Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Yesaya 50:4-9

Ambuye Yehova anandiphunzitsa mawu oyenera kuyankhula
    kudziwa mawu olimbitsa mtima anthu ofowoka.
Mmawa mulimonse amandidzutsa,
    amathwetsa khutu langa kuti ndimve monga amachitira munthu amene akuphunzira.
Ambuye Yehova wanditsekula makutu anga,
    ndipo sindinakhale munthu wowukira
    ndipo sindinabwerere mʼmbuyo.
Ndinapereka msana wanga kwa ondimenya
    masaya anga ndinawapereka kwa anthu ondizula ndevu;
sindinawabisire nkhope yanga
    anthu ondinyoza ndi ondilavulira.
Popeza Ambuye Yehova amandithandiza,
    sindidzachita manyazi.
Tsono ndalimba mtima ngati msangalabwi,
    chifukwa ndikudziwa kuti sindidzachita manyazi.
Wondikhalira kumbuyo ali pafupi,
    ndaninso amene adzandiyimba mlandu?
    Abwere kuti tionane maso ndi maso!
Mdani wanga ndi ndani?
    Abweretu kuti tilimbane!
Ambuye Yehova ndiye amene amandithandiza.
    Ndaninso amene adzanditsutsa?
Onse adzatha ngati chovala
    chodyedwa ndi njenjete.

Masalimo 70

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Pempho.

70 Fulumirani Mulungu kundipulumutsa;
    Yehova bwerani msanga kudzandithandiza.
Iwo amene akufunafuna moyo wanga
    achititsidwe manyazi ndi kusokonezedwa;
onse amene akukhumba chiwonongeko changa
    abwezedwe mopanda ulemu.
Onse amene akunena kwa ine kuti, “Aha, aha,”
    abwerere chifukwa cha manyazi awo.
Koma onse amene akufunafuna Inu
    akondwere ndi kusangalala mwa Inu;
iwo amene amakonda chipulumutso chanu
    nthawi zonse anene kuti, “Mulungu akuzike!”

Koma ine ndine wosauka ndi wosowa;
    bwerani msanga kwa ine Inu Mulungu.
Inu ndinu thandizo langa ndi momboli wanga;
    Inu Yehova musachedwe.

Ahebri 12:1-3

Yesu Chitsanzo Chathu

12 Tsono popeza ifenso tazunguliridwa ndi gulu lalikulu la mboni, tiyeni titaye chilichonse chimene chimatitchinga, makamaka tchimo limene limatikola mosavuta, ndipo tithamange ndi khama mpikisano umene tayambawu. Tiyeni tiyangʼanitsitse Yesu, amene ndi woyamba ndi wotsiriza wa chikhulupiriro chathu. Chifukwa cha chimwemwe chimene chimamudikira anapirira zowawa zapamtanda. Iye ananyoza manyazi a imfa yotere ndipo tsopano akukhala ku dzanja lamanja la mpando waufumu wa Mulungu. Muzilingalira za Iye amene anapirira udani waukulu chotere wochokera kwa anthu ochimwa, kuti musafowoke ndi kutaya mtima.

Yohane 13:21-32

Yesu Aneneratu za Kuperekedwa Kwake

21 Yesu atanena izi, anavutika kwambiri mu mzimu ndipo anachitira umboni kuti, “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti mmodzi mwa inu adzandipereka.”

22 Ophunzira ake anapenyetsetsana wina ndi mnzake, posadziwa kuti amanena za yani. 23 Mmodzi wa ophunzira ake amene Yesu anamukonda, anali atatsamira pachifuwa chake. 24 Simoni Petro anamukodola wophunzirayo ndi kuti, “Mufunseni akunena za yani.”

25 Atamutsamiranso Yesuyo, anamufunsa Iye kuti, “Ambuye, kodi ndani?”

26 Yesu anayankha kuti, “Iye amene ndidzamupatsa buledi amene ndanyema ndikususa ndi ameneyo.” Kenaka, atasunsa gawo la buledi, Iye anapereka kwa Yudasi Isikarioti, mwana wa Simoni. 27 Nthawi yomweyo Yudasi atangodya bulediyo, Satana analowa mwa Iye.

Yesu anamuwuza Iye kuti, “Chomwe ukufuna kuchita, chita msanga.” 28 Koma panalibe ndi mmodzi yemwe pa chakudyapo amene anamvetsa chifukwa chimene Yesu ananenera izi kwa iye. 29 Popeza Yudasi amasunga ndalama, ena amaganiza kuti Yesu amamuwuza iye kuti akagule zomwe zimafunika pa phwando, kapena kukapereka kanthu kena kake kwa osauka. 30 Nthawi yomweyo Yudasi atangodya buledi, anatuluka, ndipo unali usiku.

Yesu Aneneratu kuti Petro Adzamukana

31 Yudasi atatuluka, Yesu anati, “Tsopano Mwana wa Munthu walemekezedwa, ndipo mwa Iyeyu Mulungu walemekezedwanso. 32 Ngati Mulungu walemekezedwa mwa Iye, Mulungu mwini adzalemekezanso Mwana, ndipo amulemekeza nthawi yomweyo.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.