Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
BUKU LACHISANU
Masalimo 107–150
107 Yamikani Yehova chifukwa ndi wabwino;
pakuti chikondi chake ndi chosatha.
2 Owomboledwa a Yehova anene zimenezi
amene Iyeyo anawawombola mʼdzanja la mdani,
3 iwo amene anawasonkhanitsa kuchokera ku mayiko,
kuchokera kumadzulo ndi kummawa, kuchokera kumpoto ndi kummwera.
17 Ena anakhala zitsiru chifukwa cha njira zawo zowukira,
ndipo anamva zowawa chifukwa cha mphulupulu zawo.
18 Iwo ananyansidwa ndi chakudya chilichonse
ndipo anafika pafupi ndi zipata za imfa.
19 Pamenepo analirira Yehova mʼmasautso awo
ndipo Iye anawapulumutsa ku masautso awowo.
20 Iye anatumiza mawu ake ndi kuwachiritsa;
anawalanditsa ku manda.
21 Ayamike Yehova chifukwa cha chikondi chake chosatha
ndi machitidwe ake odabwitsa kwa anthu.
22 Apereke nsembe yachiyamiko
ndi kufotokoza za ntchito zake ndi nyimbo zachimwemwe.
Aaroni Amwalira
22 Gulu lonse la Aisraeli linachoka ku Kadesi ndipo linafika ku phiri la Hori. 23 Ali pa phiri la Hori, pafupi ndi malire a Edomu, Yehova anati kwa Mose ndi Aaroni, 24 “Aaroni adzakakhala ndi anthu a mtundu wake, sadzalowa mʼdziko limene ndapereka kwa Aisraeli, chifukwa nonse munandiwukira motsutsana ndi malamulo anga ku madzi a ku Meriba. 25 Tenga Aaroni ndi mwana wake wamwamuna Eliezara ndipo ukwere nawo ku phiri la Hori. 26 Uvule Aaroni zovala zake ndipo umuveke mwana wake Eliezara, pakuti Aaroni adzafera komweko, ndipo adzakakhala ndi anthu a mtundu wake.”
27 Mose anachita monga Yehova anamulamulira: Anapita ku phiri la Hori gulu lonse likuona. 28 Pamenepo Mose anavula Aaroni zovala zake ndi kuveka mwana wake Eliezara. Aaroni anafa kumeneko pamwamba pa phirilo. Koma Mose ndi Eliezara anatsika ku phiriko, 29 ndipo pamene anthu onse anamva kuti Aaroni wafa, nyumba yonse ya Israeli inamulira Aaroniyo masiku makumi atatu.
Yesu Aphunzitsa Nekodimo za Kubadwa Kwatsopano
3 Ndipo panali Mfarisi wotchedwa Nekodimo, wa mʼgulu lolamulira la Ayuda. 2 Iye anabwera kwa Yesu usiku ndipo anati, “Rabi, ife tikudziwa kuti ndinu aphunzitsi wochokera kwa Mulungu, pakuti palibe amene angachite zizindikiro zodabwitsa zimene Inu mukuchita ngati Mulungu sali naye.”
3 Poyankha Yesu ananena kuti, “Zoonadi, Ine ndikukuwuza kuti, ngati munthu sabadwanso mwatsopano sangathe kuona ufumu wa Mulungu.”
4 Nekodimo anati, “Kodi munthu angabadwenso bwanji atakalamba? Kodi angalowe kachiwiri mʼmimba ya amayi ake kuti abadwenso?”
5 Yesu anayankha kuti, “Zoonadi, Ine ndikukuwuza kuti ngati munthu sabadwa mwa madzi ndi Mzimu Woyera, sangalowe mu ufumu wa Mulungu. 6 Thupi limabereka thupi, koma Mzimu amabereka mzimu. 7 Iwe usadabwe chifukwa ndakuwuza kuti, ‘Uyenera kubadwanso.’ 8 Mphepo imawomba kulikonse kumene ikufuna. Ungathe kumva kuwomba kwake, koma sungathe kudziwa kumene ikuchokera kapena kumene ikupita. Nʼchimodzimodzi ndi amene abadwa ndi Mzimu Woyera.”
9 Nekodimo anafunsa kuti, “Kodi izi zingatheke bwanji?”
10 Yesu anati, “Iwe mphunzitsi wa Israeli, kodi sukuzindikira zimenezi? 11 Zoonadi, Ine ndikukuwuza kuti ife tiyankhula zimene tikuzidziwa ndi kuchitira umboni zimene taziona, komabe inu simuvomereza umboni wathu. 12 Ine ndikuyankhula kwa iwe zinthu za dziko lapansi ndipo sukukhulupirira. Nanga kodi udzakhulupirira bwanji ngati nditayankhula zinthu zakumwamba? 13 Palibe wina aliyense anapita kumwamba, koma yekhayo amene watsika kuchokera kumwamba, Mwana wa Munthu.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.