Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 51:1-12

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Pamene Mneneri Natani anabwera kwa iye atachita chigololo ndi Batiseba.

51 Mundichitire chifundo, Inu Mulungu,
    molingana ndi chikondi chanu chosasinthika;
molingana ndi chifundo chanu chachikulu
    mufafanize mphulupulu zanga.
Munditsuke zolakwa zanga zonse
    ndipo mundiyeretse kuchotsa tchimo langa.

Pakuti ndikudziwa mphulupulu zanga,
    ndipo tchimo langa lili pamaso panga nthawi zonse.
Motsutsana ndi Inu, Inu nokha, ndachimwa
    ndipo ndachita zoyipa pamaso panu,
Kotero kuti inu mwapezeka kuti ndinu wolungama
    pamene muyankhula ndi pamene muweruza.
Zoonadi ine ndinali wochimwa pomwe ndimabadwa,
    wochimwa kuyambira pa nthawi imene amayi anga anakhala woyembekezera ine.
Zoonadi inu mumafuna choonadi mu ziwalo zamʼkati mwanga;
    mumandiphunzitsa nzeru mʼkati mwanga mwenimweni.

Mundiyeretse ndi hisope ndipo ndidzayera,
    munditsuke ndipo ndidzayera kuposa matalala
Mundilole ndimve chimwemwe ndi chisangalalo,
    mulole kuti mafupa amene mwawamphwanya akondwere.
Mufulatire machimo anga
    ndi kufafaniza zolakwa zanga zonse.

10 Mulenge mʼkati mwanga mtima woyera Inu Mulungu
    ndi kukonzanso mzimu wokhazikika mwa ine.
11 Musandichotse pamaso panu
    kapena kuchotsa Mzimu wanu Woyera mwa ine.
12 Bwezeretsani mwa ine chimwemwe cha chipulumutso chanu
    ndipo mundipatse mzimu wofuna kumvera kuti undilimbitse.

Habakuku 3:2-13

Inu Yehova, ndamva za kutchuka kwanu;
    Inu Yehova, ntchito zanu zandiopsa.
Muzichitenso masiku athu ano,
    masiku athu ano zidziwike;
    mu ukali wanu mukumbukire kuchita chifundo.

Mulungu anabwera kuchokera ku Temani,
    Woyerayo kuchokera ku Phiri la Parani.
            Sela
Ulemerero wake unaphimba mlengalenga
    ndipo dziko lapansi linadzaza ndi matamando ake.
Kuwala kwa ulemerero wake kunali ngati kutuluka kwa dzuwa;
    kunyezimira kunkatuluka mʼdzanja lake,
    mʼmene anabisamo mphamvu zake.
Patsogolo pake pankagwa mliri;
    nthenda yoopsa inkagwa kumbuyo kwake.
Iye anayimirira ndi kugwedeza dziko lapansi;
    anayangʼana ndipo mitundu ya anthu inanjenjemera.
Mapiri okhazikika anagumuka
    ndipo zitunda zakalekale zinatitimira.
    Njira zake ndi zachikhalire.
Ndinaona matenti a ku Kusani ali pa mavuto,
    mokhala a ku Midiyani muli ululu waukulu.

Inu Yehova, kodi munakwiyira mitsinje?
    Kodi munakalipira timitsinje?
Kodi munapsera mtima nyanja
    pamene munakwera pa akavalo anu
    ndiponso magaleta anu achipulumutso?
Munasolola uta wanu mʼchimake,
    munayitanitsa mivi yambiri.
            Sela
Munagawa dziko lapansi ndi mitsinje;
10     mapiri anakuonani ndipo anagwedezeka.
Madzi amphamvu anasefukira;
    nyanja yozama inakokoma
    ndipo mafunde ake anakwera kwambiri.

11 Dzuwa ndi mwezi zinayima chilili mlengalenga,
    pa kungʼanima kwa mivi yanu yowulukayo,
    pa kunyezimira kwa mkondo wanu.
12 Munayendayenda mʼdziko lapansi muli ndi ukali,
    ndipo munapondereza mitundu ya anthu muli ndi mkwiyo.
13 Munapita kukalanditsa anthu anu,
    kukapulumutsa wodzozedwa wanu.
Munakantha mtsogoleri wa dziko la anthu oyipa,
    munawononga anthu ake onse.
            Sela

Yohane 12:1-11

Mariya Adzoza Mapazi a Yesu

12 Masiku asanu ndi limodzi Paska asanafike, Yesu anafika ku Betaniya, kumene kumakhala Lazaro, amene Yesu anamuukitsa kwa akufa. Kumeneko anamukonzera Yesu chakudya cha madzulo. Marita anatumikira pamene Lazaro anali mmodzi wa iwo amene anakhala nawo pa chakudyacho. Kenaka Mariya anatenga botolo la mafuta a nadi, onunkhira bwino kwambiri, amtengowapatali; Iye anadzoza mapazi a Yesu napukuta ndi tsitsi lake. Ndipo nyumba yonse inadzaza ndi fungo lonunkhira bwino la mafutawo.

Koma mmodzi wa ophunzira ake, Yudasi Isikarioti, amene pambuyo pake adzamupereka anati, “Nʼchifukwa chiyani mafuta awa sanagulitsidwe ndipo ndalama zake nʼkuzipereka kwa osauka?” Mafutawo anali a mtengo wa malipiro a chaka chimodzi. Iye sananene izi chifukwa cha kuganizira osauka koma chifukwa anali mbava; ngati wosunga thumba la ndalama, amabamo zomwe ankayikamo.

Yesu anayankha kuti, “Mulekeni. Mafutawa anayenera kusungidwa mpaka tsiku loyika maliro anga. Inu mudzakhala ndi osauka nthawi zonse, koma simudzakhala nane nthawi zonse.”

Pa nthawi imeneyi gulu lalikulu la Ayuda linadziwa kuti Yesu anali kumeneko, ndipo linabwera, sichifukwa cha Iye yekha koma kudzaonanso Lazaro, amene anamuukitsa kwa akufa. 10 Choncho akulu a ansembe anakonza njira yoti aphenso Lazaro, 11 pakuti chifukwa cha iye Ayuda ambiri amapita kwa Yesu ndi kumukhulupirira.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.