Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Pangano la Mdulidwe
17 Pamene Abramu anali ndi zaka 99, Yehova anamuonekera nati, “Ine ndine Mulungu Wamphamvuzonse. Ukhale munthu wochita zolungama nthawi zonse. 2 Ndipo Ine ndikulonjeza kuti ndidzakupatsa zidzukulu zambiri.”
3 Pomwepo Abramu anadziponya pansi ndipo Mulungu anati kwa iye, 4 “Pangano langa ndi iwe ndi ili: Udzakhala kholo la mitundu yambiri ya anthu. 5 Sudzatchedwanso Abramu; dzina lako lidzakhala Abrahamu, chifukwa ndakusandutsa kukhala kholo la mitundu yambiri ya anthu. 6 Ndidzakupatsa zidzukulu zambiri motero kuti mitundu yambiri ya anthu idzatuluka mwa iwe. Mafumunso adzatuluka mwa iwe. 7 Pangano langa ndi iwe pamodzi ndi zidzukulu za mibado ya mʼtsogolo lidzakhala la muyaya. Ndidzakhala Mulungu wako ndi Mulungu wa zidzukulu zako.
15 Mulungu anatinso kwa Abrahamu, “Sarai mkazi wako, sudzamutchanso Sarai; dzina lake lidzakhala Sara. 16 Ndidzamudalitsa ndipo adzakubalira mwana wamwamuna. Ndidzamudalitsa kuti akhale mayi wa mitundu ya anthu; mafumu a anthuwo adzachokera mwa iye.”
23 Inu amene mumaopa Yehova mutamandeni!
Inu zidzukulu zonse za Yakobo, mulemekezeni!
Muopeni mwaulemu, inu zidzukulu zonse za Israeli!
24 Pakuti Iye sanapeputse kapena kunyoza
kuvutika kwa wosautsidwayo;
Iye sanabise nkhope yake kwa iye.
Koma anamvera kulira kwake kofuna thandizo.
25 Ndidzakutamandani pa msonkhano waukulu chifukwa cha zimene mwandichitira.
Ndidzakwaniritsa lonjezo langa pamaso pa amene amaopa Inu.
26 Osauka adzadya ndipo adzakhuta;
iwo amene amafunafuna Yehova adzamutamanda.
Mitima yanu ikhale ndi moyo mpaka muyaya!
27 Malekezero onse a dziko lapansi
adzakumbukira Yehova ndi kutembenukira kwa Iye,
ndipo mabanja a mitundu ya anthu
adzawerama pamaso pake,
28 pakuti ulamuliro ndi wake wa Yehova
ndipo Iye amalamulira anthu a mitundu yonse.
29 Anthu olemera onse a dziko lapansi adzachita phwando ndi kulambira;
onse amene amapita ku fumbi adzagwada pamaso pake;
iwo amene sangathe kudzisunga okha ndi moyo.
30 Zidzukulu zamʼtsogolo zidzamutumikira Iye;
mibado ya mʼtsogolo idzawuzidwa za Ambuye.
31 Iwo adzalengeza za chilungamo chake
kwa anthu amene pano sanabadwe
pakuti Iye wachita zimenezi.
13 Abrahamu ndi zidzukulu zake sanalandire lonjezano lakuti adzalandira dziko lapansi kudzera mu Malamulo, koma kudzera mu chilungamo chimene chimabwera ndi chikhulupiriro. 14 Pakuti ngati amene amadalira Malamulo ndiye olowa mʼmalo, ndiye kuti chikhulupiriro nʼchopanda pake ndipo lonjezano ndi lopanda phindu 15 chifukwa Malamulo anabweretsa chilango. Ndipo kumene kulibe Malamulo kulibenso kuwalakwitsa.
16 Motero, timalandira lonjezo mwachikhulupiriro. Laperekedwa mwachisomo kuti patsimikizidwe kuti lonjezolo liperekedwa kwa ana ndi zidzukulu zonse za Abrahamu, osati kwa iwo okha amene amatsatira Malamulo komanso kwa iwo amene ali ndi chikhulupiriro cha Abrahamu. Iye ndiye kholo la ife tonse. 17 Monga kwalembedwa kuti, “Ine ndakusandutsa kukhala kholo la mitundu yambiri.” Iye ndiye kholo lathu pamaso pa Mulungu, amene anamukhulupirira, Mulungu amene amapereka moyo kwa akufa ndipo amapereka moyo kwa zinthu zopanda moyo.
