Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
14 “Munthu wobadwa mwa amayi
amakhala masiku owerengeka ndipo ndi odzaza ndi mavuto okhaokha.
2 Amaphuka ngati duwa ndipo kenaka amafota;
amathawa ngati mthunzi ndipo sakhalitsa.
3 Kodi munthu wotereyo nʼkumuyangʼanitsitsa?
Kodi mungamubweretse pamaso panu kuti mumuzenge mlandu?
4 Ndani angatulutse chabwino mʼchoyipa?
Palibe ndi mmodzi yemwe!
5 Masiku a munthu ndi odziwikiratu;
munakhazikitsa chiwerengero cha miyezi yake
ndipo munamulembera malire amene sangathe kuwalumpha.
6 Choncho Inu mumufulatire ndipo mumuleke apumule
kufikira atakondwera nawo moyo ngati munthu waganyu.
7 “Mtengo uli nacho chiyembekezo:
ngati wadulidwa, udzaphukiranso
ndipo nthambi zake sizidzaleka kuphukira.
8 Mizu yake ingathe kukalamba mʼnthaka
ndipo chitsa chake nʼkuwola pa dothi,
9 koma pamene chinyontho chafika udzaphukira
ndipo udzaphuka nthambi ngati mtengo wanthete.
10 Koma munthu amafa nayikidwa mʼmanda,
amapuma mpweya wotsiriza ndipo kutha kwake nʼkomweko.
11 Monga madzi amaphwera mʼnyanja
kapena monga mtsinje umaphwera nuwuma,
12 momwemonso munthu amagona ndipo sadzukanso;
mpaka zamlengalenga zidzathe, anthu sadzauka
kapena kudzutsidwa ku tulo tawo.
13 “Aa, Inu mukanangondibisa mʼmanda
ndi kundiphimba kuti ndisaoneke mpaka mkwiyo wanu utapita!
Achikhala munandiyikira nthawi,
kuti pambuyo pake mundikumbukirenso.
14 Munthu akafa, kodi adzakhalanso ndi moyo?
Masiku anga onse a moyo wovutikawu
ndidzadikira mpaka itafika nthawi yomasulidwa.
3 Ine ndine munthu amene ndaona masautso
ndi ndodo ya ukali wake.
2 Wandipititsa kutali ndipo wandiyendetsa
mu mdima osati mʼkuwala;
3 zoonadi anandikantha ndi dzanja lake
mobwerezabwereza tsiku lonse.
4 Wakalambitsa khungu langa ndi mnofu wanga,
ndipo waphwanya mafupa anga.
5 Wandizinga ndi kundizungulira
ndi zowawa ndi zolemetsa.
6 Wandikhazika mu mdima
ngati amene anafa kale.
7 Wandimangira khoma kotero kuti sindingathawe,
wandimanga ndi maunyolo.
8 Ngakhale pamene ndifuwula kapena kupempha chithandizo,
amakana pemphero langa.
9 Wanditsekera njira yanga ndi miyala yosema;
ndipo wakhotetsa tinjira tanga.
19 Kukumbukira masautso anga ndi kusowa pokhala,
zili ngati zowawa ndi ndulu.
20 Ine ndikuzikumbukira bwino izi,
ndipo moyo wanga wathedwa mʼkati mwanga.
21 Komabe ndimakumbukira zimenezi,
nʼchifukwa chake ndili ndi chiyembekezo.
22 Ife sitinawonongekeretu chifukwa chikondi cha Yehova ndi chachikulu,
ndi chifundo chake ndi chosatha.
23 Zimaoneka zatsopano mmawa uliwonse;
kukhulupirika kwanu nʼkwakukulu.
24 Mu mtima mwanga ndimati, “Yehova ndiye zanga zonse;
motero ndimamuyembekezera.”
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.
31 Mwa Inu Yehova, ine ndimathawiramo;
musalole nʼkomwe kuti ndichititsidwe manyazi;
mundipulumutse chifukwa cha chilungamo chanu.
2 Tcherani khutu lanu kwa ine,
bwerani msanga kudzandilanditsa;
mukhale thanthwe langa lothawirapo,
linga lolimba kundipulumutsa ine.
3 Popeza Inu ndinu thanthwe langa ndi linga langa,
chifukwa cha dzina lanu tsogolereni ndi kundiwongolera.
4 Ndimasuleni mu msampha umene anditchera
pakuti ndinu pothawirapo panga.
15 Masiku anga ali mʼmanja mwanu;
ndipulumutseni kwa adani anga
ndi kwa iwo amene akundithamangitsa.
