Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 77

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a Yedutuni. Salimo la Asafu.

77 Ndinafuwulira Mulungu kupempha thandizo;
    ndinafuwula mokweza kwa Mulungu kuti anditcherere khutu.
Pamene ndinali pa masautso ndinafunafuna Ambuye;
    usiku ndinatambasula manja mosalekeza
    ndipo moyo wanga unakana kutonthozedwa.

Ndinakumbukira Inu Mulungu, ndipo ndinabuwula;
    ndinasinkhasinkha ndipo mzimu wanga unalefuka.
            Sela
Munagwira zikope zanga kuti ndisagone
    ndipo ndinavutika kwambiri kuti ndiyankhule.
Ndinaganizira za masiku akale,
    zaka zamakedzana;
Ndinakumbukira nyimbo zanga usiku.
    Mtima wanga unasinkhasinkha ndipo mzimu wanga unafunsa kuti,

“Kodi Ambuye adzatikana mpaka muyaya?
    Kodi Iwo sadzaonetsanso kukoma mtima kwawo?
Kodi Chikondi chake chosatha chija chatheratu?
    Kodi malonjezo ake alephera nthawi yonse?
Kodi Mulungu wayiwala kukhala wokoma mtima?
    Kodi mu mkwiyo wake waleka chifundo chake?”

10 Ndipo ndinaganiza, “Pa izi ine ndidzapemphanso:
    zaka za dzanja lamanja la Wammwambamwamba.
11 Ine ndidzakumbukira ntchito za Yehova;
    Ine ndidzakumbukira zodabwitsa zanu za kalekale.
12 Ndidzakumbukira ntchito zanu
    ndi kulingalira zodabwitsa zanu.”

13 Njira zanu Mulungu ndi zoyera.
    Kodi ndi mulungu uti ali wamkulu kuposa Mulungu wathu?
14 Inu ndinu Mulungu wochita zodabwitsa;
    Mumaonetsera mphamvu yanu pakati pa mitundu ya anthu.
15 Ndi dzanja lanu lamphamvu munawombola anthu anu,
    zidzukulu za Yakobo ndi Yosefe.
            Sela

16 Madzi anakuonani Mulungu,
    madzi anakuonani ndipo anachita mantha;
    nyanja yozama inakomoka.
17 Mitambo inakhuthula madzi ake pansi,
    mu mlengalenga munamveka mabingu;
    mivi yanu inawuluka uku ndi uku.
18 Bingu lanu linamveka mʼmphepo ya kamvuluvulu,
    mphenzi yanu inawalitsa dziko lonse;
    dziko lapansi linanjenjemera ndi kugwedezeka.
19 Njira yanu inadutsa pa nyanja,
    njira yanu inadutsa pa madzi amphamvu,
    ngakhale zidindo za mapazi anu sizinaoneke.

20 Inu munatsogolera anthu anu ngati gulu la nkhosa
    mwa dzanja la Mose ndi Aaroni.

Yobu 5:8-27

“Koma ndikanakhala ine, ndikanamudandawulira Mulungu;
    ndikanapereka mlandu wanga kwa Iye.
Iye amachita zozizwitsa zimene sizimvetsetseka,
    zodabwitsa zimene sizingatheke kuwerengedwa.
10 Iye amagwetsa mvula pa dziko lapansi,
    ndipo amathirira minda ya anthu.
11 Iye amakweza anthu wamba,
    ndipo iwo amene akulira amawayika pa malo otetezedwa.
12 Iyeyo amalepheretsa chiwembu cha anthu ochenjera,
    kotero kuti cholinga chawo sichipindula kanthu.
13 Iye amakola anthu ochenjera mu msampha wa kuchenjera kwawo,
    ndipo zolinga za atambwali amazithetsa msangamsanga.
14 Mdima umawagwera nthawi yamasana;
    nthawi yamasana amayenda moyambasayambasa monga nthawi ya usiku.
15 Mulungu amapulumutsa amphawi ku lupanga la mʼkamwa mwawo;
    amawapulumutsa mʼmanja mwa anthu amphamvu.
16 Choncho osauka ali ndi chiyembekezo,
    ndipo anthu opanda chilungamo amawatseka pakamwa.

