Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 51:1-12

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Pamene Mneneri Natani anabwera kwa iye atachita chigololo ndi Batiseba.

51 Mundichitire chifundo, Inu Mulungu,
    molingana ndi chikondi chanu chosasinthika;
molingana ndi chifundo chanu chachikulu
    mufafanize mphulupulu zanga.
Munditsuke zolakwa zanga zonse
    ndipo mundiyeretse kuchotsa tchimo langa.

Pakuti ndikudziwa mphulupulu zanga,
    ndipo tchimo langa lili pamaso panga nthawi zonse.
Motsutsana ndi Inu, Inu nokha, ndachimwa
    ndipo ndachita zoyipa pamaso panu,
Kotero kuti inu mwapezeka kuti ndinu wolungama
    pamene muyankhula ndi pamene muweruza.
Zoonadi ine ndinali wochimwa pomwe ndimabadwa,
    wochimwa kuyambira pa nthawi imene amayi anga anakhala woyembekezera ine.
Zoonadi inu mumafuna choonadi mu ziwalo zamʼkati mwanga;
    mumandiphunzitsa nzeru mʼkati mwanga mwenimweni.

Mundiyeretse ndi hisope ndipo ndidzayera,
    munditsuke ndipo ndidzayera kuposa matalala
Mundilole ndimve chimwemwe ndi chisangalalo,
    mulole kuti mafupa amene mwawamphwanya akondwere.
Mufulatire machimo anga
    ndi kufafaniza zolakwa zanga zonse.

10 Mulenge mʼkati mwanga mtima woyera Inu Mulungu
    ndi kukonzanso mzimu wokhazikika mwa ine.
11 Musandichotse pamaso panu
    kapena kuchotsa Mzimu wanu Woyera mwa ine.
12 Bwezeretsani mwa ine chimwemwe cha chipulumutso chanu
    ndipo mundipatse mzimu wofuna kumvera kuti undilimbitse.

Eksodo 30:1-10

Guwa Lansembe Yofukiza

30 Upange guwa lamatabwa amtengo wa mkesha lofukizirapo lubani. Likhale lofanana mbali zonse. Mulitali masentimita 46, mulifupi masentimita 46, ndipo msinkhu masentimita 91. Nyanga zake zipangidwe kumodzi ndi guwalo. Ukute guwa lonse ndi golide wabwino kwambiri, pamwamba pake, mbali zonse zinayi, pamodzi ndi nyanga zake. Ndipo upange mkombero wagolide kuzungulira guwalo. Upange mphete ziwiri zagolide ndipo uzilumikize ku guwa mʼmunsi mwa mkombero, mphete ziwiri ku mbali zonse ziwiri zoyangʼanana. Mphetozo zizigwira nsichi zonyamulira guwalo. Upange mizati yamtengo wa mkesha ndipo uyikute ndi golide. Uyike guwalo patsogolo pa nsalu yotchinga Bokosi la Chipangano. Apa ndi pamene ndizidzakumana nawe.

“Aaroni ayenera kumafukiza lubani wonunkhira pa guwalo mmawa uliwonse. Pamene akukonza nyale zija afukizenso lubani. Aaroni ayenera kufukizanso lubani pamene ayatsa nyale madzulo kuti lubani akhale akuyaka nthawi zonse pamaso pa Yehova kwa mibado imene ikubwera. Pa guwapo usafukize lubani wachilendo kapena kuperekapo nsembe yopsereza kapena nsembe yaufa. Usathire pa guwapo ngakhale nsembe yachakumwa. 10 Aaroni azidzapereka nsembe yopepesera machimo pa nyanga za guwalo kamodzi pa chaka. Mwambowu uzidzachitika pogwiritsa ntchito magazi a nsembe yopepesera machimo, ndipo zizidzachitika mʼmibado yanu yonse. Choncho guwa lansembelo lidzakhala loyera ndi loperekedwa kwa Yehova.”

Ahebri 4:14-5:4

Yesu Mkulu wa Ansembe Wopambana

14 Popeza kuti tili ndi Mkulu wa ansembe wopambana, amene analowa kale kumwamba, Yesu Mwana wa Mulungu, tiyeni tigwiritsitse chikhulupiriro chathu chimene timavomereza. 15 Pakuti sitili ndi Mkulu wa ansembe amene sangathe kutimvera chifundo chifukwa cha zofowoka zathu. Koma tili naye amene anayesedwa mʼnjira zonse monga ife, koma sanachimwe. 16 Tiyeni tsono tiyandikire ku mpando waufumu, wachisomo mopanda mantha, kuti tilandire chifundo ndi kupeza chisomo chotithandiza pa nthawi yeniyeni.

Mkulu wa ansembe aliyense amasankhidwa kuchokera pakati pa anthu ndipo amayikidwa kuti aziwayimirira pamaso pa Mulungu, kuti azipereka mphatso ndi nsembe chifukwa cha machimo. Popeza kuti iye mwini ali ndi zofowoka zake, amatha kuwalezera mtima amene ali osadziwa ndi osochera. Chifukwa cha ichi, iye amadziperekera nsembe chifukwa cha machimo ake omwe ndiponso chifukwa cha machimo a anthu ena.

Palibe amene amadzipatsa yekha ulemu wotere, koma amachita kuyitanidwa ndi Mulungu monga momwe anayitanidwira Aaroni.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.