Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 84

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a Gititi. Salimo la ana a Kora.

84 Malo anu okhalamo ndi okomadi,
    Inu Yehova Wamphamvuzonse!
Moyo wanga ukulakalaka, mpaka kukomoka,
    kufuna mabwalo a Yehova;
Mtima wanga ndi thupi langa zikufuwulira
    Mulungu wamoyo.

Ngakhale timba wapeza nyumba yokhalamo,
    ndiponso namzeze wadzipezera yekha chisa,
    kumene amagonekako ana ake
pafupi ndi guwa lanu la nsembe,
    Inu Yehova Wamphamvuzonse, Mfumu yanga ndi Mulungu wanga.
Odala amene amakhala mʼNyumba yanu;
    nthawi zonse amakutamandani.
            Sela

Odala amene mphamvu yawo ili mwa Inu,
    mitima yawo ikufunitsitsa kuyenda mʼmisewu yopita ku Ziyoni.
Pamene akudutsa chigwa cha Baka,
    amachisandutsa malo a akasupe;
    mvula ya chizimalupsa imadzazanso mayiwe ake.
Iwo amanka nakulirakulira mphamvu
    mpaka aliyense ataonekera pamaso pa Mulungu mu Ziyoni.

Imvani pemphero langa, Inu Yehova Mulungu Wamphamvuzonse;
    mvereni Inu Mulungu wa Yakobo.
            Sela
Yangʼanani chishango chathu, Inu Mulungu;
    yangʼanani mokoma mtima pa wodzozedwa wanu.

10 Nʼkwabwino kukhala mʼmabwalo anu tsiku limodzi
    kuposa kukhala kwina kwake kwa zaka 1,000;
Ine ndingakonde kukhala mlonda wa pa khomo la Nyumba ya Mulungu wanga
    kuposa kukhala mʼmatenti a anthu oyipa.
11 Pakuti Yehova Mulungu ndi dzuwa ndi chishango;
    Yehova amapereka chisomo ndi ulemu;
Iye sawamana zinthu zabwino
    iwo amene amayenda mwangwiro.

12 Inu Yehova Wamphamvuzonse,
    wodala ndi munthu amene amakhulupirira Inu.

1 Mafumu 6:1-4

Solomoni Amanga Nyumba ya Mulungu

Patapita zaka 480 Aisraeli atatuluka mʼdziko la Igupto, chaka chachinayi cha ulamuliro wa Solomoni mu Israeli, mwezi wa Zivi, umene ndi mwezi wachiwiri, Solomoni anayamba kumanga Nyumba ya Yehova.

Nyumba imene Solomoni anamangira Yehova mulitali mwake inali mamita 27, mulifupi mwake inali mamita asanu ndi anayi, ndipo msinkhu wake unali mamita 13 ndi theka. Chipinda chakubwalo mʼmbali mwake chinali mamita asanu ndi anayi kulingana ndi mulifupi mwa Nyumbayo ndipo kutalika kwake kunali kwa mamita anayi ndi theka. Anapanga mazenera amene maferemu ake anali olowa mʼkati mwa makoma a Nyumbayo.

1 Mafumu 6:21-22

21 Solomoni anakutira golide weniweni mʼkati mwake mwa Nyumbayi, ndipo anayalika maunyolo a golide mopingasa kutsogolo kwa malo wopatulika amene anakutidwa ndi golide. 22 Motero anakuta mʼkati monse ndi golide. Anakutanso ndi golide guwa lansembe la mʼkati mwa chipinda chopatulika.

1 Akorinto 3:10-23

10 Mwachisomo chimene Mulungu wandipatsa, ine ndinayika maziko monga mmisiri waluntha, ndipo ena akumangapo. Koma aliyense ayenera kuchenjera mmene akumangira. 11 Pakuti wina sangayikenso maziko ena oposera amene anakhazikitsidwa kale, amene ndi Yesu Khristu. 12 Ngati munthu aliyense amanga pa maziko awa pogwiritsa ntchito golide, siliva, miyala yamtengowapatali, milimo yamitengo, tsekera kapena udzu, 13 ntchito yake idzaonekera pamene Tsiku la chiweruzo lidzazionetsa poyera. Tsikulo lidzafika ndi moto, ndipo motowo ndi umene udzayesa ntchito ya munthu aliyense. 14 Ngati zimene zamangidwazo sizidzagwa, adzalandira mphotho yake. 15 Ndipo ngati zidzanyeke ndi moto, sadzalandira mphotho koma iye mwini adzapulumukabe, koma monga ngati munthu amene wapulumuka mʼmoto.

16 Kodi inu simukudziwa kuti ndinu Nyumba ya Mulungu ndipo kuti Mzimu wa Mulungu amakhala mwa inu? 17 Ngati wina aliyense awononga Nyumba ya Mulunguyo, Mulungu nayenso adzamuwononga ameneyo; popeza Nyumba ya Mulungu ndi yopatulika ndipo Nyumbayo ndi inu amene.

18 Choncho musadzinyenge. Ngati wina wa inu akuganiza kuti ndi wanzeru pa mulingo wa mʼbado uno, ayenera kukhala “wopusa” kuti athe kukhala wanzeru. 19 Pakuti nzeru ya dziko lapansi ndi yopusa pamaso pa Mulungu. Monga kwalembedwera kuti, “Iye amakola anthu ochenjera mu msampha wa kuchenjera kwawo,” 20 ndiponso, “Ambuye amadziwa kuti maganizo a wanzeru ndi opandapake.” 21 Choncho, wina asanyadire anthu chabe! Zonse ndi zanu, 22 kaya Paulo kapena Apolo kapena Kefa kapena dziko lapansi, kapena moyo, kapena imfa, kapena tsopano, kapena mʼtsogolo, zonse ndi zanu, 23 ndipo inu ndinu a Khristu, ndipo Khristu ndi wa Mulungu.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.