17 “Wodala munthu amene Mulungu amamudzudzula;
    nʼchifukwa chake usanyoze chilango cha Wamphamvuzonse.
18 Pakuti Iye amavulaza koma amamanganso mabalawo;
    Iye amakantha munthu, komanso manja ake amachiritsa.
19 Pakuti adzakupulumutsa ku masautso nthawi ndi nthawi,
    mavuto angachuluke bwanji, sadzakukhudza ndi pangʼono pomwe.
20 Pa nthawi ya njala adzakulanditsa ku imfa,
    ndipo nthawi ya nkhondo adzakupulumutsa ku lupanga.
21 Adzakuteteza kwa anthu osinjirira,
    ndipo palibe chifukwa chochitira mantha pamene chiwonongeko chafika.
22 Uzidzaseka pa nthawi ya chiwonongeko ndi ya njala,
    ndipo palibe chifukwa chochitira mantha ndi zirombo za mʼdziko lapansi.
23 Pakuti udzachita pangano ndi miyala ya mʼmunda mwako,
    ndipo nyama zakuthengo zidzakhala nawe mwamtendere.
24 Udzadziwa kuti nyumba yako ndi malo otetezedwa;
    udzawerengera katundu wako ndipo sudzapeza kanthu kamene kasowapo.
25 Udzadziwa kuti ana ako adzakhala ambiri,
    ndipo zidzukulu zako zidzakhala ngati udzu wa mʼdziko lapansi.
26 Udzafika ku manda utakalamba,
    monga mitolo ya zokolola pa nyengo yake.

27 “Ife tafufuza zimenezi ndipo ndi zoona,
    choncho uzimvere ndi kuzitsata.”

1 Petro 3:8-18

Kumva Zowawa Chifukwa cha Chilungamo

Potsiriza, nonse khalani a mtima umodzi, omverana chisoni. Kondanani monga abale, muchitirane chifundo ndi kudzichepetsa. Wina akakuchitirani choyipa musabwezere pochitanso choyipa, kapena kubwezera chipongwe akakuchitirani chipongwe, koma muwadalitse. Munayitanidwa kuti mulandire mdalitso. 10 Pakuti,

“Iye amene angakonde moyo
    ndi kuona masiku abwino,
aletse lilime lake kuyankhula zoyipa,
    ndiponso milomo yake kunena mabodza.
11 Apewe zoyipa, ndipo azichita zabwino.
    Afunefune mtendere ndi kuyesetsa kuwupeza.
12 Pakuti Ambuye amayangʼanira bwino anthu olungama
    ndipo amatchera khutu ku mapemphero awo.
Koma Ambuye sawayangʼana bwino amene amachita zoyipa.”

13 Ndani angakuchitireni zoyipa ngati muchita changu kuchita zabwino? 14 Koma ngakhale mumve zowawa chifukwa cha chilungamo, ndinu odala. “Musaope anthu, musachite mantha.” 15 Koma lemekezani Khristu mʼmitima mwanu ngati Ambuye wanu. Khalani okonzeka nthawi zonse kuyankha aliyense amene akufunsani za chiyembekezo chimene muli nacho. 16 Koma chitani zimenezi mofatsa ndi mwaulemu, mukhale ndi chikumbumtima chosakutsutsani, kuti anthu ena akanena zoyipa za makhalidwe anu abwino mwa Khristu, achite okha manyazi ndi chipongwe chawocho. 17 Nʼkwabwino ngati ndi chifuniro cha Mulungu kumva zowawa chifukwa chochita zabwino kusiyana ndi kumva zowawa chifukwa chochita zoyipa. 18 Pakuti Khristu anafa chifukwa cha machimo kamodzi kokha kufera onse, wolungama kufera osalungama, kuti akufikitseni kwa Mulungu. Anaphedwa ku thupi koma anapatsidwa moyo mu mzimu.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.