Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.
19 Zakumwamba zimalengeza za ulemerero wa Mulungu;
thambo limalalikira ntchito za manja ake.
2 Tsiku ndi tsiku zimayankhula mawu ambiri,
usiku ndi usiku zimaonetsa poyera nzeru.
3 Palibe kuyankhula, palibe mawu aliwonse;
liwu lawo silimveka.
4 Koma uthenga wawo umapita pa dziko lonse lapansi,
mawuwo amafika mpaka
kumalekezero a dziko lapansi.
5 Dzuwa lili ngati mkwatibwi wobwera kuchokera ku nsanja yake,
ngati katswiri wokondwerera kuthamanga pa mpikisano.
6 Limatuluka kuyambira mbali ina ya thambo
ndi kuzungulira mpaka mbali inanso;
palibe chinthu chotha kupewa kutentha kwake.
7 Lamulo la Yehova ndi langwiro,
kutsitsimutsa moyo.
Maumboni a Yehova ndi odalirika,
amapereka nzeru kwa wopanda nzeru.
8 Malangizo a Yehova ndi olungama,
amapereka chimwemwe mu mtima.
Malamulo a Yehova ndi onyezimira,
amapereka kuwala.
9 Kuopa Yehova ndiye chinthu changwiro,
chimakhala mpaka muyaya.
Maweruzo a Yehova ndi owona
ndipo onse ndi olungama;
10 ndi a mtengowapatali kuposa golide,
kuposa golide weniweni;
ndi otsekemera kuposa uchi,
kuposa uchi wochokera pa chisa chake.
11 Mtumiki wanu amachenjezedwa nawo;
powasunga pali mphotho yayikulu.
12 Ndani angathe kudziwa zolakwa zake?
Mundikhululukire zolakwa zanga zobisika.
13 Muteteze mtumiki wanunso ku machimo ochita akudziwa;
iwo asandilamulire.
Kotero ndidzakhala wosalakwa,
wopanda mlandu wa tchimo lalikulu.
14 Mawu a mʼkamwa mwanga ndi zolingalira za mu mtima mwanga
zikhale zokondweretsa pamaso panu,
Inu Yehova, Thanthwe langa ndi Mpulumutsi wanga.
Pa Phiri la Sinai
19 Ana a Israeli aja anafika ku chipululu cha Sinai pa tsiku loyamba la mwezi wachitatu chichokere mʼdziko la Igupto. 2 Atachoka ku Refidimu, anafika ku Sinai, ndipo Aisraeli anamangako misasa yawo moyangʼanana ndi phirilo.
3 Mose anakwera ku phiri kukakumana ndi Mulungu ndipo Yehova anamuyitana nati, “Ukawuze zidzukulu za Yakobo, ana onse a Israeli kuti, 4 ‘Inu eni munaona zimene ndinawachitira Aigupto ndiponso mmene ndinakunyamulirani, monga mmene chiwombankhanga chimanyamulira ana ake pa mapiko,’ ndikukubweretsani kwa Ine. 5 Tsopano, ngati mumveradi mawu anga ndi kusunga pangano langa, mudzakhala chuma changa chapamtima pakati pa mitundu yonse. Ngakhale kuti dziko lonse lapansi ndi langa, 6 inu mudzakhala ansembe achifumu ndi mtundu woyera mtima. Awa ndi mawu amene uyenera kuwawuza Aisraeli.”
7 Ndipo Mose anabwerera ndi kuyitanitsa akuluakulu. Atabwera anawafotokozera mawu amene Yehova anamulamulira kuti adzanene. 8 Anthu onse anayankha pamodzi kuti, “Ife tidzachita zonse zimene Yehova wanena.” Choncho Mose anabweza yankho lawo kwa Yehova.
9 Yehova anati kwa Mose, “Ine ndibwera kwa iwe mu mtambo wakuda kuti anthu adzandimve ndikuyankhula ndi iwe. Choncho adzakukhulupirira nthawi zonse.” Kenaka Mose anawuza Yehova zimene anthu ananena.
Mwala wa Moyo ndi Anthu Osankhidwa
4 Pamene mukubwera kwa Iye, amene ndi Mwala wa moyo, umene anthu anawukana, koma Mulungu anawusankha kuti ndi wa mtengowapatali, 5 inunso, mukhale ngati miyala ya moyo yoti Mulungu amangire nyumba yake yauzimu kuti mukhale ansembe opatulika, opereka nsembe zauzimu zovomerezeka ndi Mulungu mwa Yesu Khristu. 6 Pakuti mʼMalemba mwalembedwa kuti,
“Taonani, ndikuyika mwala wa maziko mu Ziyoni,
wosankhika ndi wamtengowapatali.
Amene akhulupirira Iye
sadzachititsidwa manyazi.”
7 Tsono kwa inu okhulupirira, mwalawo ndi wamtengowapatali. Koma kwa amene sakhulupirira,
“Mwala umene amisiri anawukana
wasanduka mwala wa maziko,
8 ndi
“Mwala wopunthwitsa anthu
ndiponso thanthwe limene limagwetsa anthu.”
Iwo amapunthwa chifukwa samvera uthenga, pakuti ichi ndiye chinali chifuniro cha Mulungu pa iwo.
9 Koma inu ndinu anthu osankhidwa ndi Mulungu, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu ake enieni a Mulungu, munasankhidwa kuti mulalikire za ntchito zamphamvu za Iye amene anakuyitanani kuti mutuluke mu mdima ndi kulowa mʼkuwunika kwake kodabwitsa. 10 Kale simunali anthu ake, koma tsopano ndinu anthu a Mulungu. Kale simunalandire chifundo, koma tsopano mwalandira chifundo.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.