Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
105 Yamikani Yehova, itanani dzina lake;
lalikirani pakati pa anthu a mitundu ina zimene Iye wachita.
2 Imbirani Iye, imbani matamando kwa Iyeyo;
fotokozani za machitidwe ake onse odabwitsa.
3 Munyadire dzina lake loyera;
mitima ya iwo amene amafunafuna Yehova ikondwere.
4 Dalirani Yehova ndi mphamvu zake;
funafunani nkhope yake nthawi yonse.
5 Kumbukirani zodabwitsa zimene Iye anazichita,
zozizwitsa zake ndi maweruzo amene anapereka,
6 inu zidzukulu za Abrahamu mtumiki wake,
inu ana a Yakobo, osankhika ake.
7 Iye ndiye Yehova Mulungu wathu;
maweruzo ake ali pa dziko lonse lapansi.
8 Iyeyo amakumbukira pangano lake kwamuyaya,
mawu amene analamula kwa mibado yonse,
9 pangano limene Iye anapanga ndi Abrahamu,
lumbiro limene analumbira kwa Isake.
10 Iye analitsimikiza kwa Yakobo monga zophunzitsa,
kwa Israeli monga pangano lamuyaya:
11 “Ndidzapereka kwa iwe dziko la Kanaani
ngati gawo la cholowa chako.”
37 Yehova anatulutsa Israeli, atatenga siliva ndi golide wambiri,
ndipo pakati pa mafuko awo palibe mmodzi amene anafowoka.
38 Dziko la Igupto linakondwa pamene iwo anachoka,
pakuti kuopsa kwa Israeli kunawagwera iwo.
39 Iye anatambasula mitambo ngati chofunda chawo,
ndi moto owawunikira usiku.
40 Iwo anapempha, ndipo Iye anawabweretsera zinziri
ndipo anawakhutitsa ndi chakudya chochokera kumwamba.
41 Iye anatsekula thanthwe, ndipo madzi anatuluka;
ngati mtsinje anayenda mʼchipululu.
42 Pakuti anakumbukira lonjezo lake loyera limene
linaperekedwa kwa Abrahamu mtumiki wake.
43 Iye anatulutsa anthu ake akukondwera,
osankhika ake akufuwula mwachimwemwe;
44 Iye anawapatsa mayiko a anthu a mitundu ina
ndipo anakhala olowamʼmalo a zimene ena anazivutikira,
45 kuti iwo asunge malangizo ake
ndi kutsatira malamulo ake.
Tamandani Yehova.
12 Yehova akuti,
“Chilonda chanu nʼchosachizika,
bala lanu ndi lonyeka.
13 Palibe amene angathe kukutetezani pa mlandu wanu,
palibe chiyembekezo choti inu nʼkuchira,
palibe mankhwala ochiritsa inu.
14 Abwenzi anu onse akuyiwalani;
sasamalanso za inu.
Ndakukanthani ngati mmene mdani akanachitira.
Ndipo ndakulangani mwa nkhanza,
chifukwa machimo anu ndi ambiri,
ndipo kulakwa kwanu ndi kwakukulu.
15 Chifukwa chiyani mukulira nacho chilonda chanu?
Bala lanu silingapole ayi.
Ine ndakuchitani zimenezi chifukwa machimo anu ndi ambiri
ndipo kulakwa kwanu nʼkwakukulu.
16 “Tsono onse amene anakuwonongani, nawonso adzawonongedwa;
adani anu onse adzapita ku ukapolo.
Iwo amene anafunkha zinthu zanu, zinthu zawo zidzafunkhidwanso;
onse amene anakusakazani nawonso adzasakazidwa.
17 Ndidzachiza matenda anu
ndi kupoletsa zilonda zanu,
akutero Yehova,
‘chifukwa mukutchedwa anthu otayika.
Amati, ndi anthu a ku Ziyoni awa amene alibe wowasamala.’ ”
18 Yehova akuti,
“Ndidzabwera nalo banja la Yakobo ku dziko lawo
ndipo ndidzachitira chifundo malo ake okhalamo;
mzinda wa Yerusalemu udzamangidwanso pa bwinja pake,
nyumba yaufumu idzamangidwanso pa malo pake penipeni.
19 Anthuwo adzayimba nyimbo zoyamika Yehova
ndipo kudzamveka phokoso lachisangalalo.
Ndidzawachulukitsa,
ndipo chiwerengero chawo sichidzatsika;
ndidzawapatsa ulemerero,
ndipo sadzanyozedwanso.
20 Ana awo adzakhalanso monga mmene analili kale,
ndipo gulu lawo ndidzalikhazikitsa pamaso panga;
ndidzalanga onse owazunza.
21 Mtsogoleri wawo adzakhala mmodzi mwa iwo.
Wodzawalamulira adzachokera pakati pawo.
Choncho ndidzawakokera kufupi ndi Ine ndipo iye adzandiyandikira.
Ndani angalimbe mtima payekha kuyandikana nane
popanda kuyitanidwa?”
akutero Yehova.
22 “Choncho inu mudzakhala anthu anga,
ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wanu.”
36 Khulupirirani kuwunika, pamene mukanali ndi kuwunika, kuti mukhale ana a kuwunika.” Yesu atamaliza kuyankhula izi, Iye anachoka nabisala kuti asamuone.
Ayuda Apitirira Kusakhulupirira
37 Ngakhale Yesu anachita zizindikiro zodabwitsa zonsezi pamaso pawo, sanamukhulupirirebe. 38 Izi zinakwaniritsa mawu a mneneri Yesaya kuti:
“Ambuye, wakhulupirira uthenga wathu ndani,
ndipo ndi kwa yani komwe mkono wa Ambuye wavumbulutsidwa?”
39 Pa chifukwa cha ichi iwo sanakhulupirire, chifukwa Yesaya ananenanso kuti:
40 “Iye wachititsa khungu maso awo
ndi kuwumitsa mitima yawo,
kotero kuti iwo sangathe kuona ndi maso awo,
kapena kuzindikira ndi mitima yawo,
kapena kutembenuka kuti Ine ndikanawachiza.”
41 Yesaya ananena izi chifukwa anaona ulemerero wa Yesu ndi kuyankhula za Iye.
42 Komabe pa nthawi yomweyi ambiri ngakhale atsogoleri anakhulupirira Iye. Koma chifukwa cha Afarisi iwo sanavomereze chikhulupiriro chawo chifukwa amaopa kuti angawatulutse mʼsunagoge; 43 pakuti iwo amakonda kuyamikiridwa ndi anthu kuposa kuyamikiridwa ndi Mulungu.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.