo.

Pamenepo Mulungu anati, “Kuwale” ndipo kunawaladi. Mulungu anaona kuti kuwalako kunali bwino ndipo Iye analekanitsa kuwala ndi mdima. Mulungu anatcha kuwalako “usana” ndipo mdima anawutcha “usiku.” Ndipo panali madzulo ndiponso mmawa pa tsiku loyamba.

Kenaka Mulungu anati, “Pakhale thambo pakati pa madzi kuti lilekanitse madzi a mʼmwamba ndi madzi a pansi.” Ndipo Mulungu anapanga thambo nalekanitsa madzi amene anali pansi ndi pamwamba pa thambo lija, ndipo zinachitikadi. Mulungu anatcha thambo lija “kumwamba.” Ndipo panali madzulo ndiponso mmawa pa tsiku lachiwiri.

Mulungu anati, “Madzi a pansi pa thambo asonkhane pa malo amodzi kuti mtunda uwoneke,” ndipo zinachitikadi. 10 Mulungu anawutcha mtundawo “dziko,” madzi osonkhana pamodziwo anawatcha “nyanja.” Ndipo Mulungu anaona kuti zinali bwino.

11 Kenaka Mulungu anati, “Dziko libereke zomera zobala mbewu, mitengo yobala zipatso za mbewu, molingana ndi mitundu yake.” Ndipo zinachitikadi. 12 Dziko linabereka zomera zokhala ndi mbewu monga mwa mitundu yake ndi mitengo yokhala ndi zipatso za mbewu mʼkati mwake monga mwa mitundu yake. Ndipo Mulungu anaona kuti zinali bwino. 13 Ndipo panali madzulo ndiponso mmawa pa tsiku lachitatu.

14 Mulungu anati, “Pakhale zowunikira kuthambo kuti zilekanitse usana ndi usiku. Ndipo zimenezi zikhale zizindikiro zoonetsa nyengo, masiku ndi zaka; 15 zikhale kuthambo kuti ziwunikire pa dziko lapansi. Ndipo zinachitikadi.” 16 Mulungu anapanga zowunikira zazikulu ziwiri; chachikulu chilamulire usana ndi chachingʼono chilamulire usiku. Iye anapanganso nyenyezi. 17 Mulungu anaziyika mlengalenga kuti ziziwunikira pa dziko lapansi, 18 kuti zilamulire usana ndi usiku, ndi kuti zilekanitse kuwala ndi mdima. Mulungu anaona kuti zinali bwino. 19 Ndipo panali madzulo ndiponso mmawa pa tsiku lachinayi.

1 Akorinto 15:35-49

Kuukitsidwa kwa Thupi

35 Koma wina akhoza kufunsa kuti, “Kodi akufa amaukitsidwa motani? Adzauka ndi thupi la mtundu wanji?” 36 Wopusa iwe! Chimene mudzala sichikhala ndi moyo pokhapokha chitayamba chafa. 37 Mukadzala, simudzala thupi limene lidzamere, koma mbewu chabe, mwina ya tirigu kapena ya china chake. 38 Koma Mulungu amayipatsa thupi monga Iye wafunira, ku mbewu ya mtundu uliwonse amapereka thupi lakelake. 39 Mnofu siwofanana. Anthu ali ndi mnofu wa mtundu wina, nyama zili ndi wina, mbalame zili ndi wina, nsomba zili ndi winanso. 40 Palinso matupi akumwamba ndipo palinso matupi a dziko lapansi; koma ulemerero wa matupi akumwamba ndi wina, ndi wa matupi a dziko lapansi ndi winanso. 41 Dzuwa lili ndi ulemerero wake, ndipo pali ulemerero wina wa mwezi, palinso ulemerero winanso wa nyenyezi. Ulemerero wa nyenyezi ndi wosiyanasiyana.

42 Zidzaterenso pamene akufa adzauka. Thupi loyikidwa mʼnthaka ngati mbewu limavunda, koma likadzauka lidzakhala losavunda. 43 Limayikidwa mʼmanda mopanda ulemu, koma likadzaukitsidwa lidzakhala ndi ulemerero. Limayikidwa mʼmanda lili lofowoka, koma likadzaukitsidwa lidzakhala ndi mphamvu. 44 Limayikidwa mʼmanda thupi la mnofu chabe, koma likadzaukitsidwa lidzakhala lauzimu.

Ngati pali thupi la mnofu, palinso thupi lauzimu. 45 Kwalembedwa kuti, “Munthu woyamba Adamu anakhala wamoyo,” Adamu wotsiriza anakhala wopatsa moyo. 46 Zauzimu sizinabwere koyambirira, koma zachilengedwe, pambuyo pake zauzimu. 47 Munthu woyamba anali wa dziko lapansi, wochokera mʼnthaka koma munthu wachiwiri anali wochokera kumwamba. 48 Monga analili munthu wa dziko lapansi, momwemonso anthu onse amene ndi a dziko lapansi. Ndipo monga alili munthu wakumwamba, momwemonso anthu onse amene ndi akumwamba. 49 Ndipo monga momwe tinabadwa ofanana ndi munthu wa dziko lapansi uja, momwemonso tidzakhala ofanana ndi munthu wakumwamba.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.