16 Walitsani nkhope yanu pa mtumiki wanu;
pulumutseni mwa chikondi chanu chosatha.
Moyo Watsopano
4 Popeza kuti Khristu anamva zowawa mʼthupi lake, mukhale nawonso mtima omwewo, chifukwa iye amene wamva zowawa mʼthupi lake walekana nawo uchimo. 2 Chifukwa cha ichi, iwo sakhalanso moyo wawo akuchita zofuna za matupi awo, koma amachita chifuniro cha Mulungu. 3 Pakuti mwataya kale nthawi yambiri mʼmbuyomu pochita zimene anthu osapembedza amachita, moyo wokhumba zonyansa, zilakolako zoyipa kuledzera, zochitika zoyipa za pa phwando, mapokoso ndi kupembedza mafano onyansa. 4 Anthu osapembedza amadabwa pamene simuthamangira nawo kuchita zoyipitsitsazi, nʼchifukwa chake amakuchitani chipongwe. 5 Koma adzafotokoza okha mlandu wawo kwa Mulungu amene wakonzeka kuweruza amoyo ndi akufa. 6 Pa chifukwa chimenechi, Uthenga Wabwino unalalikidwa ngakhale kwa iwo amene tsopano ndi akufa, kuti adzaweruzidwe monga anthu ku thupi, koma adzakhale ndi moyo monga mwa Mulungu mu mzimu.
7 Chimaliziro cha zinthu zonse chili pafupi. Choncho khalani maso ndi odziletsa kuti muthe kupemphera. 8 Koposa zonse muzikondana wina ndi mnzake kwambiri, chifukwa chikondi chimaphimba machimo ambiri.
Yesu Ayikidwa Mʼmanda
57 Pamene kumada, kunabwera munthu wolemera wa ku Arimateyu dzina lake Yosefe amene anali wophunzira wa Yesu. 58 Anapita kwa Pilato kukapempha mtembo wa Yesu, ndipo Pilato analamula kuti uperekedwe kwa iye. 59 Yosefe anatenga mtembowo, nawukulunga nsalu yabafuta. 60 Ndipo anawuyika mʼmanda ake atsopano amene anasema mu thanthwe, natsekapo ndi mwala waukulu pa khomo la mandawo nachokapo. 61 Mariya wa Magadala ndi Mariya wina anakhala pansi moyangʼanizana ndi mandawo.
Alonda a pa Manda
62 Litapita tsiku lokonzekera Sabata, mmawa mwake, akulu a ansembe ndi Afarisi anapita kwa Pilato. 63 Iwo anati, “Bwana takumbukira kuti munthu wonyenga uja akanali ndi moyo anati, ‘Pakatha masiku atatu ndidzauka.’ 64 Choncho lamulirani kuti manda ake atetezedwe mpaka pa tsiku lachitatu. Chifukwa tikapanda kutero, ophunzira ake angabwere kudzaba mtembo wake ndipo angawuze anthu kuti waukitsidwa kwa akufa. Ndipo chinyengo chomalizachi chidzakhala choyipa kwambiri kusiyana ndi choyamba chija.”
65 Pilato anayankha kuti, “Tengani mlonda kalondereni monga mudziwira.” 66 Tsono anapita nakatseka manda kolimba ndi kuyikapo chizindikiro ndipo anayikapo mlonda.
Yesu Ayikidwa Mʼmanda
38 Kenaka, Yosefe wa ku Arimateyu anakapempha mtembo wa Yesu kwa Pilato. Tsono Yosefe anali wophunzira wa Yesu koma mobisa chifukwa iye ankaopa Ayuda. Atalandira chilolezo kwa Pilato, anakatsitsa mtembo wa Yesu. 39 Nekodimo, munthu amene poyamba pake anabwera kwa Yesu usiku, anatenga mafuta osakaniza ndi mure ndi aloe wolemera pafupifupi makilogalamu 32. 40 Pamenepo anatenga mtembo wa Yesu nawukulunga pamodzi ndi zonunkhiritsa mu nsalu za mtundu woyera monga mwa mwambo wa maliro wa Ayuda. 41 Pamalo pamene anapachikidwa Yesu panali munda ndipo mʼmundamo munali manda atsopano mʼmene munali simunayikidwemo aliyense. 42 Chifukwa linali Tsiku la Ayuda Lokonzekera ndi kuti mandawo anali pafupipo, iwo anayika Yesu mʼmenemo.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.