18 Ngakhale zinali zosayembekezeka, Abrahamu anakhulupirira ndi chiyembekezo kuti adzakhala kholo la mitundu yambiri. Izi ndi monga zinanenedwa kwa iye kuti, “Ndi mmene adzakhalire ana ako ndi zidzukulu zako.” 19 Iye sanafowoke mʼchikhulupiriro. Anadziwa choonadi cha thupi lake kuti linali lakufa popeza anali ndi zaka pafupifupi 100 ndiponso mimba ya Sara inali yowuma. 20 Komabe iye sanagwedezeke chifukwa chosakhulupirira pa zokhudzana ndi lonjezo la Mulungu. Iye analimbikitsidwa mʼchikhulupiriro chake ndi kupereka ulemerero kwa Mulungu. 21 Anatsimikiza mu mtima mwake kuti Mulungu anali ndi mphamvu yochita chomwe analonjeza. 22 Nʼchifukwa chake “chinamuchititsa kukhala wolungama.” 23 Mawu akuti, “chinatengedwa kwa iye” sanalembedwe chifukwa cha iye yekha, 24 komanso chifukwa ife amene Mulungu adzatiyesa olungama, ife amene tikhulupirira mwa Iye amene anamuukitsa kwa akufa, Yesu Ambuye athu. 25 Iye anaperekedwa kuti aphedwe chifukwa cha machimo athu ndipo anaukitsidwa ndi kukhala ndi moyo kuti tilungamitsidwe.
Yesu Aneneratu za Imfa Yake
31 Iye anayamba kuwaphunzitsa kuti, “Mwana wa Munthu ayenera kumva zowawa zambiri ndi kukanidwa ndi akulu a ansembe, ndi aphunzitsi a malamulo, ndi kuti ayenera kuphedwa ndipo patatha masiku atatu adzaukanso.” 32 Izi anaziyankhula momveka bwino, ndipo Petro anamutengera pambali ndipo anayamba kumudzudzula.
33 Koma Yesu atatembenuka ndi kuyangʼana ophunzira ake, anamudzudzula Petro nati, “Choka pamaso panga Satana! Suganizira zinthu za Mulungu koma za anthu.”
Njira ya Mtanda
34 Kenaka anayitana gulu la anthu pamodzi ndi ophunzira ake nati: “Ngati wina aliyense afuna kunditsata Ine, ayenera kudzikana yekha ndi kunyamula mtanda wake ndi kunditsata. 35 Pakuti aliyense amene afuna kupulumutsa moyo wake adzawutaya, koma aliyense amene ataya moyo wake chifukwa cha Ine ndi cha Uthenga Wabwino, adzawupulumutsa. 36 Kodi munthu adzapindulanji akalandira dziko lonse lapansi, koma ndi kutaya moyo wake? 37 Kapena nʼchiyani chomwe munthu angapereke chosinthana ndi moyo wake? 38 Ngati wina achita manyazi chifukwa cha Ine ndi mawu anga mu mʼbado uno wachigololo ndi wochimwa, Mwana wa Munthu adzachita naye manyazi pamene adzabwera mu ulemerero wa Atate ake pamodzi ndi angelo oyera.”
Maonekedwe a Ulemerero wa Yesu pa Phiri
2 Patatha masiku asanu ndi limodzi Yesu anatenga Petro, Yakobo ndi Yohane nawatsogolera kupita ku phiri lalitali, kumene anali okhaokha. Kumeneko maonekedwe ake anasinthika pamaso pawo. 3 Zovala zake zinawala monyezimira kwambiri, kotero kuti palibe sopo wina aliyense amene angaziyeretse monyezimira chotere pa dziko la pansi. 4 Ndipo anaonekera Eliya ndi Mose pamaso pawo, amene ankayankhulana ndi Yesu.
5 Petro anati kwa Yesu, “Aphunzitsi, ndi kwabwino kuti ife tili pano. Tiyeni timange misasa itatu; umodzi wanu, wina wa Mose ndi wina wa Eliya.” 6 (Iye sanadziwe choti anene, anali ndi mantha akulu).
7 Pamenepo mtambo unaoneka ndi kuwaphimba, ndipo mawu anamveka kuchokera mu mtambo kuti, “Uyu ndi Mwana wanga wokondedwa. Mvereni Iye!”
8 Mwadzidzidzi, atayangʼanayangʼana, sanaonenso wina aliyense ali ndi iwo kupatula Yesu.
9 Pamene ankatsika kuchokera ku phiri, Yesu anawalamulira kuti asawuze aliyense zimene anaona mpaka Mwana wa Munthu atauka kwa akufa.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.